1Tsono munthu wolungama adzaima osaopa kanthu
pamaso pa anthu amene ankamusautsa
ndi amene ankanyazitsa kulimbika kwake.
2Pomuwona adzanjenjemera ndi mantha oopsa,
adzadabwa poona kupulumuka kwake kosayembekezeka.
3Ndi nthumanzi mumtima mwao,
ndiponso movutika ndi moŵiringula,
adzayamba kuuzana kuti,
4“Ndi uyutu munthu uja tinkamuseka nkumunyozayu.
Tinali opusa!
Tinkayesa kuti moyo wake unali wamisala,
kutinso imfa yake inali yochititsa manyazi.
5Nanga adamuŵerengera bwanji
pamodzi ndi ana a Mulungu?
Adapezeka bwanji pakati pa anthu oyera mtima?
6Kwenikweni ndife amene tidasokera posiya njira yoona,
kuŵala kwa chilungamo sikudatiŵalire ife,
ndipo dzuŵa silidatitulukire.
7Tidayenda mosadzimana kanthu
m'njira ya kusamvera ndi ya chiwonongeko.
Tidayenda m'zipululu zopanda njira,
sitidadziŵe njira ya Ambuye.
8Nanga kunyada kwathu kudatipindulira chiyani?
Chuma chimene tinkachinyadira chidatipatsa chiyani?
9Zonsezi zidangozimirira
ngati mthunzi, ngati mphekesera.
10“Zonsezo zidangopita
ngati chombo chodutsa pa mafunde amphamvu,
chimene sichisiya mkwaso pamene chadutsa,
ndipo njira yake siwonekanso.
11Ndi ngatinso mbalame youluka m'mwamba,
osaonetsa chizindikiro cha njira yake,
koma tingoona mapiko ake akukupiza mu mpweya.
Ndi mphamvu zake imauluka mwaliŵiro,
koma sitiwonapo chizindikiro pamene yadutsa.
12Zilinso ngati muvi umene anthu auponya
pofuna kulasa kanthu,
mphepo imene waidula imabwerera msanga mwakale,
ndipo sitizindikira pamene yadutsa.
13Chimodzimodzinso ife, titabadwa chatsopano,
pompo tidaleka kukhala ndi moyo,
ndipo tinalibe nkanthu kabwino komwe koti tikasonyeze,
koma tidaonongekeratu ndi ntchito zathu zoipa.”
14Zoonadi chikhulupiriro cha munthu
wosamvera Mulungu chili ngati mungu
wouluzika ndi mphepo,
ngati thovu lopepuka lomwazika ndi namondwe.
Chili ngati utsi womwazika ndi mphepo,
chimazimirira msanga
monga momwe amaiŵalikira mlendo
wa tsiku limodzi lokha.
15Koma olungama ali ndi moyo wamuyaya.
Malipiro ao ali kwa Ambuye,
Wopambanazonse ndiye amaŵasamala.
16Nchifukwa chake adzalandira ulemerero waufumu
ndi nsangamutu yaulemu kuchokera kwa Ambuye,
pakuti Mulunguyo adzaŵateteza
ndi dzanja lake lamanja,
adzaŵachirikiza ndi mkono wake
ngati chishango.
17 Aef. 6.11-17 Iyeyo adzavala changu chake cholipsira
ngati zovala zankhondo,
zolengedwa zidzakhala ngati zida zake
zothyolera adani.
18Chilungamo chidzakhala ngati malaya ankhondo,
chiweruzo choona chidzakhala ngati chisoti chankhondo.
19Kuyera kwake kudzakhala
ngati chishango chosapambanika.
20Ukali wake udzakhala wakuthwa ngati lupanga.
Zolengedwa zonse za m'dziko lapansi
zidzamuthandiza kumenya nkhondo
yothyola adani ake openga.
21M'mitambo yamumlengalenga
yokhala ngati mauta okoka bwino,
mudzafumira mphezi zong'anima,
zimene zidzalasa adani ngati mivi yosaphonya.
22Ukali wa Mulunguwo udzaŵagwetsera matalala,
monga amachitira makina oponyera miyala.
Madzi am'nyanja adzaŵaopsa,
mitsinje idzaŵamiza mopanda chisoni.
23Mphepo yamkuntho idzaŵaukira,
idzaŵamwaza ngati kamvulumvulu.
Choncho kusaweruzika kudzasandutsa dziko lonse
kukhala chipululu,
machitidwe oipa adzagwetsa pansi
mipando ya mafumu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.