1Mose adauza atsogoleri a mafuko a Aisraele kuti, Chauta walamula kuti,
2Deut. 23.21-23; Mt. 5.33 “Pamene munthu wamwamuna alumbira kwa Chauta kapena alonjeza kuti adzachitadi zimene walumbira, asaphwanye lonjezo lakelo. Achite molingana ndi zimene adalumbira.
3Mkazi akakhala mtsikana, nakhalabe m'nyumba ya bambo wake, ndipo alumbira kwa Chauta kuti adzachitadi zina zake zimene walumbira,
4tsono bambo wake nkumva za kulumbira kwakeko ndi za malonjezo amene walumbira kuti adzachitadi, koma bambo wakeyo osalankhula kanthu, mwanayo achitedi zimene adalumbirazo. Ayenera kuchitadi zonse zimene walonjezazo.
5Koma bambo wake akamkaniza mwanayo pa tsiku lomwe wamva zimenezo, palibe lamulo lomkakamiza mwanayo kuti achite zimene adalumbirazo ndi zimene adalonjezazo. Chauta adzamkhululukira mwanayo chifukwa choti bambo wake adamkaniza.
6Ngati mkazi alonjeza kapena alumbira mosaganiza bwino kuti adzachitadi kanthu kena, ndipo pambuyo pake akwatiwa,
7tsono mwamuna wake nkumva, koma osamuuza kanthu mkaziyo pa tsiku lomwe wamvalo, mkaziyo achitedi zimene walumbirazo, achite ndithu zimene walonjezazo.
8Koma ngati pa tsiku limene mwamunayo wamva zimenezo, amkaniza, pamenepo ammasula mkaziyo kwa zimene adalumbira ndi kwa zimene adalankhula mosaganiza bwino, ndipo Chauta adzamkhululukira.
9“Mkazi wamasiye kapena wosudzulidwa akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi.
10“Mkazi wokwatiwa akalonjeza nalumbira kuti adzachitadi zimene walonjeza,
11tsono mwamuna wake nkumva, koma osamuuza kanthu mkaziyo ndiponso osamkaniza, ayenera kuchitadi zonse zimene adalumbira ndi zonse zimene adalonjeza.
12Koma pa tsiku limene mwamuna wake wamva zimenezo, akamletsa mkaziyo kuti asachite zimene adalumbirazo, palibe lamulo lomkakamiza mkaziyo kuchita zimene adalumbira kapenanso zimene adalonjeza. Mwamuna wake waletsa, ndipo Chauta adzamkhululukira mkaziyo.
13Mwamuna wake ali ndi mphamvu za kuvomereza kapena kukana zimene mkaziyo adalumbira kapena zimene adalonjeza zokhudza za kudzilanga.
14Koma ngati m'maŵa mwake ndi masiku otsatirawo mwamuna wake samkaniza, atamva zimenezo, mkaziyo achitedi zonse zimene adalumbira, kapena zimene adalonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa choti sadamuuze kanthu mkaziyo pa tsiku limene adamva.
15Koma mwamunayo akamkaniza patapita kanthaŵi atazimva kale, iyeyo ndiye wochimwa pamalo pa mkaziyo.”
16Ameneŵa ndiwo malamulo amene Chauta adalamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso za bambo ndi mwana wake wamkazi amene akadali mtsikana wokhalabe m'nyumba ya bambo wake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.