Mphu. 45 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mose

1 Malamulowo.

Aroni

6 Eks. 4.14 Ambuye adakweza Aroni, munthu woyera mtima

ngati Mose,

mbale wake wa fuko la Levi.

7 Eks. 28.1-43 Adapangana naye chipangano chosatha,

namdzoza kuti akhale wansembe wa anthu ake.

Adamlemekeza pomuveka zovala zokongola kwambiri

ndi mkanjo waulemu.

8Adamuveka zokoma kotheratu, ndi kumpatsa

zizindikiro za mphamvu zake.

Kabudula wabafuta, mkanjo wautali ndi chovala

cha efodi.

9Pa mkanjo adaikapo mphonje zonga makangaza,

nauzunguliza ndi mabelu ambiri agolide,

omaimba akuyenda,

kuti azimveka m'Nyumba ya Mulungu,

ndi kukhala chikumbutso kwa anthu ake.

10Adamuveka zovala zaunsembe zagolide ndi zobiriŵira,

ndiponso zofiirira, zopetedwa bwino ndi mmisiri.

Kenaka adamuveka chovala chapachifuwa

chimene adaikamo Urimu ndi Tumimu,

cha thonje lofiira, ntchitodi yaumisiri.

11Pa chovalacho adaikapo miyala yamtengowapatali

yozokotedwa ngati zosindikizira

yokhala m'zoikamo zagolide.

Zonsezi zinali ntchito za akatswiri.

Pa miyalayo adalembapo maina khumi ndi aŵiri,

okumbutsa mafuko a Israele.

12Pamwamba pa nduŵira yake adaikapo nsangamutu

yagolide yolembapo kuti “Woperekedwa kwa Ambuye.”

Chinali chinthu chaluso kwambiri, makaka okongola zedi,

chinthu chokondweretsa m'maso pochiwona.

13Iye asanaloŵe unsembe, panalibe zinthu

zokongola chotere.

Palibe munthu wina aliyense amene adazivalapo,

koma ana ake okha a Aroni,

ndiponso zidzukulu zake nthaŵi zonse.

14Nsembe zake zidzapserezedwa kwathunthu

kaŵiri pa tsiku, nthaŵi zonse.

15 Lev. 8.1-36 Ndi Mose amene adapatula Aroni

namdzoza ndi mafuta odalitsidwa.

Chimenechi chinali chipangano chosatha kwa iye

ndiponso kwa ana ake mpaka kutha kwa mlengalenga,

chakuti iye atsogolere chipembedzo ndi kukhala

wansembe ndipo azidalitsa anthu m'dzina la Mulungu.

16Adamsankhula pakati pa anthu onse

kuti azipereka kwa Ambuye nsembe zopsereza,

za lubani ndi zonunkhira ngati chikumbutso,

kutinso azipepesera anthu machimo ao.

17Adamsungiza Malamulo ake ndi udindo woweruza

potsata Malamulo,

kuti aziphunzitsa Yakobe za chipangano chake

kuti azimfotokozera bwino Israele Malamulo ake.

18 Num. 16.1-35 Anthu ena osakhala a m'banja lake adamuukira

ndi kumchitira chiwembu m'chipululu.

Ameneŵa anali aŵa: Datani, Abiramu ndi anzao,

ndiponso Kora ndi gulu lake,

ali ndi ukali waukulu.

19Ambuye adaziwona zimenezi ndipo adaipidwa nazo.

Ali ndi ukali woyaka adaŵaononga,

ndipo adaŵachita zoopsa pakuŵatentha ndi moto.

20Tsono adaonjezeranso Aroni zaulemu zina,

adafuna kuti choloŵa chake chikhale ichi:

adampatsa zipatso zoyamba kucha,

kuti azikhala ndi chakudya chambiri.

21Choncho iwo amadyapo nsembe zopereka kwa Ambuye,

zimene adaapatsa Aroni ndi adzukulu ake.

22 Num. 18.20; Deut. 12.12 Koma Ambuye sadapatse Aroni dziko lakelake

ngati anthu ena.

Iye yekha analibe chigawo chake pakati pa anthu,

poti Ambuye ndiwo anali chigawo chake ndi

choloŵa chake.

Finehasi

23 Num. 25.7-13 Finehasi, mwana wa Eleazara, anali wachitatu potchuka,

chifukwa cha changu chake pa za kupembedza Mulungu,

ndiponso chifukwa anali ndi mtima wolimba ndi

wosafookera pamene anthu ena adaapanduka.

Potero adapepesera Aisraele machimo ao.

24Nchifukwa chake Ambuye adachita naye

chipangano chamtendere.

Adampatsa ulamuliro pa Nyumba ya Mulungu ndi

pa mpingo wake.

Adampatsanso iyeyo ndi adzukulu ake ukulu

wa unsembe mpaka muyaya.

25Kunalinso chipangano ndi Davide, mwana wa

Yese, wa fuko la Yuda,

kuti odzaloŵa ufumu wake ndi mmodzi mwa

ana ake okha.

Koma unsembe wa Aroni unali wopita kwa

zidzukulu zake zonse.

26Mulungu akupatseni mtima wanzeru

kuti muweruze anthu ake mwachilungamo

kuti zonse zisaleke kuŵayendera bwino,

ndipo ulemerero wao ufikire ku mibadwo yonse

yakutsogolo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help