1Mafumu onse a Aamori amene ankakhala kuzambwe kwa Yordani, pamodzi ndi mafumu a Akanani okhala m'mphepete mwa nyanja, adamva kuti Chauta adaumitsa Yordani pamene Aisraele ankaoloka. Choncho adachita mantha, ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraelewo.
Aumbala Aisraele ku Giligala2Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “Sema miyala ngati mipeni, kuti uumbalire Aisraeleŵa.”
3Yoswa adasemadi mipeni yamiyalayo, naŵaumbala onsewo ku phiri lotchedwa “Koumbalira.”
4 ndipo mpaka lero lino malo ameneŵa akudziŵika ndi dzina limeneli.
10 Eks. 12.1-13 Pamene Aisraele anali m'zithando ku Giligala m'chigwa cha ku Yeriko, adachita Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo.
11M'maŵa mwake mpamene anthu aja adayamba kudya chakudya cha ku Kanani. Adakazinga tirigu, naphikanso buledi wosatupitsa tsiku limenelo.
12Eks. 16.35 Zitangotero, mana uja adaleka kugwa, ndipo sadapezekenso pakati pa Aisraele. Kuyambira nthaŵi imeneyo adayamba kudya chakudya cha ku Kanani.
Yoswa ndi munthu wa lupanga.13Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, mwadzidzidzi adaona munthu ataimirira kutsogolo kwake, lupanga losolola lili m'manja. Tsono Yoswa adapita pomwe panali munthupo, namufunsa kuti, “Kodi iwe ndiwe mmodzi wa ankhondo athu kapena ndiwe mdani wathu?”
14Munthu uja adayankha kuti, “Sindine mmodzi mwa ankhondo anu kapenanso mdani wanu. Ndine mtsogoleri wa gulu lankhondo la Chauta pano.” Choncho Yoswa adadzigwetsa pansi chafufumimba naati, “Ine ndine wantchito wanu, mbuyanga. Nanga mufuna kuti ndichite chiyani?”
15Wolamula gulu lankhondo la Chauta uja adamuyankha kuti, “Vula nsapato zako. Malo amene ukuimirirapoŵa ngoyera.” Yoswa adachitadi zimene adamuuzazo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.