1 Lk. 1.46-55 Hana adapemphera nati,
“Mtima wanga ukukondwa
chifukwa cha zimene Chauta wandichitira,
Ndikuyenda ndi mdidi chifukwa cha Chauta.
Pakamwa panga pakula nkuseka adani anga monyodola.
Ndakondwa kwambiri chifukwa mwandipulumutsa.
2“Palibe woyera wina wofanafana ndi Chauta,
palibe wina koma Iye yekha.
Palibe thanthwe lina lotchinjiriza
lofanafana ndi Mulungu wathu.
3Anthu inu musalankhulenso modzitama,
pakamwa panu pasatuluke zodzikuza.
Pakuti Chauta ndi Mulungu wanzeru,
ndiye amene amaweruza ntchito za anthu.
4Ankhondo amphamvu mauta ao athyoka,
koma anthu ofooka avala dzilimbe.
5Anthu amene kale adaali okhuta, tsopano akusuma,
koma amene kale adaali ndi njala, tsopano akukhuta.
Chumba chabala ana asanu ndi aŵiri,
koma wobereka ana ambiri watsala yekha.
6 Lun. 16.13; Tob. 13.2 Chauta amadzetsa imfa ndipo amabwezeranso moyo,
amatsitsira ku manda, ndipo amaŵatulutsakonso.
7Chauta amasaukitsa ndipo amalemeretsa,
amatsitsa ndipo amakweza.
8Amakweza osauka kuŵachotsa pa fumbi,
amachotsa anthu osoŵa pa dzala,
amaŵakhazika pamodzi ndi akalonga,
amaŵapatsa mpando waulemu.
Nsanamira za dziko lapansi nzake za Chauta,
adakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
9“Anthu okhulupirika Iye adzatchinjiriza moyo wao,
koma anthu oipa adzazimirira mu mdima,
pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake.
10Chauta adzatswanya adani ake,
adzaŵaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba.
Chauta adzaŵaweruza mpaka ku mathero a dziko lapansi.
Koma adzalimbikitsa mfumu yake,
adzakuza mphamvu za wodzozedwa wake.”
11Tsono Elikana adabwerera kwao ku Rama. Koma mnyamata uja Samuele adatsala, ndipo ankatumikira Chauta pamaso pa wansembe Eli.
Kuipa kwa ana a Eli.12Tsono ana a Eli anali achabechabe, sankasamalako za Chauta.
13Sankasamalanso za khalidwe loyenera ansembe pakati pa anthu. Ankachita motere: pamene munthu wina ankapereka nsembe, nyama ilikuŵira pa moto, mtumiki wake wa wansembe ankabwera, atatenga chiforoko cha mano atatu.
14Ankachipisa mu mphika, ndipo zonse zimene chiforoko chija chinkajinya, wansembe ankatenga kuti zikhale zake. Aisraele onse amene ankafika ku Silo, ana a Eli ankaŵachita mokhamokhamo.
15Kuwonjezera apo, mafuta asanatenthedwe, mtumiki wa wansembe ankabwera ndi kuuza munthu wopereka nsembeyo kuti, “Patse nyama yoti ndikaotchere wansembe. Pakuti sadzalandira nyama yophika, koma yosaphika.”
16Ndipo munthuyo akanena kuti, “Apserezeretu mafutaŵa poyamba, pambuyo pake ndiye mutenge monga momwe mufunira,” mtumiki uja ankati, “Iyai, patsiretu tsopano pompano. Ngati sutero, ndichita kukulanda.”
17Motero tchimo la ana a Eli linali lalikulu pamaso pa Chauta, pakuti ankanyoza nsembe za Chauta.
Samuele ku Silo.18Samuele pa unyamata wake ankatumikira pamaso pa Chauta, atavala efodi yabafuta.
19Chaka chilichonse mai wake ankamsokera mkanjo, ndi kukampatsa pamene ankapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe ya chaka ndi chaka.
20Tsono Eli ankadalitsa Elikana ndi mkazi wake, ponena kuti, “Chauta akupatseni ana mwa mkazi ameneyu, chifukwa cha mwana amene iye adampereka kwa Chauta.” Atatero, iwowo ankabwerera kwao.
21Chauta adadalitsadi Hana, ndipo adabala ana aamuna atatu ndi ana aakazi aŵiri. Ndipo mnyamata uja Samuele ankakula akutumikira Chauta.
Eli ndi ana ake.22Tsopano Eli adafika pokalamba kwambiri, ndipo ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachita Aisraele onse, ndiponso zoti anawo ankagona ndi akazi otumikira pa chipata cha chihema chamsonkhano.
23Tsono adafunsa ana akewo kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu zotere? Ndilikumvatu kwa anthu zonse zoipa zimene mukuchita.
24Iyai ana anga, zimene ndilikumva anthu a Chauta akusimba nkumafalitsa, si zabwino ai.
25Munthu akachimwira munthu mnzake, mwina Mulungu adzampepesera munthuyo. Koma akachimwira Chauta, adzampepesera ndani?” Koma anawo sadamvere mau a bambo wao, chifukwa kunali kufuna kwa Chauta kuti anawo aphedwe.
26Mphu. 46.13; Lk. 2.52Monsemo mnyamata uja Samuele ankakulabe mu msinkhu, ndipo ankapeza kuyanja pamaso pa Chauta ndi anthu omwe.
Mneneri alosa za banja la Eli.27Tsiku lina munthu wa Mulungu adafika kwa Eli namuuza kuti, “Chauta akuti, ‘Suja ndidadziwulula kwa banja la kholo lako Aroni pamene anali akapolo a Farao ku Ejipito?
28Eks. 28.1-4; Lev. 7.35, 36 Ndipo ndidamsankha pakati pa mafuko onse a Israele, kuti akhale wansembe wanga, ndipo kuti azipita ku guwa langa lansembe, azifukiza lubani, ndi kumavala efodi pamaso panga. Ndidalipatsa banja la bambo wako gawo la nsembe zanga zonse zopsereza zimene Aisraele amapereka.
29Nanga chifukwa chiyani ukunyoza nsembe zanga ndi zopereka zanga zimene ndidalamula? Kodi ukulemekeza ana ako kupambana Ine, pomadzinenepetsa nonsenu ndi zakudya zokoma kwambiri za pa nsembe zanga zimene anthu anga Aisraele amapereka?
30Paja Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndidaalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la atate ako, azidzanditumikira nthaŵi zonse. Koma tsopano ndikuti zimenezo zithe basi! Ndidzachitira ulemu anthu ondichitira ulemu, koma anthu ondinyoza, Inenso ndidzaŵanyoza.
31Ndithudi, masiku akudza pamene ndidzachotse anyamata onse a m'banja la atate ako, kotero kuti siidzapezekanso nkhalamba pabanja pako.
32Tsono pakati pa mavuto ako, udzayang'ana ndi maso ansanje zabwino zonse zimene ndidzapatsa Aisraele ena. Sipadzapezekadi nkhalamba pabanja pako nthaŵi zonse.
33Komabe pabanja pako ndidzasungapo mmodzi wodzanditumikira pa guwa langa, azidzangokuliritsa ndi kukumvetsa chisoni mumtima mwako. Koma ena onse a banja lako adzaphedwa ku nkhondo akali anyamata abiriŵiri.
341Sam. 4.11 Zimene zidzaŵagwere ana ako aŵiriwo, Hofeni ndi Finehasi, zidzakhala chizindikiro kwa iwe. Aŵiri onsewo adzafa tsiku limodzi.
35Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika amene adzachita zinthu pomvera zimene mtima wanga ufuna ndiponso potsata maganizo anga. Ndidzammangira banja lolimba, ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthaŵi zonse.
36Apo aliyense amene adzatsale pabanja pako adzabwera kudzampempha iyeyo tindalama kapena kachakudya. Adzanena kuti, “Mundilole ndizithandizako ansembe, kuti ndipezeko kanthu kakudya.” ’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.