1 Yes. 15.1—16.14; 25.10-12; Ezek. 25.8-11; Amo. 2.1-3; Zef. 2.8-11 Ponena za Mowabu,
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti,
“Tsoka kwa mzinda wa Nebo, wasanduka chipululu.
Kiriyataimu wachititsidwa manyazi, wagonjetsedwa.
Linga lake lankhondo alinyoza ndipo aligumula.
2Mowabu sakutchukanso.
Adampanganirana zachiwembu ku Hesiboni, adati,
‘Tiyeni timuwononge, asakhalenso mtundu wa anthu.’
Ndipo inu okhala ku Madimeni,
adzakukhalitsani chete,
adzakupirikitsani ndi lupanga.
3“Imvani kulira kwachisoni
kwa anthu a ku Horonaimu, akuti,
‘Chisakazo ndi chiwonongeko chachikulutu!’
4Mowabu waonongeka,
ana ake akulira kwambiri.
5Anthu akupita nalira kwambiri
pa chikwera cha ku Luhiti.
Kulira kwa chiwonongeko kukumveka
ku matsitso a ku Horonaimu.
6Thaŵani, mudzipulumutse.
Thamangani ngati mbidzi yam'chipululu.
7Inunso mudzagwidwa
chifukwa choti munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu.
Kemosi, mulungu wanu, adzatengedwa ukapolo,
pamodzi ndi ansembe ake ndi akalonga ake.
8Woononga uja adzasakaza mzinda uliwonse,
palibe mzinda ndi umodzi womwe umene udzapulumuke.
Malo am'zigwa adzaonongeka,
malo okwera nawonso adzasakazika.
Zidzachitika monga momwe Chauta adanenera.
9“Mowabu mchenjezeni,
chifukwa posachedwa asakazika.
Mizinda yake isanduka mabwinja,
ikhala yopanda anthu.
10“Ndi wotembereredwa
amene amagwira ntchito ya Chauta mwaulesi.
Ndi wotembereredwa
amene amaletsa lupanga lake kutema ndi kupha anthu.
11Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira unyamata wake,
ngati vinyo wokhazikika pa masese ake,
osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina
kuthira mu mtsuko wina.
Sadatengedwe ukapolo.
Nchifukwa chake khalidwe lake lili losasinthika,
ndipo fungo lake lili lomwe lija.”
12Chauta akunena kuti, “Chenjerani tsono, akubwera masiku pamene ndidzatuma anthu oti Mowabuyo adzamkhuthule ngati vinyo. Kenaka mitsuko yake itasanduka yopanda kanthu m'kati, ndidzaiphwanya.
13Motero Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi, mulungu wake, monga momwe Israele adachitira naye manyazi Betele, mulungu amene ankamukhulupirira.
14“Kodi mungathe kunena bwanji kuti,
‘Ife ndife ngwazi, asilikali olimba mtima pa nkhondo?’
15Woononga Mowabu ndi mizinda yake wabwera.
Anyamata ake asee akupita kukaphedwa.
Ikutero mfumu imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
16Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi.
Chiwonongeko changokhala pang'onong'ono kuti chimugwere.
17Mumvereni chisoni kwambiri inu nonse anansi ake,
anzake nonse amene mumamdziŵa.
Ndipo munene kuti,
‘Ogo, taonani m'mene yathyokera ndodo
yachifumu yamphamvu ija!
Taonani m'mene yathyokera ndodo yaulemu ija!’
18“Inu anthu a ku Diboni, tsikanipo pa ulemerero wanu,
khalani pansi poumapa.
Woononga Mowabu wafika kudzamenyana nanu,
wapasula malinga anu ankhondo.
19Inu amene mumakhala ku Aroere,
imani m'mbali mwa mseu muziwonerera.
Mufunse mwamuna amene wathaŵa
ndiponso mkazi amene wapulumuka,
munene kuti, ‘Kodi kwagwanji?’
20Iwo adzayankha kuti,
‘Ukutu Mowabu wagwa, amchititsa manyazi,
mlireni mofuula.
Mulengeze ku mtsinje wa Arinoni
kuti Mowabu wasanduka bwinja.’
21“Chiweruzo chafika ku dziko lakumapiri, ndiye kuti mizinda iyi: Holoni, Yaza, Mefati
22ndi Diboni, Nebo ndi Betedibilataimu,
23Kiriyataimu, Betegamuli, Betemeoni,
24Keriyoti, Bozira ndi mizinda yonse ya ku Mowabu, yakutali ndi yakufupi.
25Mphamvu za Mowabu zaonongeka, mkono wake wolimba wathyoka,” akutero Chauta.
Zakuti Mowabu adzamchititsa manyazi26“Mledzeretseni Mowabu chifukwa adadzikuza poukira Chauta. Avimvinizike m'masanzi ake omwe. Akhale chinthu chomachiseka.
27Kodi suja Israele adaali chinthu chonyozeka kwa iwe? Kodi adapezeka pakati pa mbala, kuti nthaŵi zonse polankhula za iye uzimpukusira mutu momunyoza?”
28Chauta akuti,
“Inu okhala ku Mowabu, siyani mizinda yanu.
Kapezeni pokhala pakati pa mathanthwe.
Mukhale ngati nkhunda yomanga chisa kukamwa kwa phanga.
29Tamva za kunyada kwa Mowabu,
ndi wonyadadi kwabasi.
Ndi wodzikweza, wodzitama, wodzitukumula,
ndipo ndi wa mtima wodzimva zedi.
30Ndikudziŵa kudzikuza kwake.
Mau ake odzitama ngachabechabe,
ntchito zake nzopanda pake.
31Motero ndikulira chifukwa cha Mowabu.
Ndikulira mwachisoni chifukwa cha anthu
onse a ku Mowabu.
Ndikulira anthu a ku Kiriheresi.
32Ndikulira anthu a ku Sibima
kupambana m'mene ndidalirira anthu a ku Yazere.
Iwe mzinda wa Sibima, uli ngati mpesa
umene nthambi zake zidatambalala mpaka ku nyanja,
kukafika mpaka ku Yazere.
Woononga wasakaza zipatso zako zam'chilimwe,
wasakaza mipesa yako yonse.
33Kusangalala ndi kukondwa kwa dziko lachonde
la Mowabu kwatha.
Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopondera mphesa.
Palibe amene akufuula mokondwa akamaponda mphesa.
Kufuula kulipo, koma si kufuula kokondwa ai.
34“A ku Hesiboni ndi a ku Eleale akulira movutika. Kulira kwao kukumveka mpaka ku Yaza, kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati-Selisiya. Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.
35Ndidzaŵaphadi Amowabu amene amapereka nsembe ku akachisi ku mapiri, ndi kufukiza lubani kwa milungu yao,” akutero Chauta.
36“Nchifukwa chake mtima wanga ukulira Mowabu ngati chitoliro. Mtima wanga ukulira anthu a ku Kiriheresi ngati chitoliro, chifukwa chuma chao chonse chimene adaachipata chatheratu.
37Kumutu kwa munthu aliyense nkometa, ndevu nazonso nzometa, manja onse ndi ochekekachekeka, ndipo m'chiwuno mwao avala ziguduli.
38Pa madenga onse a ku Mowabu ndiponso m'miseu yake simukumvekanso kanthu kena, koma kulira kokha. Ndamtswanya Mowabu ngati chiŵiya chopanda ntchito.
39Taonani m'mene watswanyikira! Tamvani m'mene akulirira anthu ake! Taonani m'mene wakhalira chofulatira mwamanyazi! Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka, chinthu chochititsa mantha kwa anzake okhala nawo pafupi,” akutero Chauta.
Zakuti Amowabu sadzapulumuka40Chauta akunena kuti,
“Mtundu wina udzachita kuuluka
nkudzagwera Mowabu ngati nkhwazi ya mapiko otambalitsa.
41Mizinda idzagwidwa,
malinga adzalandidwa.
Tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku
Mowabu idzakhala ili thithithi ndi mantha,
ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira.
42Mowabu adzaonongeka,
sadzakhalanso mtundu wa anthu,
pakuti adadzikuza poukira Chauta.
43Nkhaŵa, dzenje ndi msampha
zikuyembekeza inu anthu okhala ku Mowabu,”
akutero Chauta.
44“Wothaŵa nkhaŵa, adzagwa m'dzenje.
Wotuluka m'dzenje, adzakodwa mu msampha.
Zimenezi nzimene ndidzamgwetsere Mowabu
pa nthaŵi ya chilango chake,”
akutero Chauta.
45“Amene akuthaŵa, amaima pa mthunzi wa Hesiboni,
chifukwa chotopa kwambiri.
Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni,
malaŵi a moto abuka kuchokera
ku nyumba ya mfumu Sihoni,
ndipo motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu,
dziko la anthu andeu.
46Tsoka kwa iwe Mowabu!
Anthu opembedza Kemosi atha.
Ana ako onse aamuna ndi aakazi adatengedwa ukapolo.
47Komabe masiku akutsogolo
ndidzambwezeranso ufulu Mowabu,”
akutero Chauta.
Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.