1Inu Mulungu, pulumutseni.
Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza.
2Anthu ofunafuna moyo wanga,
muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza.
Amene akhumba kundipweteka,
abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa.
3Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,”
achoke ndi manyazi poona kuti alephera.
4Koma onse okufunafunani
akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu.
Onse okondwerera chipulumutso chanu,
azinena kosalekeza kuti,
“Chauta ndi wamkulu.”
5Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa,
bwerani msanga kwa ine, Inu Mulungu.
Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga.
Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.