Mas. 80 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha kuti mtundu wonse ubwerere mwakaleKwa Woimbitsa Nyimbo. Kutsata maimbidwe a nyimbo yoti: Akakombo a Chipangano. Salmo la Asafu.

1 Eks. 25.22 Imvani, Inu Mbusa wa Israele,

Inu amene mumatsogolera anthu a Yosefe

ngati gulu la nkhosa.

Inu amene mumakhala pa akerubi

ngati pa mpando wanu wachifumu,

2dziwonetseni kwa mafuko a Efuremu

ndi Benjamini ndi Manase.

Onetsani mphamvu zanu,

ndipo mubwere kudzatipulumutsa.

3Inu Mulungu, tibwezereni mwakale,

mutiwonetse nkhope yanu yokondwa,

ndipo ife tidzapulumuka.

4Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse,

mudzakwiyira mapemphero a anthu anu mpaka liti?

5Mwaŵadyetsa chisoni ngati chakudya,

mwaŵapatsa misozi ngati chakumwa.

6Mwaŵasandutsa chinthu chonyozeka

kwa anzathu a mitundu ina,

ndipo adani athu akakhala pamodzi, amangotiseka.

7Inu Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale,

mutiwonetse nkhope yoŵala, kuti ife tipulumuke.

8Mudatulutsa mpesa wanu Israele m'dziko la Ejipito.

Mudapirikitsa mitundu ina ya anthu kuti muubzale mpesawo.

9Mudaulimira munda mpesawo,

udamera mizu yozama, nudzaza m'dzikolo.

10Mapiri adaphimbidwa ndi mthunzi wake,

mikungudza yaikulu yomwe idaphimbidwa ndi nthambi zake.

11Nthambizo zidafika mpaka ku nyanja yaikulu yakuzambwe,

ndipo mphukira zake mpaka ku mtsinje waukulu wakuvuma.

12Nanga chifukwa chiyani mwagumula mpanda wake,

kuti opita m'njira azithyola nawo zipatso zake?

13Nguluŵe zam'nkhalango zimauwononga,

ndipo zonse zoyenda m'thengo zimaudya.

14Mutembenukirenso kwa ife, Inu Mulungu Wamphamvuzonse,

muyang'ane Inu okhala kumwamba, ndipo muwone.

Samalani mpesawo,

15mtengo woyambirira

umene Inu mudaubzala ndi dzanja lanu lamanja.

16Adani athu autentha, augwetsa pansi.

Ayang'aneni iwowo mokwiya ndi kuŵaononga.

17Koma ndi dzanja lanu

muteteze anthu amene mudaŵasankha,

anthu amene Inu nomwe mwaŵalimbikitsa

kuti akutumikireni.

18Tsono sitidzakusiyaninso,

tipatseni moyo,

ndipo tidzatama dzina lanu mopemba.

19Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse,

tibwezereni mwakale.

Mutiwonetse nkhope yoŵala,

kuti ife tipulumuke.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help