1Tsono Ayuda amaposa bwanji anthu a mitundu ina? Kapena pali phindu lanjinso pa kuumbala?
2Pali phindu lalikulu ndithu kukhala Myuda. Choyamba, Mulungu adapatsa Ayuda mau ake kuti aŵasunge.
3Nanga ngati ena mwa iwo anali osakhulupirika, kodi chifukwa cha kusakhulupirika kwaoko ndiye kuti ndi Mulungu yemwe sadzakhulupirika?
4Mas. 51.4 Mpang'ono pomwe. Koma anthu adziŵe kuti zimene Mulungu amalankhula nzoonadi, ngakhale kuti anthu onse ndi onama. Ndi monga Malembo akunenera kuti,
“Inu Mulungu, anthu adziŵe
kuti mumanena zoona mukamalankhula,
adziŵe kuti mumapambana mukamazenga mlandu.”
5Koma ngati kuipa mtima kwathu kuwonetsa kuti Mulungu ngwolungama, tinganene chiyani? Kodi tinganene kuti Mulungu ngwosalungama pamene atilanga? (Ndikulankhulatu monga momwe anthu ena amalankhulira).
6Mpang'ono pomwe. Mulungu akadakhala wosalungama, akadatha bwanji kukhala woweruza anthu onse?
7Koma wina nkunena kuti, “Nanga kunama kwanga kutaonetsa koposa kale kuti Mulungu ndi woona, ndi kuwonjezera pa ulemu wake, kodi pamenepo angandiweruze kuti ndine wochimwa?”
8Apo bwanji sitingonena kuti, “Tizichita zoipa kuti zabwino ziwoneke”? Alipo anthu ena amene amatisinjirira kuti timanena zotere. Iwoŵa adzalangidwa monga kuyenera.
Palibe munthu wolungama9Nanga bwanji tsono? Kodi ife Ayuda tikuposa anthu a mitundu ina? Mpang'ono pomwe. Tafotokoza kale kuti onse ndi ochimwa, Ayuda ndi anthu a mitundu ina omwe.
10Mas. 14.1-3; 53.1-3 Paja Malembo akuti,
“Palibe munthu wolungama,
ai ndithu ndi mmodzi yemwe.
11Palibe munthu womvetsa,
palibe munthu wofunadi kutumikira Mulungu.
12Onse asokera,
onse pamodzi achimwa,
palibe wochita zabwino,
ai ndithu ndi mmodzi yemwe.
13 Mas. 5.9; Mas. 140.3 M'kamwa mwao m'moopsa ngati manda apululu,
ndi lilime lao amalankhula zonyenga,
pamilomo pao pamatuluka mau aululu,
ululu wake wonga wa mamba.
14 Mas. 10.7 M'kamwa mwao m'modzaza ndi matemberero,
mumatuluka mau oŵaŵa.
15 Yes. 59.7, 8 Amafulumira kupweteka ndi kupha anzao.
16Amasakaza ndi kusautsa kulikonse kumene amapita,
17ndipo njira yamtendere saidziŵa.
18 Mas. 36.1 Saopa Mulungu mpang'ono pomwe.”
19Tsono tikudziŵa kuti zonse zimene Malamulo a Mulungu anena, zimakhalira amene ali olamulidwa ndi Malamulowo. Cholinga chake nchakuti anthu onse asoŵe ponena, ndipo onse adzazengedwe ndi Mulungu.
20Mas. 143.2; Aga. 2.16Pajatu palibe munthu amene Mulungu amamuwona kuti ngwolungama chifukwa cha kutsata Malamulo chabe. Malamulo amangotizindikiritsa kuchimwa kwathu.
Za m'mene Mulungu amaonera anthu kuti ngolungama21Koma tsopano yaoneka njira yopezera chilungamo pamaso pa Mulungu, ndipo njira yake si kutsata Malamulo ai. Malamulowo ndi aneneri omwe amaichitira umboni.
22Aga. 2.16Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai,
23popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera.
24Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.
25Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
26Koma tsopano wapereka Yesu pofuna kutsimikiza chilungamo chake, kuti anthu adziŵe kuti Iye mwini ngwolungama, adziŵenso kuti aliyense wokhulupirira Yesu amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.
27Nanga tsono pamenepa munthu anganyadenso? Iyai, sanganyade konse. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti pamaso pa Mulungu chachikulu si ntchito zabwino zimene munthu amachita, koma chachikulu nkuti munthu azikhulupirira.
28Paja timaona kuti munthu amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, osati pakutsata Malamulo ai.
29Kapena Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha kodi? Suja alinso Mulungu wa anthu a mitundu ina? Ndithu ndiyenso Mulungu wa anthu a mitundu ina.
30Deut. 6.4; Aga. 3.20Paja Mulungu ndi mmodzimodzi yemweyo, mwakuti pakukhulupirira, anthu oumbalidwa amapezeka kuti ngolungama pamaso pake, nawonso osaumbalidwa, pakukhulupirira amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu.
31Kodi ndiye kuti tikutaya Malamulo pamene tikunenetsa kuti pafunika chikhulupiriro? Mpang'ono pomwe. Makamaka tikuŵafikitsa pake penipeni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.