2 Maf. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Naamani achiritsidwa khate lake

1 lokwanira kunyamula abulu aŵiri. Pakuti kuyambira tsopano ine sindidzaperekanso nsembe zopsereza, kapena nsembe ina iliyonse, kwa mulungu wina aliyense, koma kwa Chauta basi.

18Chauta andikhululukire ine pa chokhachi chakuti pamene mbuyanga mfumu akupita kukapembedza ku nyumba ya Chauta wake Rimoni, ine ndimatsagana naye ndipo ndimakagwada m'nyumba ya Rimoniyo. Chauta andikhululukire ine mtumiki wanu zimenezi.”

19Elisa adamuuza kuti, “Ai, inu kafikeni bwino.”

Gehazi alangidwa ndi nthenda ya khate

20Koma Naamani atangoyenda mtunda pang'ono, Gehazi, mtumiki wa Elisa mneneri wa Mulungu, adayamba kulingalira kuti, “Mbuyanga walekerera Naamani Msiriyayu, osalandira zimene adabwera nazo kudzapereka. Pali Chauta, Mulungu wamoyo, ine ndimthamangira kuti ndikalandireko kanthu.”

21Motero Gehazi adalondola Naamani uja. Naamani ataona kuti munthu akumthamangira, adatsika pa galeta kuti amchingamire. Tsono adafunsa kuti “Kodi nkwabwino?”

22Gehazi adati, “Inde, nkwabwino. Koma mbuyanga wandituma chifukwa tsopano apa kwangomufikira anthu aŵiri a m'gulu la aneneri, kuchokera ku dziko lamapiri la Efuremu. Tsono akukupemphani kuti chonde muŵapatseko ndalama zasiliva 3,000 ndi zovala ziŵiri zapaphwando.”

23Pamenepo Naamani adati, “Inu tengani ndithu ngakhale 6,000 zimene.” Choncho adamkakamiza, nalonga m'matumba ndalama za silivazo, pamodzi ndi zovala zapaphwandozo, nasenzetsa antchito ake aŵiri. Ndipo adanyamuka, antchitowo patsogolo, Gehazi pambuyo pao.

24Tsono Gehazi uja atafika kuphiri kumene kunali nyumba ya Elisa, adaŵalanda antchitowo ndalama zija nazilonga m'nyumba mwake. Ndipo adaŵauza kuti apite, iwo nkupita.

25Pambuyo pake Gehazi adapita kwa mbuyake. Elisa adamufunsa kuti, “Kodi Gehazi, unali kuti?” Iyeyo adati, “Sindidayende kwina kulikonse, bambo.”

26Koma Elisayo adamufunsanso kuti, “Kodi ukuyesa kuti sindidakuwone monse muja munthu uja amatsika pa galeta kuti adzakuchingamire? Kodi imeneyi inali nthaŵi yolandira ndalama ndi zovala, minda ya olivi ndi ya mphesa, kapena ng'ombe, akapolo kapena adzakazi?

27Ndiyetu tsono khate la Naamani lidzakumatirira iweyo ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.” Motero Gehazi adatuluka m'nyumbamo ali ndi khate lambuu ngati chipale.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help