Yes. 46 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kupasuka kwa Babiloni ndi mafano ake

1Nayu Beli wapendekeka, Nebo waŵerama!

Mafano ameneŵa a Babiloni aŵaika pa abulu ndi ng'ombe.

Zinthu zimene kale munkanyamula ndinu,

tsopano mukuziika ngati katundu

wolemera pamsana pa nyama zotopa.

2Nyamazo zikuŵerama ndi kufuna kugwa naye katunduyo,

sizikutha kumpulumutsa.

Izo zomwe zikupita ku ukapolo.

3“Mundimvere, inu zidzukulu za Yakobe,

inu nonse otsala a m'nyumba ya Israele.

Ndakhala ndikukusamalani chibadwire chanu,

ndidakunyamulani kuyambira m'mimba mwa amai anu.

4Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja,

mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu.

Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani.

Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.

5“Kodi Ine mungandifanizire ndi yani,

kapena kundilinganiza ndi yani?

Kodi mungandiyerekeze ndi yani,

kuti Ine ndi iyeyo tikhale ofanana?

6Anthu ena amatsekula zikwama zao

namatulutsamo golide,

ndipo amayesa siliva pa masikelo.

Amalemba mmisiri wosula,

ndipo iye amaŵapangira milungu.

Kenaka iwowo amagwada pansi,

namaipembedza milunguyo.

7Amainyamula pa mapewa ao, naisenza.

Amaikhazika pamalo pake nikhala pomwepo,

ndipo singathe kusuntha pamalo pakepo.

Wina aliyense akapemphera kwa milunguyo, siyankha,

kapena kumpulumutsa ku mavuto ake.

8“Mukumbukire zimenezi ndi kuganizapo,

muzilingalire, inu ochimwanu.

9Mukumbukire zamakedzana zija.

Mulungu ndine ndekha, palibenso wina ai.

Ndithudi, Mulungu ndine,

ndipo palibenso wina wonga Ine.

10Ndidaneneratu zakumathero kuchokera pa chiyambi pomwe.

Kuyambira kalekale ndidaloseratu

zimene zidakali zosachitikabe.

Ndidaanena kuti, ‘Maganizo anga sadzalephera,

ndidzachitadi zonse zimene ndidafuna kuchita.’

11Ndikuitana chiwombankhanga kuchokera kuvuma,

ndiye kuti munthu wofumira ku dziko lakutali,

amene adzapherezetsa zimene ndikufuna kuchita.

Zimene ndalankhula, ndidzazifitsa,

zimene ndafuna kuchita ndidzazichitadi.

12“Mundimvere, inu ouma mitunu,

inu amene muli kutali ndi chipulumutso.

13Tsiku la chipulumutso ndalisendeza pafupi,

layandikira, sindidzachedwa kukupulumutsani.

Ndidzapulumutsa Ziyoni,

ndipo ndidzapatsa dziko la Israele ulemerero.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help