1Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.
2Zophunzitsa zimenezi nzochokera ku chinyengo cha anthu onama, amene mumtima mwao adalembedwa chizindikiro ndi chitsulo chamoto.
3Iwo amaletsa anthu ukwati, nkumaŵalamula kusala zakudya zina. Koma tsono zakudyazo Mulungu adazilenga kuti amene ali okhulupirira ndi odziŵa choona, azidye moyamika Mulungu.
4Pajatu chilichonse chimene Mulungu adalenga nchabwino, palibe chilichonse choti munthu asale, akamachilandira moyamika Mulungu,
5pakuti chimayeretsedwa ndi mau a Mulungu ndi mapemphero aja.
Za mtumiki wabwino wa Khristu Yesu6Ngati abale uŵalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa ndi mau a chikhulupiriro ndi a chiphunzitso choona chimene wakhala ukutsata.
7Koma upewe nthano zachabe, monga zimene akazi okalamba amakonda kukamba. Udzizoloŵeze kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu.
8Kuzoloŵeza thupi kumapindulitsapo pang'ono, koma moyo wolemekeza Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo wakutsogolo.
9Ameneŵa ndi mau otsimikizika oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse.
10Nchifukwa chake timagwira ntchito kolimba, ndipo timayesetsa kupambana, pakuti chiyembekezo chathu chili pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka okhulupirira Khristu.
11Uzilamula ndi kuphunzitsa zimenezi.
12Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
13Mpaka pamene ndidzabwere, uchite khama kuŵerengera anthu mau a Mulungu, kuŵalalikira ndi kuŵaphunzitsa.
14Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja.
15Ntchito zimenezi uzizichita mosamala ndi modzipereka, kuti anthu onse aone kuti moyo wako wautumiki ukukulirakulira.
16Udziyang'anire bwino wekha, ndi kusamala zimene umaphunzitsa. Ulimbikire kutero, chifukwa pakuchita zimenezi udzadzipulumutsa iwe wemwe, ndiponso anthu amene amamva mau ako.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.