1Pamenepo Pilato adalamula kuti atenge Yesu ndi kumkwapula.
2Tsono asilikali adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake. Adamuveka chovala chofiirira,
3nadza kwa Iye nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda!” Ndipo adayamba kumuwomba makofi.
4Pilato adatulukanso nauza Ayudawo kuti, “Onani, ndikumtulutsira kuli inu kuno kuti mudziŵe kuti sindikumpeza chifukwa chilichonse.”
5Pamene Yesu adatuluka, atavala nsangamutu ija ndi chovala chofiirira chija, Pilato adati, “Nayutu munthu uja.”
6Akulu a ansembe ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja ataona Yesu, adafuula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Pilato adaŵauza kuti, “Mtengeni inuyo mukampachike, ine ndiye sindikumpeza chifukwa.”
7Anthuwo adati, “Ife tili ndi lamulo, ndipo potsata lamulolo ayenera kufa, chifukwa ankati, ‘Ndine Mwana wa Mulungu.’ ”
8Pamene Pilato adamva mau ameneŵa, adachita mantha kwabasi.
9Tsono adaloŵanso m'nyumba ya bwanamkubwa ija nafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, kwanu nkuti?” Koma Yesu sadayankhe kanthu.
10Pamenepo Pilato adamufunsa kuti, “Sukundiyankha? Kodi sukudziŵa kuti ine ndili ndi mphamvu zokumasula, ndiponso mphamvu zokupachika?”
11 pa tsiku la Sabata, chifukwa Lasabata limenelo linali lalikulu. Nchifukwa chake adakapempha Pilato kuti alamule kuti akathyole miyendo ya anthu opachikidwa aja, nkuŵachotsa.
32Tsono asilikali adabwera, nathyola miyendo ya mmodzi mwa aŵiri aja amene adaapachikidwa pamodzi ndi Yesu. Adateronso ndi mnzake uja.
33Koma pamene adafika pa Yesu, poona kuti wafa kale, sadathyole miyendo yake.
34Koma mmodzi mwa asilikali aja adamubaya m'nthiti mwake ndi mkondo, ndipo nthaŵi yomweyo mudatuluka magazi ndi madzi.
35Amene adaona zimenezi ndiye akuzichitira umboni, kuti inunso mukhulupirire. Umboni wakewo ngwoona, ndipo mwiniwakeyo akudziŵa kuti zimene akunena nzoona.
36Eks. 12.46; Num. 9.12; Mas. 34.20 Izi zidaatero kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.”
37Zek. 12.10; Chiv. 1.7 Ndipo penanso Malembo akuti, “Anthu azidzamuyang'ana amene iwo adamubaya.”
Yesu aikidwa m'manda(Mt. 27.57-61; Mk. 15.42-47; Lk. 23.50-56)38Pambuyo pake Yosefe wa ku Arimatea adapempha Pilato kuti amlole kukachotsa mtembo wa Yesu. (Yosefeyo anali wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa choopa akulu a Ayuda.) Tsono Pilato atamlola, iye adakachotsa mtembowo.
39Yoh. 3.1, 2 Kudabweranso Nikodemo, yemwe uja amene adaabwera kwa Yesu usiku poyamba paja. Iye adabwera ndi mafuta onunkhira a mure osanganiza ndi aloe, kulemera kwake ngati makilogaramu 32.
40Anthu aŵiriwo adatenga mtembo wa Yesu, naukulunga m'nsalu zoyera zabafuta pamodzi ndi zonunkhira zija, potsata mwambo wamaliro wachiyuda.
41Kumene Yesu adaapachikidwako kunali munda. Ndipo m'mundamo munali manda atsopano, amene anali asanaikemo munthu.
42Tsono popeza kuti linali tsiku la Ayuda lokonzekera chikondwerero cha Paska, ndipo mandawo anali pafupi, adaika Yesu m'menemo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.