2 Mbi. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apereka Nyumba Ya Chauta(1 Maf. 8.62-66)

1 Lev. 9.23-24 Solomoni atatha kupemphera, moto udatsika kuchokera kumwamba, nuwotcha nsembe zopsereza pamodzi ndi nsembe zina. Pomwepo ulemerero wa Chauta udadzaza Nyumba ya Chauta ija.

2Tsono ansembe sadathe kuloŵa m'Nyumbamo, popeza kuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'menemo.

31Mbi. 16.34; 2Mbi. 5.13; Eza. 3.11; Mas. 100.5; 106.1; 107.1; 118.1; 136.1; Yer. 33.11 Ndipo Aisraele onse ataona moto wotsika kumwambawo, pamodzi ndi ulemerero wa Chauta m'Nyumba ya Chauta ija, adaŵerama, nazyolikitsa nkhope zao pansi, ndipo adapembedza nathokoza Chauta ndi mau akuti,

“Ndithu Chauta ndi wabwino

pakuti chikondi chake chosasinthika

chimakhala mpaka muyaya.”

4Tsono mfumu pamodzi ndi anthu onsewo adapereka nsembe pamaso pa Chauta.

5Mfumu Solomoni adapereka nsembe pakupha ng'ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Motero mfumuyo pamodzi ndi anthu onsewo adaipereka Nyumba ya Mulungu ija.

6Ansembe adaimirira m'malo mwao, pamene Alevi ankatamanda Chauta poimba nyimbo zothokoza Chauta ndi zipangizo zimene Davide adapanga, pakuti chikondi cha Mulungu chimakhala mpaka muyaya. Anthu onseŵa ankatero nthaŵi zonse Davide akamapereka matamando kudzera mwa iwo. Poyang'anana ndi iwowo panali ansembe oliza malipenga. Ndipo Aisraele onse adaakhala chilili.

7Tsono Solomoni adapatula malo apakatikati a bwalo lija lokhala kumaso kwa Nyumba ya Chauta, ndipo kumeneko adaperekako nsembe zopsereza ndiponso mafuta a nsembe zachiyanjano, chifukwa chakuti pa guwa lamkuŵa limene adapanga Solomoni lija, panalibe malo oti nkukhalapo nsembe zonse zopsereza ndi zopereka za chakudya, pamodzi ndi mafuta omwe.

8Nthaŵi imeneyo Solomoni adachita chikondwerero cha masiku asanu ndi aŵiri pamodzi ndi Aisraele onse. Unali msonkhano waukulu kwambiri, kuyambira ku chipata cha ku Hamati mpaka ku kamtsinje wa ku Ejipito.

9Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adachita mwambo wotsekera. Pakuti masiku asanu ndi aŵiri anthuwo ankachita mwambo wopereka guwa, ndipo masiku ena asanu ndi aŵiri kunali chikondwerero.

10Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiŵiriwo, Solomoni adauza anthu aja kuti apite kwao. Anthuwo anali okondwa ndiponso a mtima wosangalala, chifukwa cha zokoma zimene Chauta adaachitira Davide ndi Solomoni ndiponso Aisraele, anthu ake.

Mulungu aonekeranso Solomoni(1 Maf. 9.1-9)

11Motero Solomoni adamaliza kumanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu ndipo zonse zimene adaaganiza kuti achite m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba yake adazimalizadi mokhoza kwambiri.

12Tsono Chauta adamuwonekera usiku namuuza kuti, “Ndamva pemphero lako, ndipo ndadzisankhira malo ano kuti akhale Nyumba yoperekera nsembe.

13Ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe, kapena ndikalamula dzombe kuti liwononge zomera zapadziko, kapena ndikatumiza mliri pakati pa anthu anga,

14ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.

15Ndiye maso anga adzatsekuka, ndipo ndidzatchera khutu ku pemphero limene adzapemphere ku malo ano.

16Chifukwa tsopano ndaisankha ndipo ndapatula Nyumba ino kuti dzina langa lizikhala m'menemo mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga, zidzakhala m'menemo nthaŵi zonse.

17Tsono iweyo ukamayenda pamaso panga monga m'mene ankayendera Davide bambo wako, ukamachita zonse zimene ndidakulamula ndi kumvera mau anga ndi malangizo anga,

181Maf. 2.4ukatero Ine ndidzaukhazikitsa mpando wako waufumu, monga momwe ndidalonjezera Davide bambo wako kuti, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wolamulira Israele.’

19“Koma inu mukapatuka ndi kusiya malamulo anga ndi malangizo anga amene ndidakupatsani, mukamatumikira milungu ina ndi kumaipembedza,

20pamenepo ndidzaŵachotsa Aisraelewo m'dziko limene ndidaŵapatsa. Ndipo nyumba ino imene ndaipatulira dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga, ndipo ndidzaisandutsa ngati mwambi ndi chisudzo chabe pakati pa anthu a mitundu yonse.

21Ndiye Nyumba yotchuka ndi yokomayi, aliyense wopitapo adzadabwa nadzafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta walichita zotere dzikoli, ndiponso Nyumbayi?’

22Tsono azidzati, ‘Nchifukwa chakuti anthuwo adasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao, amene adaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, ndipo adadzifunira milungu ina, namaipembedza ndi kumaitumikira. Nkuwona Chautayo waŵachita zoipa zonsezi.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help