Tit. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndine, Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Adandituma kuti amene Mulungu adaŵasankha, ndiŵatsogolere ku chikhulupiriro, azizindikira choona chimene chimaŵafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu,

2ndi kuŵapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. Mulungu amene sanama, adalonjeza moyo wosathawu nthaŵi isanayambe.

3Pa nthaŵi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu, adaululadi mau ake, ndipo adalamula kuti ine ndipatsidwe udindo wolalika uthengawu.

4 2Ako. 8.23; Aga. 2.3; 2Tim. 4.10 Ndikulembera iwe Tito, mwana wanga weniweni chifukwa choti ineyo ndi iwe tili m'chikhulupiriro chimodzimodzi.

Mulungu Atate ndi Khristu Yesu, Mpulumutsi wathu, akukomere mtima ndi kukupatsa mtendere.

Za ntchito ya Tito ku Krete

5Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira.

61Tim. 3.2-7Mkulu wa mpingo akhale munthu wosapalamula konse, ndipo akhale wa mkazi mmodzi yekha. Ana ake akhalenso okhulupirira Khristu, opanda mbiri yoti ngosakaza kapena yoti ngosaweruzika.

7Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama.

8Akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziŵa kudzilamula, wolungama, woyera mtima, ndiponso wodzigwira.

9Asunge mogwiritsa mau okhulupirika, amene ali ogwirizana ndi zimene tidaphunzitsidwa. Pakutero adzatha kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona, ndiponso kugonjetsa otsutsana nacho.

10Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka pakati pa gulu la anthu ochokera ku Chiyuda. Anthu ameneŵa amalankhula nkhani zopanda pake nkumasokeretsa anzao.

11Nkofunika kuŵakhalitsa chete, chifukwa akusokoneza mabanja ena athunthu pakuŵaphunzitsa zimene sayenera kuŵaphunzitsa. Amangochita zimenezi ndi cholinga choipa, chofuna kupata ndalama.

12Mneneri wina wa ku Krete, mmodzi mwa iwo omwewo, adati, “Akrete nthaŵi zonse ndi amabodza, zilombo zoipa, alesi adyera.”

13Mau ameneŵa ngotsimikizika. Nchifukwa chake uŵadzudzule kwamphamvu anthuwo, kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba,

14m'malo momasamala nthano zachiyuda, ndi malamulo a anthu okana choona.

15Kwa anthu oyera mtima, zinthu zonse nzoyera. Koma kwa amene ali odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera; mitima yao ndi nzeru zao zomwe, zonse nzodetsedwa.

16Amatsimikiza kuti amadziŵa Mulungu, pamene ndi zochita zao amamkana, pakuti ndi anthu onyansa osamvera, ndi osayenera kuchita kanthu kalikonse kabwino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help