1Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mloŵachuma akali wamng'ono sasiyana ndi kapolo, ngakhale iyeyo ndi mwini chuma chonsecho.
2Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso akapitao oyang'anira chuma chake, mpaka nthaŵi imene bambo wake adakhazikitsa.
3Chimodzimodzinso ifeyo, pamene tinali ana, tinali akapolo a miyambo yapansipano.
4Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose.
5Aro. 8.15-17Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu.
6 2Es. 10.7 Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”
7Motero sindiwenso kapolo ai, koma mwana. Ndipo popeza kuti ndiwe mwana wake, Mulungu adakusandutsanso mloŵachuma wake.
Paulo adera nkhaŵa Agalatiya8Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse.
9Koma tsopano mukumdziŵa Mulungu, makamaka ndinene kuti Mulungu ndiye akudziŵa inu. Nanga bwanji mukubwereranso ku miyambo yachabe ndi yopanda phindu ija? Bwanji mukufuna kukhalanso akapolo ake?
10Mumasunga masiku, miyezi, nyengo ndi zaka.
11Ndikuwopa kuti mwinatu ntchito zanga zonse pakati panu ndidazigwira pachabe.
12Ndikukupemphani abale, musanduke ngati ine, pakuti inenso ndidasanduka ngati inu nomwe. Simudandilakwire konse.
13Monga mukudziŵa, pamene ndidayamba kukulalikirani Uthenga Wabwino, ndinkadwala.
14Ngakhale matendawo anali ngati mayeso kwa inu, komabe simudandinyoze kapena kunyansidwa nane. Kwenikweni mudandilandira ngati mngelo wa Mulungu, kapenanso ngati Khristu Yesu mwini.
15Nanga chimwemwe chanu chija chili kuti tsopano? Ndikukuchitirani umboni kuti nthaŵi imene ija, kukadatheka, mukadakolowola maso anu nkundipatsa ineyo.
16Monga ndasanduka mdani wanu popeza kuti ndakuuzani zoona?
17Anthu amene aja akuchita changu kwambiri pothandiza inu kuti akukopeni, koma changu chaocho sichili chabwino ai. Amangofuna kukupatutsani kuti muzichita changu pakuŵathandiza iwowo.
18Kwabwino nkumachita changu pa chinthu chabwino masiku onse, osati pokhapokha pamene ndili pamodzi nanu.
19Inu ana anga, monga mkazi amamva zoŵaŵa pochira, inenso ndikumva zoŵaŵa chifukwa cha inu mpaka moyo wa Khristu ukhazikike mwa inu.
20Ndikadakonda nditakhala nanu tsopano. Apo kapena ndikadasintha mau anga, chifukwa mwandithetsa nzeru.
Chitsanzo cha Hagara ndi Sara21Inu ofuna kukhala akapolo a Malamulo, tandiwuzani. Kodi simukumvetsa zimene Malamulowo akunena?
22Gen. 16.15; Gen. 21.2 Paja Malembo akuti, Abrahamu anali ndi ana aamuna aŵiri: wina mai wake anali kapolo, winayo mai wake anali mfulu.
23Mwana amene mai wake anali kapolo uja, adabadwa monga momwe amabadwira ana onse. Koma mwana wina uja, amene mai wake anali mfulu, adabadwa chifukwa cha lonjezo la Mulungu.
24Zimenezi zili ngati fanizo. Akazi aŵiri aja akufanizira zipangano ziŵiri. Mmodzi (Hagara uja), ndi wochokera ku phiri la Sinai, ndipo ana ake amakhala akapolo.
25Hagarayo akufanizira phiri la Sinai la m'dziko la Arabiya, lofanizira Yerusalemu walero, amene ali m'ukapolo pamodzi ndi anthu ake onse.
262Es. 2.2; 10.7Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mai wathu.
27Yes. 54.1 Paja Malembo akuti,
“Sangalala iwe chumba chosabala ana,
imba nthungululu, fuula mokondwera,
iwe amene sunamvepo zoŵaŵa za kubala.
Ana a mkazi wosiyidwa ndi ochuluka
koposa ana a mkazi amene ali naye mwamuna.”
28Tsono inu abale, ndinu ana a Mulungu chifukwa cha lonjezo lake, monga Isaki.
29Gen. 21.9 Nthaŵi imeneyo mwana uja amene adaabadwa monga momwe amabadwira ana onseyu, ankasautsa mwana winayo wobadwa mwa mphamvu za Mzimu Woyera, ndipo mpaka tsopano zili chimodzimodzi.
30Gen. 21.10 Nanga Malembo akuti bwanji? Akuti, “Mpirikitseni kapoloyu pamodzi ndi mwana wake. Mwana wa kapolo asadzakhale konse mloŵachuma pamodzi ndi mwana wa mfulu.”
31Nchifukwa chake, abale, ife sindife ana a kapolo, ndife ana a mfulu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.