Gen. 47 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsono Yosefe adatenga abale ake asanu napita nawo kwa Farao kukamuuza kuti, “Bambo wanga pamodzi ndi abale anga abwera kuchokera ku Kanani. Abwera ndi zoŵeta zao monga nkhosa ndi ng'ombe, pamodzi ndi zao zonse. Tsopano akukhala m'dziko la Goseni.”

2Aŵa ndi asanu mwa abale angawo.

3Apo Farao adaŵafunsa kuti, “Kodi mumagwira ntchito yanji?” Iwo adayankha kuti, “Ndife abusa bwana, monga momwe ankachitira makolo athu.”

4“Tabwera kudzakhala nao m'dziko muno bwana, chifukwa ku Kanani kuli njala yoopsa, kotero kuti kulibe ndi msipu womwe wodyetsa zoŵeta. Chonde bwana, mutilole tikakhale ku dziko la Goseni.”

5Tsono Farao adauza Yosefe kuti, “Bambo wako pamodzi ndi abale ako abwera kwa iwe.

6Dziko la Ejipito lili m'manja mwako. Ukhazike bambo wako pamodzi ndi abale ako m'dziko lachonde, akakhale ku Goseni. Ndipo ngati ena mwa iwo ndi akatswiri a zoŵeta, uŵapatse ukapitao woyang'anira zoŵeta zanga.”

7Yosefe adatenga bambo wake Yakobe, napita naye kwa Farao. Ndipo Yakobe adadalitsa Faraoyo.

8Kenaka Farao adafunsa Yakobe kuti, “Muli ndi zaka zingati?”

9Yakobe adayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka zimenezi nzochepa ndiponso zamavuto, zosalingana ndi zaka za makolo anga pa nthaŵi yao yonse pamene anali moyo.”

10Ndipo atadalitsa Farao, adatsazikana naye nkuchokapo.

11Yosefe adamkhazika m'dziko la Ejipito bambo wake uja, pamodzi ndi abale ake onse aja, ndipo adaŵapatsa malo a nthaka yabwino ndi yachonde, m'chigawo chotchedwa Ramsesi, monga momwe Farao adaalamulira.

12Yosefe adapereka chakudya kwa bambo wake ndi kwa abale ake ndi kwa mbumba yonse, potsata kuchuluka kwa ana ao.

Yosefe ayendetsa ntchito pa nthaŵi ya njala

13Njala ija idakula kwambiri, kotero kuti panalibe chakudya pa dziko lonse lapansi, ndipo anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani komwe adafooka nayo njalayo.

14Yosefe adasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a ku Ejipito pamodzi ndi a ku Kanani adaamwaza pogula tirigu. Ndalama zonsezo adazitenga napita nazo kunyumba kwa Farao.

15Ndalama zonse zitaŵathera anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani, Aejipito ambiri adabwera kwa Yosefe, namuuza kuti, “Tipatseniko chakudya! Musatilekerere kuti tife, chitanipo kanthu! Ndalama zathu zonse zatha!”

16Yosefe adaŵayankha kuti “Bwerani ndi zoŵeta zanu, tidzasinthane ndi chakudya, ngati mukuti ndalama zanu zidatha zonse.”

17Motero adabwera ndi zoŵeta zao kwa Yosefe, nasinthitsa ndi chakudya zoŵeta zaozo, monga akavalo, nkhosa ndi mbuzi, ng'ombe ndi abulu. Chaka chimenecho Yosefe adaŵapatsa chakudya anthuwo mosinthana ndi zoŵeta zaozo.

18Chitatha chaka chimenecho, anthuwo adapitanso kwa Yosefe namuuza kuti, “Bwana, ife sitingakubisireni kuti ndalama zathu pamodzi ndi zoŵeta zathu zomwe, zatithera. Palibe chilichonse chotsala choti tingathe kukupatsani, tingodzipereka ifeyo ndi minda yathuyi.

19Musatilekerere kuti tife m'dziko mwathu, inu mukuwona. Mutipatseko chakudya, ndipo tidzigulitsa ifeyo ndi minda yathu yomwe. Tidzakhala akapolo a Farao, iye adzatenga minda yathu kuti ikhale yake. Mutipatseko mbeu kuti tisafe ndi njala, kutinso minda yathu isakhale masala.”

20Apo Yosefe adagulira Farao dziko lonse la Ejipito. Mwejipito aliyense adagulitsa minda yake chifukwa njalayo inali itafika poipa kwambiri. Motero dziko lonse lidasanduka la Farao.

21Yosefe adaŵasandutsa akapolo anthuwo ponseponse m'dziko la Ejipito.

22Dziko limene sadagule ndi la ansembe lokha. Iwowo sadagulitse dziko lao, popeza kuti Farao ankaŵapatsa chakudya choti azidya.

23Yosefe adauza anthu kuti, “Onani tsopano ndakugulani pamodzi ndi minda yanu yonse, kugulira Farao. Tsono nazi mbeu, mubzale m'minda mwanu.

24Pa nthaŵi yokolola mudzapereka kwa Farao chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse pa zokolola zanuzo, ndipo zina zonse zotsala zidzakhala zanu. Zina mudzasungire mbeu, koma zina mudzadye inuyo, mabanja anu ndi antchito anu.”

25Anthu adayankha kuti, “Mwapulumutsa moyo wathu. Mwatichitira zabwino bwana, tidzakhala akapolo a Farao.”

26Motero Yosefe adapanga lamulo m'dziko lonse la Ejipito, kuti chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse pa zokolola chidzakhala cha Farao. Lamulo limeneli lilipobe mpaka lero lino. Koma maiko a ansembe okha sadaŵatenge kuti akhale a Farao.

Yakobe alumbiritsa Yosefe potsiriza

27Aisraele atakhazikika ku Ejipito, adalemera kwambiri, ndipo adaberekanso ana ambiri.

28Yakobe adakhala ku Ejipito, zaka 17, choncho zaka za moyo wake zidakwanira 147.

29Gen. 49.29-32; 50.6 Tsono ali pafupi kumwalira, adaitana mwana wake Yosefe namuuza kuti, “Ngati ukundikondadi, undigwire m'kati mwa ntchafu zangazi, ulonjeze kuti udzandikomera mtima ndi kukhulupirika kwa ine, ndipo kuti mtembo wanga sudzauika ku Ejipito kuno.

30Ndifuna kukagona pamodzi ndi makolo anga. Mtembo wanga udzauchotse ku Ejipito kuno ukauike m'manda a makolo anga.” Yosefe adayankha kuti, “Ndidzachita monga momwe mwaneneramu.”

31Yakobe adauzanso Yosefe kuti, “Lumbira pamaso panga kuti udzachitadi zimenezi.” Apo Yosefe adalumbiradi, ndipo Yakobe adaŵerama kumutu kwa bedi lake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help