1Ndi Simoni, mwana wa Oniyasi, mkulu wa ansembe,
amene adakonza Nyumba ya Mulungu
pamene anali moyo,
naizinganso ndi malinga.
2Adakhazikitsa maziko a zipupa zazitali ziŵiri,
zolimbitsa khoma la Nyumba ya Mulungu ponse pozungulira.
3Pa nthaŵi yake anthu adakumba dziŵe la madzi,
dziŵe lake ngati nyanja kukula.
4Mtima wake unali pa kuteteza anthu ake kuti asaonongeke,
motero adalimbitsa mzinda kuti usagonje akauthira nkhondo.
5Ankaoneka waulemu kwambiri anthu akamzungulira
iye akamatuluka kuseri kwa chinsalu chochinga.
6Anali ngati nthanda yoŵala m'mitambo
kapena ngati mwezi pamene uli wathunthu.
7Anali ngati dzuŵa loŵala pa Nyumba ya Mulungu
Wopambanazonse,
kapena ngati kuŵala kwa utawaleza pa mitambo yonyezimira.
8Anali ngati maluŵa a pa nthaŵi ya phukira,
kapena ngati akakombo pafupi ndi kasupe wa madzi,
kapenanso ngati nthambi ya mtengo wa lubani
yonunkhira bwino pa dzinja.
9Anali ngati lubani wofuka m'chombo,
kapena ngati chikho chopangidwa ndi golide wosalala,
chimene adachikometsa ndi miyala yamtengowapatali.
10Anali ngati mtengo wa olivi wodzaza ndi zipatso
kapena ngati mkungudza wofika ku mitambo.
11Ankati akavala mkanjo wake wapamwambo,
nkukolekapo zokongoletsera zamakaka,
nkudzakwera ku guwa lansembe,
bwalo la Nyumba yopembedzeramo linkalemerera.
12Pamene ansembe ankampatsa zigawo za nsembe,
iye ataima pafupi ndi guwa,
abale ake ali kwete m'mbalimu,
anali ngati kamtengo ka mkungudza ka ku Lebanoni,
kokhala pakati pa kanjedza.
13Ana onse a Aroni, atavala zokongola,
ankaima pamaso pa gulu lonse la Aisraele,
ali ndi nsembe zopereka kwa Ambuye m'manja mwao.
14Atatha kuchita mwambo wapaguwa
ndi kupereka nsembe kwa Mulungu Wamphamvuzonse,
Wopambanazonse,
15ankatambalitsa dzanja nkugwira chikho,
nkuthira vinyo wa fungo lokoma patsinde pa guwa
ngati nsembe yopereka kwa Mulungu Wopambanazonse,
mfumu ya anthu onse.
16Tsono ana a Aroni ankafuula namaliza malipenga ao asiliva.
Ndipo ankachita phokoso lalikulu ngati
chikumbutso pamaso pa Ambuye.
17Pa nthaŵi yomweyo anthu onse pamodzi
ankadzigwetsa pansi moŵeramitsa mutu,
namapembedza Mulungu wao, Wamphamvuzonse,
Wopambanazonse.
18Ndipo gulu lanyimbo linkamutamanda ndi mau ao,
poimba nyimbo za maimbidwe okongola.
19Anthu ankapemba Ambuye Wopambanazonse
ndi kupemphera pamaso pa Mulungu Wachifundo
mpaka mwambo wa Ambuye utatha,
ndi kutsiriza dongosolo lake.
20 Num. 6.24-27 Tsono wansembe wamkulu ankatsika kuchokera ku guwa
nkukweza manja ake pa gulu lonse la Aisraele,
kuti aŵadalitse m'dzina la Ambuye.
21Ndiye anthu ankaŵerama pansi kachiŵiri
kuti alandire madalitso a Mulungu Wopambanazonse.
Pemphero lotamanda22Tsopano tamandani Mulungu amene adalenga zonse,
amene amachita ntchito zodabwitsa kulikonse.
Ndiye amene amatilera kuyambira m'mimba mwa amai,
ndipo amatichitira chifundo.
23Atipatse chimwemwe chamumtima
ndipo masiku athu ano akhale amtendere
m'dziko la Israele mpaka muyaya.
24Ambuye azipitiriza kutichitira chifundo
ndipo atipulumutse pa nthaŵi yomwe ino.
Mitundu yoipa ya anthu25Pali mitundu iŵiri ya anthu imene ndimaipidwa
nayo,
ndipo wachitatu si mtundu wa anthu konse.
26Amenewo ndi anthu okhala ku phiri la Seiri,
Afilisti ndi anthu opusa a ku Sekemu.
Nzeru za Yesu mwana wa Sira27Ine Yesu, mwana wa Sira, mwana wa Eleazara wa
ku Yerusalemu,
ndalemba m'buku muno malangizo a luntha ndi a nzeru
ochokera mumtima mwanga.
28Ngwodala munthu amene amatanganidwa ndi kuphunzira
malangizo ameneŵa.
Amene amaŵasunga mu mtima, adzakhala wanzeru.
29Amene amasunga malangizo ameneŵa,
adzapambana pa zonse,
poti akuyenda m'kuŵala kwa Ambuye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.