1Chauta adalankhulanso ndi Yeremiya kachiŵiri, akadali m'ndende m'bwalo la alonda a mfumu, adati,
2“Naŵa mau a Chauta amene adalenga dziko lapansi, naliwumba ndi kulikhazikitsa. Iyeyo dzina lakedi ndi Chauta.
3Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa.
4Chauta, Mulungu wa Israele, akunenapo mau pa za nyumba za mu mzinda uno ndi za nyumba za mafumu a ku Yuda, zimene anthu adazigwetsa kuti amange zotchinjiriza mzindawo, nthaŵi ya nkhondo. Akuti,
5Ababiloni akubwera kudzauthira nkhondo, ndipo nyumba zake zidzadzaza ndi mitembo ya anthu amene ndidzaŵapha mokwiya ndi mwachipseramtima. Mzinda umenewu ndaufulatira chifukwa cha makhalidwe oipa a anthu ake.
6“Komabe m'tsogolo mwake ndidzaupatsanso moyo ndi kuuchiritsa. Anthu ake ndidzaŵachiritsa ndi kuŵapatsa zabwino zochuluka ndi mtendere weniweni.
7Ndidzakhazikanso pabwino anthu a ku Yuda ndi a ku Israele, ndi kuŵabwezera momwe adaaliri poyamba.
8Ndidzaŵayeretsa pochotsa machimo ao onse ondichimwira. Ndidzaŵakhululukira zoipa zonse zimene adachita pondipandukira.
9Mzinda umenewu udzamveketsa mbiri yanga yabwino, ndipo udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemu. Anthu a mitundu yonse pansi pano adzanditamanda ndi kundilemekeza pakumva za zabwino zonse zimene ndauchitira mzinda umenewu. Adzachita mantha ndi kunjenjemera, poona kuti mzindawo ndaupatsa madalitso ndi zokoma zosaŵerengeka.”
10Chauta akuti, “Anthu amanena za malo ano kuti ndi bwinja, opanda munthu ndi nyama yomwe. Komabe m'mizinda ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu m'mene tsopano muli zii, mopanda munthu ndi nyama yomwe, mudzamveka
111Mbi. 16.34; 2Mbi. 5.13; 7.3; Eza. 3.11; Mas. 100.5; 106.1; 107.1; 118.1; 136.1mau achisangalalo ndi achimwemwe, mau achikondwerero a mkwati wamwamuna ndi wamkazi. M'Nyumba ya Mulungunso mudzamveka nyimbo ya anthu odzapereka nsembe zothokozera Mulungu. Nyimbo yake azidzati,
“ ‘Tamandani Chauta Wamphamvuzonse,
popeza kuti ndi wabwino
ndipo chikondi chake nchamuyaya!’
Ndithudi, ndidzaŵabwezeranso pabwino monga momwe adaaliri,” akutero Chauta.
12Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ku malo ano a chipululu opanda munthu ndi nyama yomwe, ndi ku mizinda yake yonse, kudzakhalanso mabusa kumene abusa angaŵetereko nkhosa zao.
13Ku mizinda yakumapiri, ku chigwa, kumwera ku Negebu, ku dera la Benjamini, ku maiko oyandikana ndi Yerusalemu ndiponso ku mizinda ya Yuda, nkhosa zidzapitanso pamaso pa munthu woziŵerenga,” akutero Chauta.
14 Yer. 23.5, 6 Chauta akutinso, “Akubwera masiku pamene ndidzachitadi zimene ndidalonjeza anthu a ku Israele ndi a ku Yuda.
15Masiku amenewo ndiponso pa nthaŵi yomweyo, ndidzaphukitsa nthambi yolungama kuchokera kubanja kwa Davide. Munthuyo adzachita zabwino ndi zolungama m'dziko lonse.
16Nthaŵi imeneyo anthu a ku Yuda adzapulumuka, ndipo a ku Yerusalemu adzakhala pa mtendere. Motero mzindawu udzakhala ndi dzina loti ‘Chauta ndiye chipulumutso chathu.’ ”
17 2Sam. 7.12-16; 1Maf. 2.4; 1Mbi. 17.11-14 Zoonadi, Chauta akunena kuti, “Davide sadzasoŵa mdzukulu woloŵa m'malo mwake pa mpando waufumu wa Israele.
18Num. 3.5-10 Ansembe Achilevi sadzasoŵa munthu womabwera kwa Ine nthaŵi zonse kudzapereka nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi nsembe zinanso, mpaka muyaya.”
19Chauta adauza Yeremiya kuti,
20“Mau anga ndi aŵa: Ine ndidachita chipangano ndi usana ndi usiku kotero kuti ziŵirizi zimafika pa nthaŵi yake. Ndipo chipanganocho sichingaphwanyike konse.
21Chimodzimodzinso ndidachita chipangano ndi Davide, mtumiki wanga, kuti nthaŵi zonse adzakhala ndi mdzukulu wodzakhala pa mpando wake waufumu. Ndidachitanso chipangano china ndi ansembe Achilevi kuti iwowo adzanditumikira nthaŵi zonse. Ndipo zipangano zimenezi sizingaphwanyike konse.
22Ndidzachulukitsa zidzukulu za mtumiki wanga Davide ndi atumiki anga ansembe Achilevi, kuchuluka kwake ngati kwa nyenyezi zakuthambo kapena kwa mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.”
23Chauta adafunsa Yeremiya kuti, “Kodi sudamve m'mene anthu ena akulankhulira,
24kumanena kuti, ‘Chauta wakana mabanja aŵiri aja amene adaŵasankha?’ Motero anthuwo amanyoza mpingo wanga osauyesanso ngati mtundu wa anthu.
25Koma Ine Chauta ndidachita chipangano ndi usana ndi usiku, ndipo ndidapanga malamulo oyendetsa zonse za pa dziko lapansi ndi zamumlengalenga.
26Tsono monga ndachita zimenezi motsimikiza, chonchonso ndidzachisunga chipangano chimene ndidachita ndi zidzukulu za Yakobe, ndiponso ndi Davide, mtumiki wanga. Ndidzasankhula mmodzi mwa zidzukulu za Davide kuti azilamulira zidzukulu za Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Komatu tsono ndidzaŵamvera chifundo ndi kuŵabwezeranso pabwino.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.