2 Ate. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ntc. 17.1 Ndife, Paulo, Silivano ndi Timoteo. Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli wake wa Mulungu Atate, ndiponso wa Ambuye Yesu Khristu.

2Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.

Za chiweruzo, Khristu akadzabwera

3Tiyenera kuthokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale. Nkoyeneradi kutero, chifukwa chikhulupiriro chanu chikunka chikukulirakulira kwambiri pamodzi ndi kukondana kwanu pakati pa inu nonse.

4Nchifukwa chake ife timakunyadirani, m'mipingo yonse ya Mulungu, chifukwa cha kulimbika kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso ndi mazunzo onse amene adakugwerani.

5Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Cholinga chake nchakuti inu mupezeke oyenera kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu umene mukuusaukira tsopano.

6Paja Mulungu mwa chilungamo chake, adzaŵalanga ndi masautso anthu amene amakusautsani inu.

7Koma inu amene mukusauka tsopano, adzakupatsani mpumulo pamodzi ndi ife tomwe. Adzachita zimenezi, Ambuye Yesu akadzabwera kuchokera Kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu.

8Adzabwera ndi moto woyaka, nadzalanga anthu amene sadziŵa Mulungu, ndi amene sadamvere Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu.

9Yes. 2.10Chilango chao nchakuti adzaonongedwa kwamuyaya, sadzaona konse nkhope ya Ambuye kapena ulemerero wa mphamvu zake,

10pa tsiku limene Iye adzabwera kuti alemekezedwe mwa oyera, ndipo alandire ulemu mwa onse omkhulupirira. Ndipotu inunso mudzakhala nawo, chifukwa mudakhulupirira umboni wathu.

11Nchifukwa chake timakupemphererani nthaŵi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera moyo umene Iye adakuitanirani. Timapemphanso kuti ndi mphamvu zake akulimbikitseni kuchita zabwino zonse zimene mumalakalaka kuzichita, ndiponso ntchito zotsimikizira chikhulupiriro chanu.

12Motero dzina la Ambuye athu Yesu lidzalemekezedwa mwa inu, ndipo inu mudzalemekezedwa mwa Iye. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu wathu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help