1Ndimakweza maso anga ku mapiri.
Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?
2Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta,
amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
3Sadzalola phazi lako kuti literereke,
Iye amene amakusunga sadzaodzera.
4Zoonadi, amene amasunga Israele,
ndithu sadzaodzera kapena kugona.
5Chauta ndiye amene amakusunga,
Chauta ndiye mtetezi wako
ali ku dzanja lako lamanja.
6DzuƔa silidzakupweteka masana,
mwezi sudzakuvuta usiku.
7Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse,
adzasamala moyo wako.
8Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.