Yak. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mt. 13.55; Mk. 6.3; Ntc. 15.13; Aga. 1.19 Ndine, Yakobe, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu.

Ndikupereka moni kwa inu anthu a Mulungu, a mafuko khumi ndi aŵiri, obalalikana ku maiko osiyanasiyana.

Za chikhulupiriro ndi nzeru

2 Lun. 3.5, 6 Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu.

3Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika.

4Koma kulimbika kumeneku kuzigwira ntchito yake kotheratu, kuti mukhale angwiro, opanda chilema ndi osapereŵera pa kanthu kalikonse.

5Lun. 8.20; Mphu. 51.13, 14Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

6Koma wopemphayo apemphe mokhulupirira, ndi mosakayika konse. Paja munthu wokayikakayika ali ngati mafunde apanyanja, amene amavunduka ndi kuŵinduka ndi mphepo.

7Munthu wotere asamaganiza kuti nkudzalandira kanthu kwa Ambuye ai;

8pakuti iyeyo ndi wa mitima iŵiri, ndi wosakhazikika pa zochita zake zonse.

Za umphaŵi ndi chuma

9Mbale woluluka anyadire pamene Mulungu amkweza.

10Yes. 40.6, 7Ndipo mbale wolemera nayenso anyadire pamene Mulungu amtsitsa, pakuti adzatha ngati duŵa la udzu.

11Dzuŵa limatuluka nkutentha kwake, ndipo limaumitsa udzu. Duŵa la udzuwo limathothoka, kukongola kwake nkutha. Chomwechonso moyo wa wolemerayo udzazimirira ali pakati pa zochita zake.

Za kuyesedwa

12Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.

13Mphu. 15.11-20Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo.

14Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola.

15Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.

16Musamanyengedwa, abale anga okondedwa.

17Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.

18Mwa kufuna kwake mwiniwakeyo, adatipatsa moyo kudzera mwa mau ake oona, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, ife tikhale ngati zipatso zoyamba zimene Iye wadzipatulira.

Za kumva ndi kuchita zimene mau a Mulungu anena

19 Mphu. 5.11 Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.

20Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

21Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.

22Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena.

23Paja munthu amene amangomva chabe mau, osachita zimene wamvazo, ali ngati munthu woyang'anira nkhope yake yachibadwa m'galasi.

24Tsono amati akadzipenya, amachokapo, posachedwa nkuiŵalako m'mene akuwonekera.

25Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse.

26Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga.

27Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help