2 Mbi. 28 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ahazi mfumu yoipa ya ku Yuda(2 Maf. 16.1-4)

1Ahazi anali wa zaka 20 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Iyeyo sadachite zolungama pamaso pa Chauta, monga m'mene ankachitira Davide kholo lake.

2Koma adatsata zitsanzo za mafumu a ku Israele. Adapanga zifanizo zosungunula za Abaala.

3Adafukiza lubani ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza, potsata miyambo yonyansa ya anthu a mitundu ina imene Chauta adaaipirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraele.

4Ndipo adapereka nsembe, namafukiza lubani ku akachisi opembedzerako mafano, pa mapiri ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.

Nkhondo pakati pa Israele ndi Siriya(2 Maf. 16.5)

5 2Maf. 16.5; Yes. 7.1 Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wake, adapereka Ahazi kwa mfumu ya ku Siriya, imene idamgonjetsa. Ndipo anthu ambiri adatengedwa ukapolo kupita ku Damasiko. Chauta adamperekanso Ahaziyo kwa mfumu ya ku Israele, imene idamgonjetsa kotheratu pakupha anthu ambiri.

6Peka mwana wa Remaliya adaphako anthu okwanira 120,000 a ku Yuda pa tsiku limodzi, chifukwa iwowo adaasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao. Onsewo anali anthu olimba mtima.

7Ndipo Zikiri, munthu wamphamvu wa ku Efuremu, adapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu, nduna ya ku nyumba ya mfumu, ndiponso Elikana, wachiŵiri mu ulamuliro wa mfumu.

8Anthu a ku Israele adagwira ukapolo abale ao a ku Yuda okwanira 200,000, akazi, ana aamuna, ndi ana aakazi. A ku Israelewo adatenganso zofunkha zambiri kubwera nazo ku Samariya.

Za mneneri Odedi

9Koma kumeneko kunali mneneri wina wa Chauta dzina lake Odedi. Iye adapita kuti akakumane ndi gulu lankhondo limene lidadza ku Samariya. Adauza anthuwo kuti, “Popeza kuti Chauta, Mulungu wa makolo anu, adaakwiyira anthu a ku Yuda, adapereka Ayudawo kwa inu. Koma inu mwaŵapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba.

10Tsono mukufuna kuti mupondereze anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, amuna ndi akazi omwe, kuti akhale akapolo anu. Kodi inuyo mulibe anu machimo pamaso pa Chauta, Mulungu wanu?

11Mverani tsono, ndipo muŵabweze akapolo amene mudaŵatenga pakati pa abale anuwo, kuti apite kwao, poti Chauta wakwiya nanu koopsa.”

12Atsogoleri enanso a anthu a ku Efuremu, monga Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, adaimirira kuti amenyane ndi anthu amene ankachoka ku nkhondo.

13Adaŵauza kuti, “Musati mubwere nawo kuno akapolowo, poti inuyo mukufuna kuti ife tichimwire Chauta kuwonjezera pa machimo athu amene tili nawo, ndiponso kuwonjezera pa zolakwa zathu. Ndithu kulakwa kwathu nkwakukulu ndipo mkwiyo woopsa uli pa Israele.”

14Motero anthu ankhondo aja adaŵasiya akapolowo, pamodzi ndi zofunkhazo, pamaso pa atsogoleriwo ndi pamaso pa msonkhano wonse.

15Kenaka anthu amene taŵatchula maina aja, adanyamuka natenga akapolowo. Amene anali maliseche adaŵaveka zovala zimene adaafunkha. Adaŵaveka, naŵapatsa nsapato. Adaŵapatsa zakudya ndi zakumwa. Tsono atanyamula anthu onse ofooka pa abulu, adabwera nawo kwa abale ao ku Yeriko, mzinda wamigwalangwa. Kenaka adabwerera ku Samariya.

Ahazi apempha chithandizo ku Asiriya(2 Maf. 16.7-9)

16Pa nthaŵi imeneyo Mfumu Ahazi adatumiza mau kwa mfumu ya ku Asiriya, kupempha chithandizo.

17Paja Aedomu anali atathiranso nkhondo ku Yuda, ndipo adaagonjetsa Yudayo, natenga anthu kuti akhale akapolo.

18Afilisti nawonso anali atathira nkhondo mizinda yakuchigwa ndiponso Megebu wa ku Yuda. Ndipo adalanda Betesemesi, Aiyaloni, Gederoti ndiponso Soko pamodzi ndi midzi yake yomwe, Timna pamodzi ndi midzi yake yomwe, ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yake yomwe, nakhazikika komweko.

19Zoonadi Chauta adalitsitsa dziko la Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi, popeza kuti adaaipitsa ku Yuda, ndipo anali wosakhulupirika kwa Chauta.

20Motero Tiligati-Pilinesere, mfumu ya ku Asiriya, adadzamenyana naye nkhondo, ndipo adamvutitsa m'malo momlimbikitsa.

21Ahazi ankatenga katundu ku Nyumba ya Chauta, ku nyumba ya mfumu ndi ku nyumba za nduna, namakampereka kuti akakhomere msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya. Koma zonsezo sizidamthandize.

22Pa nthaŵi yake yamavutoyo, Ahazi adapitirirabe kukhala wosakhulupirika kwa Chauta.

23Ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko imene idamgonjetsayo, ndipo ankati, “Chifukwa chakuti milungu ya mafumu a ku Siriya yaŵathandiza iwowo, ine ndidzapereka nsembe kwa milunguyo kuti indithandizenso ine.” Koma milunguyo idamuwononga pamodzi ndi anthu ake onse.

24Tsono Ahazi adasonkhanitsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta, naziphwanyaphwanya. Kenaka adatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, nadzimangira maguwa pa malo ambirimbiri mu Yerusalemu.

25Adamanga akachisi opembedzerako ku mzinda uliwonse wa Yuda, kuti azifukizako lubani kwa milungu ina, kuputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa makolo ake.

26Tsono ntchito zonse ndi makhalidwe ake kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Yuda ndi mafumu a ku Israele.

27Yes. 14.28Ahazi adamwalira, naikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sadamuike m'manda enieni a mafumu. Ndipo Hezekiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help