1Tsopano Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse,
ali pafupi kulanda Yerusalemu ndi Yuda
chithandizo cha mtundu uliwonse
chimene anthu amadalira.
Adzachotsa chakudya chonse,
adzachotsa madzi onse,
2anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo,
aweruzi ndi aneneri,
olosa ndi akuluakulu,
3atsogoleri ankhondo ndi anthu olemekezeka,
aphungu ndi amatsenga,
ndiponso akatswiri a njirisi.
4Adzaŵaikira anyamata kuti akhale mafumu ao,
ndipo ana amakanda ndiwo adzaŵalamulira.
5Anthu adzazunzana,
aliyense adzazunza mnzake.
Anyamata adzachita chipongwe akuluakulu,
ndipo anthu achabechabe adzanyoza olemekezeka.
6Munthu adzagwira mbale wake
m'nyumba ya atate ao,
nkunena kuti,
“Iwe uli nawo mwinjiro,
ndiye ukhale mtsogoleri wathu
nthaŵi yamavutoyi.”
7Tsiku limenelo mbale wakeyo adzayankha kuti,
“Ine ai toto! Mavuto otereŵa
ndilibe mankhwala ake,
m'nyumba mwanga momwe ndilibe chakudya kapena chovala.
Musaike ine kuti ndikhale
mtsogoleri wa anthu.”
8Zoonadi Yerusalemu akusakazika ndipo Yuda akugwa,
chifukwa zokamba ndiponso ntchito
za anthu am'menemo nzonyoza Chauta.
Salabadako za ulemerero wa Mulungu.
9Maonekedwe a nkhope zao amaŵatsutsa.
Amachimwa poyera ngati m'mene ankachitira
anthu a mu Sodomu, sabisa konse.
Tsoka kwa iwowo, achita kudziputira okha mavuto.
10Ngodala anthu omvera Mulungu
pakuti zinthu zidzaŵayendera bwino,
adzakondwera ndi phindu la ntchito zao.
11Koma tsoka kwa anthu oipa!
Zinthu zidzaŵaipira.
Zimene akhala akuchitira anzao
zomwezo zidzaŵabwerera.
12Inu anthu anga,
amene akukuponderezani ndi ana chabe,
ndipo amene akukulamulani ndi akazi.
Aah! Anthu anga,
atsogoleri anu akukusokeretsani,
akukusokonezerani njira zanu.
Chauta aweruza anthu ake13Tsopano Chauta afuna kuyambapo mlandu,
wakonzeka kale kuweruza anthu ake.
14Chauta akuŵaimba mlandu
akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake.
Akuŵazenga kuti,
“Ndinu amene mwaononga munda wanga wamphesa.
Nyumba zanu zadzaza ndi zinthu zolanda kwa amphaŵi.
15Mukuŵapsinjiranji anthu anga?
Chifukwa chiyani mukuŵadyera masuku pamutu amphaŵi?”
Akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
Achenjeza akazi a ku Ziyoni16Chauta adati,
“Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri:
amayenda makosi ali wee,
amayang'ana ndi maso ophika.
Amayenda nyang'anyang'a
ndi kuliza zigwinjiri zam'miyendo.
17Nchifukwa chake Ambuye adzatulutsa
zipere kumutu kwa akazi a ku Ziyoniwo,
tsitsi lao lonse lidzatha phu!”
18Tsiku limenelo Ambuye adzaŵachotsera zokongoletsera m'miyendo, kumutu ndi m'khosi,
19maukufu, makoza, ndi nsalu zakumaso,
20maduku, zigwinjiri, malamba, mabotolo a zonunkhira, zithumwa,
21mphete, zipini,
22madelesi apaphwando, makepi, miinjiro, zikwama,
23akalilole, zovala zabafuta, nduŵira, ndiponso nsalu zam'mapewa.
24M'malo mwa kununkhira padzakhala kununkha,
m'malo mwa lamba adzavala chingwe,
m'malo mwa tsitsi lopesa bwino
adzakhala ndi mipala,
m'malo mwa delesi la mtengo wapatali
adzavala chiguduli,
m'malo mwa kunyadira kukongola
adzachita manyazi.
25Iwe Yerusalemu, anthu ako aamuna
adzaphedwa ndi lupanga,
ndipo anthu ako amphamvu adzafera ku nkhondo.
26Choncho pa zipata zako
padzakhala kulira kokhakokha,
iweyo udzasakazidwa nkukhala pansi,
ukuvimvinizika pa fumbi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.