Mphu. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Gen. 1.26-28; 2.7 Mulungu adapanga anthu ndi dothi,

ndipo amaŵabwezeranso kudothi komweko.

2Adaŵalembera masiku oŵerengeka ndi nthaŵi yochepa,

koma adaŵapatsa ulamuliro pa zolengedwa zonse.

3Adaŵapatsa mphamvu zonga zake,

ndipo adaŵalenga mofanafana naye.

4Zolengedwa zamoyo zonse adazipatsa mantha oopa anthu.

Adapatsadi anthu ulamuliro pa nyama ndi mbalame.

5Anthuwo adalandira mphamvu zisanu kwa Mulungu,

ina yachisanu ndi chimodzi inali ya nzeru za

kuganiza bwino,

inanso yachisanu ndi chiŵiri inali ya nzeru

zolongosolera ntchito za mphamvu zakezo.

6Anthuwo adaŵapatsa pakamwa, maso ndi makutu,

adaŵapatsanso mtima woganizira.

7 Gen. 2.17 Adaŵadzaza ndi nzeru zodziŵa zinthu ndi zomvetsa zinthu,

ndipo adaŵasonyeza kuti zabwino ndi izi,

zoipa ndi izi.

8Mulungu adaikamo kuŵala kwake m'mitima mwao,

kuti aŵaonetse ukulu wa ntchito zake.

9Adaŵalola

kuti azinyadira ntchito zake zodabwitsa

mpaka muyaya.

10Choncho iwo adzatamanda dzina lake loyera,

adzalalika ukulu wa ntchito zake.

11Iye adaŵaninkha nzeru,

naŵapatsa Malamulo opatsa moyo.

12Adapangana nawo chipangano chamuyaya,

naŵaululira Malamulo ake.

13Motero anthu adaona ulemerero wa Mulungu ndi maso ao,

ndipo adamva ulemerero wa mau ake m'makutu mwao.

14Iye adaŵauza kuti, “Lewani choipa chilichonse,”

ndipo adaphunzitsa munthu aliyense m'mene azikhalira

ndi anzake.

Za kuweruza kwa Mulungu

15Machitidwe a anthu amadziŵika pamaso pa Mulungu

nthaŵi zonse,

sangathe kubisika konse pamaso pake.

16Kuyambira ali ana, machitidwe ao adapendekera ku zoipa,

akulephera kusandutsa mitima yao youma ngati miyala

kuti ikhale yofeŵa ngati mnofu.

17Mtundu uliwonse adaupatsa mtsogoleri wake,

koma adasankha Aisraele kuti akhale choloŵa chake.

18Amaŵaphunzitsa mwambo poti ndi ana ake achisamba,

amaŵaunikira ndi chikondi chake ndipo saŵasiya.

19Ntchito zao zonse zili ngati dzuŵa pamaso pake,

amaziyang'anitsa nthaŵi zonse.

20Zoipa zao sizibisika pamaso pa Ambuye,

Iwo amaona machimo ao onse.

21Ambuye ngokoma mtima, amadziŵa zolengedwa zao,

saziwononga kapena kuzisiya, koma amazisunga.

22Munthu akathandiza osauka,

kwa Ambuye chithandizocho chili ngati mphete

yamtengowapatali,

ndipo chifundo chimenecho kwa Ambuye chili ngati

mwana wa diso lao.

23Potsiriza pake adzadzambatuka nadzalipira onse,

ndipo adzaŵabwezera zonse pamutu pao monga kuyenera.

24Komabe munthu wolapa Ambuye amampatsa mpata kuti

abwerere kwa Iwo,

ndipo munthu wa khama lofookerapo Ambuye amamlimbitsa mtima.

Aŵauza kuti atembenuke mtima

25 Yer. 3.12 Tsono bwerera kwa Ambuye, ndipo leka zoipa zako.

Upemphere kwa Ambuye, ndipo uchepetse machimo ako.

26Bwerera kwa Mulungu Wopambanazonse,

ndipo lekeratu kuchimwa.

Udane nazo kwambiri zonyansa zonse.

27 Mas. 6.5; Yes. 38.18; Bar. 2.17, 18 Tingatamande bwanji Mulungu Wopambanazonse

pamene tili m'manda,

ngati sitimtsira ulemu pamene tili moyo?

28Anthu akufa sangathe kutamanda,

ali ngati anthu amene kunalibe chikhalire.

Okhaokhawo amene ali ndi moyo angathe kutamanda Mulungu.

29Ndithu chifundo cha Ambuye nchachikulu,

ndipo amakhululukira onse obwerera kwa Iwo.

30Munthu sangathe kukhala ndi zonse,

poti ana a anthu sadzakhalapo mpaka muyaya.

31Kodi chilipo china choŵala kupambana dzuŵa?

Komabe mwina kuŵala kwa dzuŵa kumaleka.

Momwemonso munthu wamnofu ndi wamagazi sakhalira

kuganiza zoipa.

32Mulungu amayang'anira nyenyezi zamumlengalenga,

koma anthu onse ndi fumbi ndi phulusa chabe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help