Mk. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu achiritsa munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa(Mt. 8.28-34; Lk. 8.26-39)

1Tsono Yesu ndi ophunzira ake adafika ku tsidya la Nyanja ya Galileya, ku dera la Agerasa.

2Yesu atangotuluka m'chombo, munthu wina wogwidwa ndi mzimu woipa adadzakumana naye kuchokera ku manda.

3Munthuyo ankakhala kumandako, ndipo padaalibe wina wothanso kummanga, ngakhale ndi unyolo womwe.

4Kale anthu adaayesa kangapo kummanga miyendo ndi zitsulo, ndiponso kummanga manja ndi maunyolo, koma iye ankangoŵamwetsula maunyolowo, ndipo zitsulo zomanga miyendozo ankangozithyola. Padaalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumgonjetsa.

5Usana ndi usiku ankakhala kumandako ndi m'mapiri, akumangofuula ndi kudzipweteka ndi miyala.

6Pamene iye adaona Yesu chakutali, adamthamangira nadzamgwadira.

7Mokweza mau adati, “Kodi ndakuputani chiyani, Inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wopambanazonse? M'dzina la Mulungu ndikukupemphani, musandizunze.”

8Adaatero chifukwa Yesu anali atanena kuti, “Mzimu woipawe, tuluka mwa munthuyu!”

9Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine ‘Chigulu,’ chifukwa tilipo ochuluka.”

10Ndipo iye adadandaulira Yesu kwambiri kuti mizimuyo asaitulutsire kunja kwa dera limenelo.

11Pafupi pomwepo, pachitunda poteropo, pankadya gulu lalikulu la nkhumba.

12Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti, “Tipirikitsireni ku nkhumbazo, tiloleni tikaloŵe m'menemo.”

13Yesu adailoladi. Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo. Zonse zidaalipo ngati zikwi ziŵiri.

14Oŵeta nkhumbazo adathaŵa, nakasimbira anthu mu mzinda ndi ku midzi. Pamenepo anthu adatuluka kuti akaone zimene zidaachitikazo.

15Atafika kumene kunali Yesuko, adaona munthu adaagwidwa ndi mizimu yoipa uja atakhala pansi, atavala, misala ija itatha, munthu woti adaloŵedwa ndi chigulu cha mizimu yoipa. Anthuwo adagwidwa ndi mantha.

16Anzao amene adaaonerera zonse zikuchitika, adaŵasimbira zimene zidaamuchitikira munthu wamizimuyo ndiponso nkhumba zija.

17Apo anthuwo adampempha Yesu kuti achoke ku dera laolo.

18Pamene Yesu ankakaloŵa m'chombo, munthu amene adaagwidwa ndi mizimu yoipa uja adampempha kuti apite nao.

19Koma Yesu adakana namuuza kuti, “Iyai, iwe pita kumudzi kwa anthu akwanu, ukaŵafotokozere zazikulu zimene Ambuye akuchitira mwa chifundo chao.”

20Munthuyo adapitadi nakayamba kufalitsa ku dera lotchedwa Mizinda Khumi, zazikulu zimene Yesu adaamchitira. Atamva zimenezo anthu onse adazizwa kwambiri.

Yesu achiza mwana wa Yairo ndi mai wina(Mt. 9.18-26; Lk. 8.40-56)

21Yesu adaolokanso nyanja. Pamene adafika pa tsidya, chinamtindi cha anthu chidasonkhana pamphepete pa nyanja pamene panali Iyepo.

22Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Ataona Yesu, adadzigwetsa ku mapazi ake,

23nayamba kumdandaulira kwambiri. Adati, “Pepani, mwana wanga wamkazi ali pafupi kufa. Ngati nkotheka, mukamsanjike manja kuti achire ndi kukhala ndi moyo.”

24Yesu adanyamuka namapita naye. Anthu ambiri adatsagana naye namayenda momupanikiza.

25Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri.

26Tob. 2.10Adaazunzika zedi ndi asing'anga ochuluka amene ankayesa kumuchiza. Mwakuti adaamwaza chuma chake chonse, komabe osapeza bwino konse. M'malo mwake matendawo analikunka nakulirakulira.

27Maiyo anali atamva za Yesu. Tsono adaloŵa m'chinamtindi cha anthu chija, nkuphaphatiza mpaka kukafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza chovala chake.

28Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale zovala zake zokhazo, ndichira.”

29Ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka, mwiniwakeyo nkumva m'thupi mwake kuti matenda ake aja atha.

30Pomwepo Yesu adazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Iye. Tsono adatembenuka nayang'ana anthu aja ndipo adafunsa kuti, “Kodi ndani wandikhudza zovala?”

31Ophunzira ake adati, “Ndi Inu nomwe mukuwona kuti anthu akukupanikizani, ndiye mungafunse bwanji kuti, ‘Ndani wandikhudza?’ ”

32Koma Yesu adayang'anayang'ana kuti aone yemwe wachita zimenezo.

33Apo mai uja adachita mantha nayamba kunjenjemera, chifukwa anali atazindikira zimene zidaamuwonekerazo. Adadza pafupi, nadzigwetsa pansi pamaso pa Yesu, nkumufotokozera zonse monga momwe zidaachitikira.

34Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere. Matenda anu atheretu.”

35Yesu akulankhulabe, kudafika anthu kuchokera kunyumba kwa mkulu uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.”

36Koma Yesu sadasamale zimene anthuwo ankanena. Adauza mkulu uja kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupirira.”

37Tsono sadalole kuti winanso atsagane naye, koma Petro, ndi Yakobe, ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo.

38Pamene iwo adafika kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja, Yesu adaona chipiringu cha anthu, akulira ndi kubuma.

39Iye ataloŵa, adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita phokoso lonseli ndi kubuma? Mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.”

40Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola. Iye adaŵatulutsira panja onse, nangotenga bambo wake ndi mai wake wa mwanayo, ndiponso amene adaali naye aja, nkuloŵa kuchipinda kumene kunali mwana uja.

41Tsono adagwira mwanayo pa dzanja namuuza kuti, “Talita, kumi.” (Ndiye kuti, “Mtsikana iwe, ndikuti dzuka.”)

42Pomwepo mtsikanayo adadzukadi, nayamba kuyenda, pakuti adaali wa zaka khumi ndi ziŵiri. Pamenepo anthu aja adazizwa kwambiri.

43Koma Yesu adaŵalamula mwamphamvu kuti zimenezo wina aliyense asazidziŵe. Kenaka adaŵauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help