1Pambuyo pake ndidaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera Kumwamba. Adaavala mtambo, ndipo pozungulira mutu wake panali utawaleza. Nkhope yake inali ngati dzuŵa, miyendo yake ngati mizati yamoto.
2M'manja mwake anali ndi kampukutu kofutukula. Ndi mwendo wa ku dzanja lamanja adaaponda pa nyanja, ndi wakumanzere adaaponda pa mtunda.
3Tsono adaafuula mokweza ngati kubangula kwa mkango. Mngeloyo atangofuula choncho, mabingu asanu ndi aŵiri aja adagunda.
4Mabinguwo atangogunda, ndidaati ndilembe. Koma ndidamva mau ochokera Kumwamba akuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi aŵiri aja anena. Usazilembe.”
5 Eks. 20.11; Deut. 32.40; Dan. 12.7; Amo. 3.7 Pamenepo mngelo amene ndidaaona ataponda pa nyanja ndi pa mtunda uja, adakweza dzanja lake lamanja kumwamba.
6Atatero adalumbira m'dzina la Mulungu wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene adalenga thambo lakumwamba ndi zonse zokhala kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo, ndiponso nyanja ndi zonse zokhala m'menemo. Mngeloyo kulumbira kwake adati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano.
7Pamene mngelo wachisanu ndi chiŵiri adzaliza lipenga lake, zachinsinsi zimene Mulungu adakonzeratu zidzachitika, monga momwe Iye adaalonjezera kwa atumiki ake aja, aneneri.”
8 Ezek. 2.8—3.3 Pamenepo mau amene ndidaamva kuchokera Kumwamba adandilankhulanso, adati, “Pita, katenge kampukutu kofutukula kaja kamene kali m'manja mwa mngelo woponda pa nyanja ndi pa mtunda uja.”
9Ndidapitadi kwa mngeloyo nkumupempha kuti andipatse kampukutuko. Iye adati, “Kwaya, idya. M'mimba mwako kaziŵaŵa, koma m'kamwa mwako kazizuna ngati uchi.”
10Ndidalandira kampukutuko m'manja mwa mngelo uja, ndipo ndidadyadi. M'kamwamu kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, m'mimbamu munkaŵaŵa.
11Pamenepo adandiwuza kuti, “Uyenera kulengezanso za mitundu yambiri ya anthu, za zilankhulo zosiyanasiyana, ndi za mafumu ambiri.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.