Afi. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kudzichepetsa kwa Khristu, ndi kukwezedwa kwake

1Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni.

2Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.

3Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo.

4Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.

5Motero nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu:

6Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire,

komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu

ndi chinthu choti achigwiritsitse.

7Koma adadzitsitsa kotheratu

pakudzitengera umphaŵi wa kapolo,

ndi kukhala munthu wonga anthu onse.

8Ali munthu choncho adadzichepetsa,

adakhala womvera mpaka imfa,

imfa yake yapamtanda.

9Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana,

nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse.

10 Yes. 45.23 Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu,

zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko,

zidzagwade pansi mopembedza,

11Zonse zidzavomereze poyera kuti,

“Yesu Khristu ndi Ambuye,”

ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.

Akhristu akhale ngati nyenyezi zounikira dziko lapansi

12Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera.

13Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.

14Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,

15Deut. 32.5kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,

16pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe.

17Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu.

18Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi.

Za Timoteo ndi Epafrodito

19Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko.

20Ndilibenso wina wonga amene ali ndi mtima wosamala za inu kwenikweni.

21Paja ena onse amangofuna zokomera iwo okha, osati zokomera Yesu Khristu.

22Koma mukudziŵa kuti mkhalidwe wa Timoteo ndi wotsimikizika kale kuti ngwabwino. Mukudziŵanso kuti adagwira mogwirizana nane ntchito yofalitsa Uthenga Wabwino, monga mwana ndi bambo wake.

23Ndikuyembekeza tsono kumtumiza kwa inu msanga, nditadziŵa za m'mene ziyendere zanga.

24Koma ndikhulupirira kuti, Ambuye akalola, inenso ndidzafika kwanuko msanga.

25Ndaganiza kuti nkofunikadi kuti ndikutumizireni mbale wathu uja, Epafrodito. Mudaamtuma kuti adzandithandize pa zosoŵa zanga, ndipo wagwiradi ntchito ndi kumenya nkhondo yachikhristu pamodzi ndi ine.

26Tsonotu akukulakalakani nonsenu, ndipo ndi wokhumudwa podziŵa kuti inu mudamva zoti iye ankadwala.

27Nzoonadi adaadwala zedi mpaka pafupi kufa. Mwai kuti Mulungu adamchitira chifundo. Ndipotu sadangochitira chifundo iye yekhayu, komanso ineyo, kuti chisoni changa chisakhale chosanjikizana.

28Nchifukwa chake ndikufunitsitsa ndithu kumtumiza kwa inu, kuti podzamuwonanso mudzasangalale, kutinso nkhaŵa yanga ichepeko.

29Mlandireni mwachikhristu ndi chimwemwe chachikulu. Anthu otere muziŵachitira ulemu.

30Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help