1Mfumu ikusangalala
chifukwa mwaipatsa mphamvu, Inu Chauta,
ikukondwa kwambiri
chifukwa mwaipambanitsa ndinu.
2Mwaipatsa zimene mtima wake umakhumba,
simudaimane zimene pakamwa pake padapempha.
3Mumafika kwa mfumuyo ndi madalitso okoma kwambiri.
Mwaiveka chipewa chaufumu chagolide pamutu.
4Iyo idakupemphani moyo,
ndipo Inu mudaipatsa moyo wautali, wamuyaya.
5Ulemerero wake ndi waukulu
chifukwa mwaipambanitsa ndinu.
Mwaipatsa ufumu waukulu ndi waulemu.
6Zoonadi, mwaisandutsa yodala kopambana mpaka muyaya.
Mwaisangalatsa ndi chimwemwe, chifukwa muli nayo.
7Paja mfumuyo imakhulupirira Chauta,
ndipo siidzagwedezeka
chifukwa cha chikondi chosasinthika cha Wopambanazonse.
8Idzagonjetsa adani ake onse.
Dzanja lake lamphamvu lidzakantha onse odana nayo.
9Ikangotulukira, idzaŵaononga
monga m'mene ng'anjo yamoto imaonongera.
Chauta adzaŵatha phu, chifukwa cha kukwiya nawo,
ndipo iwo adzanyeka ndi moto kuchita kuti psiti.
10Mfumuyo idzaononga ana ao pa dziko lapansi,
zidzukulu zao zidzatha pakati pa anthu.
11Akafuna kuti aichite choipa ndi kuipweteka,
adzalephereratu,
12pakuti idzaŵapirikitsa
potendekera nkhope zao ndi mauta ake.
13Mutamandike, Inu Chauta,
chifukwa cha kupambana kwanu.
Tidzaimba ndi kuyamika mphamvu zanu zazikulu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.