1Imvani pemphero langa, Inu Chauta.
Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga.
Mundiyankhe chifukwa cha kukhulupirika kwanu
ndi kulungama kwanu.
2 Aro. 3.20; Aga. 2.16 Musandizenge mlandu ine mtumiki wanu,
popeza kuti palibe munthu wamoyo
amene ali wolungama pamaso panu.
3Mdani wandilondola,
wavimviniza moyo wanga m'dothi,
wandikhazika mu mdima,
ngati anthu amene adafa kale.
4Nchifukwa chake mtima wanga wafooka m'kati mwanga,
mumtima mwangamu mukuchita mantha.
5Ndimakumbukira masiku amakedzana,
ndimasinkhasinkha za zonse zimene mwazichita,
ndimalingalira ntchito za manja anu.
6Ndimatambalitsira manja anga kwa Inu,
mtima wanga umamva ludzu lofuna Inu,
monga limachitira dziko louma.
7Fulumirani kundiyankha, Inu Chauta.
Ndataya mtima kwambiri,
musandibisire nkhope yanu,
kuti ndingafanefane ndi anthu otsikira ku manda.
8Lolani kuti m'maŵa ndimve
za chikondi chanu chosasinthika,
chifukwa ndimakhulupirira Inu.
Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo,
pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu.
9Inu Chauta, pulumutseni kwa adani anga,
chifukwa ndathaŵira kwa Inu.
10Phunzitseni, kuti ndizichita zofuna Inu,
pakuti ndinu Mulungu wanga.
Mzimu wanu wabwino unditsogolere
pa njira yanu yosalala.
11Sungani moyo wanga, Inu Chauta,
kuti dzina lanu lilemekezeke.
Munditulutse pa mavuto
chifukwa cha kulungama kwanu.
12Kanthani adani anga
chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika pa ine.
Muwononge onse ondizunza,
pakuti ine ndine mtumiki wanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.