Deut. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Malamulo khumi(Eks. 20.1-17)

1Mose adaitana Aisraele onse naŵauza kuti: Inu Aisraele, mverani malamulo ndi malangizo onse amene ndikukupatsani lero. Muŵaphunzire, ndipo musamaledi kuti muzimvera.

2Chauta, Mulungu wathu, adachita nafe chipangano pa phiri la Horebu.

3Sikuti chipangano chimenechi adangochita ndi makolo athu okha ai, komanso ndi ife tonse amene tili ndi moyo pano lero lino.

4Mulungu adalankhula nanu pamasompamaso, kuchokera m'moto paphiri paja.

5Nthaŵi imene ija, ine ndidaaima pakati pa inu ndi Chauta ndi kumakuuzani mau a Chauta, chifukwa inu munkaopa moto, ndipo simudakwere phiri. Chauta adaati,

6“Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndidakutulutsa iwe ku Ejipito, dziko laukapolo.

7“Usapembedze Mulungu wina, koma Ine ndekha.

8 Lev. 26.1; Deut. 4.15-18; 27.15 “Usadzipangire fano kufanizira kanthu kolengedwa kalikonse kakumwamba, kapena ka pa dziko lapansi, kapena ka m'madzi a pansi pa dziko.

9Eks. 34.6, 7; Num. 14.18; Deut. 7.9, 10 Usagwadire fano lililonse kapena kulipembedza, chifukwa Ine, Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, sindilola kuti wina apikisane nane. Ndimalanga amene adana nane. Ndimalanganso zidzukulu zao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.

10Koma ndimachitira chifundo chosasinthika anthu zikwi zambirimbiri amene amandikonda namasunga malamulo anga.

11 Lev. 19.12 “Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Chauta adzamlanga aliyense wotchula pachabe dzina lakelo.

12 Eks. 16.23-30; 31.12-14 “Uzisunga tsiku la Sabata ndi kuliyeretsa, monga momwe Ine Chauta, Mulungu wako, ndidakulamulira.

13Eks. 23.12; 31.15; 34.21; 35.2; Lev. 23.3 Uzigwira ntchito zako zonse ndi kuzitsiriza pa masiku asanu ndi limodzi.

14Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata la Chauta, Mulungu wako. Pa tsiku limenelo, usagwire ntchito iliyonse iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, wantchito wako wamwamuna, mdzakazi wako, ng'ombe yako, bulu wako, kaya choŵeta chako chilichonse, ngakhale mlendo wokhala m'mudzi mwako. Motero atumiki ako aamuna ndi aakazi azipumanso monga iwe wemwe.

15Uzikumbukira kuti paja udaali kapolo m'dziko la Ejipito, ndipo kuti Ine Chauta, Mulungu wako, ndidakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula. Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wako, adakulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata ndi kuliyeretsa.

16 Deut. 27.16; Mphu. 3.1-16; Mt. 15.4; 19.19; Mk. 7.10; 10.19; Lk. 18.20; Aef. 6.2; Aef. 6.3 “Uzilemekeza atate ako ndi amai ako, monga momwe Chauta, Mulungu wako, adakulamulira, kuti pakutero masiku a moyo wako achuluke ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa iwe.

17 Gen. 9.6; Lev. 24.17; Mt. 5.21; 19.18; Mk. 10.19; Lk. 18.20; Aro. 13.9; Yak. 2.11 “Usaphe.

18 Lev. 20.10; Mt. 5.27; 19.18; Mk. 10.19; Lk. 18.20; Aro. 13.9; Yak. 2.11 “Usachite chigololo.

19 Lev. 19.11; Mt. 19.18; Mk. 10.19; Lk. 18.20; Aro. 13.9 “Usabe.

20 Eks. 23.1; Mt. 19.18; Mk. 10.19; Lk. 18.20 “Usamchitire mnzako umboni wonama.

21 Aro. 7.7; 13.9 “Usasirire mkazi wa mnzako. Usasilire nyumba yake, munda wake, wantchito wake wamwamuna, wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzakoyo.”

22 Ahe. 12.18, 19 Chauta adaalankhula mau ameneŵa kwa inu nonse amene mudaasonkhana kuphiri kuja. Iye adanena mau ameneŵa osaonjezerapo kanthu, ndipo adalankhula mau amphamvu, kuchokera m'moto, m'mitambo ndiponso mu mdima wandiweyani. Pambuyo pake adalemba malamulo khumiwo pa miyala iŵiri, ndipo adandipatsa ine.

Anthu achita mantha(Eks. 20.18-21)

23Pamene mudamva mau ochokera mu mdima, phiri lonse likuyaka moto, atsogoleri anu pamodzi ndi mafumu a mabanja anu adabwera kwa ine,

24ndipo adati, “Chauta, Mulungu wathu, adatiwonetsa ukulu ndi ulemerero wake, ndipo tidamumva akulankhula m'moto muja. Lero taona kuti munthu angathe kukhalabe ndi moyo ndithu, ngakhale kuti Mulungu walankhula naye.

25Koma ife, tiferenji kuno? Moto woopsawo udzatiwononga. Tidzafa tikamva Chauta, Mulungu wathu, akulankhulanso.

26Kodi alipo wina aliyense amene adakhalapo ndi moyo atamva Mulungu wamoyo akulankhula m'moto monga momwe tidamvera ifeyo?

27Inu Mose, musendere, ndipo mukamvere zonse zimene Chauta, Mulungu wathu, adzanene. Kenaka mubwere, mudzatiwuze tonsefe zimene wakuuzani inuyo. Ife tidzamvera ndipo tidzachita.”

28Pamene mudalankhula ndi ine, Chauta adamva mau anu ndipo adandiwuza kuti, “Ndamva zimene akulankhula anthuzi, ndi zabwino zokhazokha zonsezo.

29Ine ndikufuna kuti aziganiza zimenezo masiku onse. Ndikufuna kuti azindiwopa nthaŵi zonse, ndipo kuti azimvera malamulo anga, kuti zinthu ziŵayendere bwino iwowo ndi zidzukulu zao mpaka muyaya.

30Uŵauze kuti abwerere ku mahema ao.

31Koma iwe Mose, ukhale kuno pamodzi ndi Ine, ndipo ndidzakupatsa malamulo, malangizo ndi zina zoyenera kuzitsata. Zonsezi ukaŵaphunzitse anthu kuti azikasunga malamulowo m'dziko limene ndidzaŵapatsalo.”

32Inu Aisraele, musamale ndithu kuchita zimene Chauta, Mulungu wanu, wakulamulani, osapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere.

33Muziyenda m'njira imene Chauta, Mulungu wanu, wakulamulani, kuti zinthu zidzakuyendereni bwino, ndipo mudzapitirire kukhala ndi moyo m'dziko limene mukakhalemolo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help