1Inu anthu opanda manyazinu,
chitani msonkhano, mulape,
2adani asanakumwazeni ngati mungu,
ukali woopsa wa Chauta usanakugwereni,
tsiku la mkwiyo wa Chauta lisanakupezeni.
3Funafunani Chauta, inu nonse odzichepetsa,
inu amene mumamvera malamulo ake.
Chitani zolungama, khalani odzichepetsa.
Mwina mwake mudzatha kupulumuka
pa tsiku la mkwiyo wa Chauta.
Mulungu adzaononga maiko oyandikana ndi Yuda4
Mau a Chauta akukudzudzulani,
inu anthu a ku Kanani, dziko la Afilisti,
akuti, “Ndidzakuwonongani nonse
sipadzatsala ndi mmodzi yemwe.”
6Dziko limene lili m'mphepete mwa nyanja,
lidzasanduka madambo a abusa,
ndi makola a nkhosa.
7Kumeneko kudzakhala dziko la otsala a m'banja la Yuda.
Azidzadyetsa nkhosa zao m'mbali mwanyanjamo,
ndipo madzulo azidzagona ku nyumba za ku Asikeloni.
Pakuti Chauta, Mulungu wao adzaŵasamalira,
ndiye amene adzaŵabwezere ufulu wao.
Za Amowabu ndi Aamoni8 Yes. 15.1—16.14; 25.10-12; Yer. 48.1-47; Ezek. 25.8-11; Amo. 1.13-15; Yer. 49.1-6; Ezek. 21.28-32; 25.1-7; Amo. 1.13-15 Chauta akuti,
“Ndamva kunyoza kwa Amowabu,
ndiponso kutukwana kwa Aamoni,
m'mene anyozera anthu anga
ndi m'mene adzikuzira m'dziko mwao.
9 Gen. 19.24 Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse
ndikulumbira kuti,
Pali Ine ndemwe, Mulungu wamoyo wa Israele,
Amowabu adzaonongedwa ngati anthu a ku Sodomu,
Aamoni adzaonongedwa ngati anthu a ku Gomora.
Malowo adzakhala ngati dera la zitsamba za
khwisa ndi la nkhuti za mchere,
dziko lachipululu mpaka muyaya.
Otsala mwa anthu anga adzafunkha malowo.
Opulumuka a mtundu wanga adzalandira
malowo ngati dziko lao.”
10Chimenechi chidzakhala chilango
choyenerera kunyada kwaoko,
chifukwa adanyoza anthu a Chauta Wamphamvuzonse.
11Motero Chauta adzaŵaopsa kwambiri.
Adzaononga milungu yonse ya pa dziko lapansi.
Mitundu yonse ya anthu idzampembedza Chauta,
mtundu uliwonse ku dziko lakwao.
Za Etiopiya ndi Asiriya12 Yes. 18.1-7 Inunso Aetiopiya,
Chauta adzakukanthani ndi lupanga lake.
13 Yes. 10.5-34; 14.24-27; Nah. 1.1—3.19 Chauta adzasamulira dzanja lake kumpoto
ndi kuwononga dziko la Asiriya.
Mzinda wa Ninive adzausandutsa bwinja,
udzakhala wagwaa ngati chipululu.
14Choncho zoŵeta zizidzagona kumeneko
chimodzimodzinso nyama zonse zakuthengo.
Adembo ndi akanungu azidzagona pa makapotolosi ake.
Akadzidzi azidzalira pa windo,
ndipo makwangwala azidzakhala pa bwalo lake.
Mitengo yake yamkungudza adzaisadza.
15Umenewo ndiwo mzinda
umene unkadzimva kuti ndi wokhazikika,
umene mumtima mwake unkati,
“Ine pano! Palibenso wina ai!”
Tauwonani m'mene wasakazikira tsopano!
Wasanduka bwinja lokhalamo nyama zakuthengo.
Aliyense wodutsamo
azidzangotsonya nkumapukusa mutu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.