1Wina pokonzekera kuwoloka nyanja yaukali,
amapemphera mtengo umene uli wofooka
kupambana chombo chomwe chamunyamula.
2Chombo adachiganiza ndi munthu wofuna phindu,
mmisiri wanzeru, nkuchipanga ndi luso.
3Koma inu Atate, ndi chisamaliro chanu
chimene chimayendetsa chombocho,
poti ndinu amene mudachipatsa njira pakati pa nyanja
ndiponso khwalala labwino pakati pa mafunde.
4Choncho mudatiwonetsa kuti
mungathe kutipulumutsa m'mavuto aliwonse,
kotero kuti ngakhale munthu wopanda luso lake
angathe kuyenda pa nyanja.
5Simufuna kuti ntchito za nzeru zanu
zikhale zopanda phindu.
Choncho anthu saopa imfa
ngakhale atakwera m'kabwato kofooka,
amapita pa mafunde atakwera m'kabwato,
mpaka kukafika ku mtunda.
6Pajatu ngakhale pachiyambi paja
pamene ziphona zonyada zinkatayika,
chikhulupiriro cha dziko lonse chidathaŵira m'chombo.
Ndipo mutayendetsa chombocho ndi dzanja lanu,
mudalisiyira dziko lapansi
mbeu ya anthu a mbadwo watsopano.
7Zoonadi, ndi wotamandika mtengo
wodzetsa chilungamo.
8Koma litembereredwe fano
lopangidwa ndi manja a munthu,
pamodzi ndi mmisiri wake yemwe,
poti ndiye adalipanga ndi kutchula mulungu
chinthu chimene chimaola.
9Mulungu amadana ndi anthu osamvera,
amaipidwa nako kusamvera kwao.
10Pajatu chinthu chimene chidapangidwacho
chidzalangidwira kumodzi ndi wochipanga.
11Nchifukwa chake mafano a mafuko ena
nawonso Mulungu adzaŵaononga,
pakuti ngakhale adapangidwa
ndi chinthu cholengedwa ndi Mulungu,
amalakwitsa mitima ya anthu,
ndiponso amakhala misampha yokola anthu opusa.
Chiyambi cha kupembedza mafano12Ganizo lopanga mafano
ndiye chinali chiyambi cha dama limenelo.
Moyo wa anthu udaonongeka
chifukwa chakuyamba kupanga zoterezi.
13Pa chiyambi kunalibe mafano,
ndipo sikuti adzakhalapo mpaka muyaya.
14Mafano adabwera pansi pano
ndi anthu okhulupirira zachabe,
nchifukwa chake Mulungu adaŵakonzera
zoti aonongeke msanga.
15Bambo wina akuvutika ndi maliro a mwana wake,
adapanga chithunzi cha mwanayo
amene Mulungu adamtenga mwadzidzidzi.
Chimene dzuloli chinali mtembo chabe,
adayamba kuchipembedza ngati mulungu,
ndipo adasiyira a m'nyumba mwake
miyambo yachinsinsi,
yachipembedzo ndi yachinamwali.
16Tsono ndi nthaŵi mazoloŵero oipawo adalimbika,
nasanduka ngati lamulo,
ndipo mafumu adalamula
kuti anthu azipembedza zithunzi zosemasema.
17Amene sankatha kulemekeza mafumu pamaso pao,
chifukwa choti anali kutali,
ankayesetsa kukumbukira nkhope yao.
Ndipo ankapanga chithunzi chofanafana ndi mfumu
imene ankafuna kuilemekezayo.
Choncho munthu amene ankakhala naye kutali,
ankamlambira monga ngati ali naye pafupi.
18Kudzikuza kwa mmisiri kudakakamiza
anthu osaidziŵa mfumuyo
kuti afalitse chipembedzo chake.
19Iyeyo pofuna kukomera mfumuyo,
adayesetsa ndithu kukometsa chithunzicho.
20Tsono anthu ambirimbiri
atakopeka ndi luso la ntchito yake,
adayamba kuipembedza ngati mulungu
mfumu yomwe poyamba
ankangoilemekeza ngati munthu.
21Zimenezi anthu adakodwa nazo mu msampha,
pakuti chifukwa cha matsoka
kapena malamulo a mfumu,
anthuwo ankatcha mwala kapena mtengo
dzina lopatulika.
Zotsatira za kupembedza mafano22Pambuyo pake sikudakwanire kuti iwowo asokere
posadziŵa zoona za Mulungu,
koma ankakhalanso pa nkhondo yoopsa
chifukwa cha kusadziŵako,
ndipo tsoka lotere ankalitcha mtendere.
23Chifukwa cha kupereka ana ao ku nsembe,
kapena kuchita miyambo yachinsinsi ija,
kapena kulola madyerero
pamodzi ndi zokondweretsa zonyansa,
24sankathanso kusunga ungwiro
pa moyo wao ndi pa maukwati ao.
Mwina munthu ankapha mnzake monyenga,
mwina kumuvuta pochita chigololo ndi mkazi wake.
25Ponseponse panali chisokonezo:
magazi, kupha anthu,
mabodza ndi kuchenjerera ena,
kuipiratu, kusakhulupirirana,
phokoso ndi kulumbira zonama.
26Ankasokoneza anthu abwino,
sankathokoza polandira zabwino,
ankaipitsa mitima, ankachita zadama zamtundu,
ndipo pa chikwati ankachita zosayenera,
chigololo ndi zonyansa zina.
27Chipembedzo cha mafano osatchulika,
ndiye chiyambi cha zoipa zonse,
gwero lake ndi mathero ake.
28Anthu oŵapembedza mafanowo
amasangalala kopengetsa,
mwina amalosa zabodza.
Mwina amachita zosalungama
mwina amaphwanya msanga malonjezo olumbira.
29Popeza kuti amakhulupirira mafano opanda moyo,
saopa kuti nkupeza mavuto
chifukwa cha malumbiro ao onama.
30Koma chilango chidzaŵagwera
chifukwa cha zinthu ziŵiri:
Chifukwa adalakwira Mulungu kwakukulu
potsata mafano,
ndiponso chifukwa adachita monyenga
malumbiro oipa, kunyoza chilungamo.
31Chimene chimalondola tchimo la munthu wosalungama
si mphamvu za zinthu zimene amazitchula polumbira,
koma ndi chilango choyenera
chimene chimagwera anthu ochimwawo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.