Yer. 21 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aneneratu za kuwonongedwa kwa Yerusalemu

1Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, adatuma Pasuri mwana wa Malakiya, ndiponso wansembe Zefaniya mwana wa Maseiya, naŵauza kuti,

22Maf. 25.1-11; 2Mbi. 36.17-21“Pitani kwa Yeremiya mukampemphe kuti atinenere kwa Chauta, popeza kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni akufuna kutithira nkhondo. Mwina mwake Chauta nkutichitira zodabwitsa, kuti Nebukadinezara achoke kwathu kuno.”

3Koma otumidwa aja atafika, Yeremiya adaŵauza kuti,

4“Mukamuuze Zedekiya kuti Chauta, Mulungu wa Israele akuti, ‘Ndidzakulandani zida zankhondo zimene zili m'manja mwanuzo, zimene mukumenya nazo nkhondo ndi mfumu ya ku Babiloni ndi ankhondo ake amene akuzingani ndi zithando zankhondo. Ndidzabwera nazo ndi kuziika m'kati mwa mzinda uno.

5Ineyo mwiniwakene ndi mkono wanga wamphamvu, ndidzamenyana nanu nkhondo inuyo, ndili wopsa mtima, wokalipa ndi wokwiya.

6Ndidzakantha okhala mumzindamu ndi ziŵeto zomwe, ndipo zonse zidzafa ndi mliri woopsa.

7Pambuyo pake ndidzapititsa ku ukapolo Zedekiya mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, ndi anthu otsala mumzindamu opulumuka ku mliri, ku njala ndi ku nkhondo. Ndidzaŵapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndiponso kwa adani ao amene akufuna kuŵapha. Adzaŵaphadi ndi lupanga, sadzaŵamvera chisoni kapena chifundo.’ ”

8Chauta akunena kuti, “Anthu ameneŵa udzaŵauzenso kuti asankhulepo: kodi afuna moyo kapena imfa?

9Aliyense wotsala mu mzinda uno adzafa ndi nkhondo, njala kapena mliri. Koma aliyense amene adzadzipereka kwa Ababiloni amene akuzingani ndi zithando zankhondo aja, ameneyo adzakhala ndi moyo, adzapulumuka.

10Mzinda umenewu ndatsimikiza kuti ndidzauchita zoipa osati zabwino ai. Udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babiloni ndipo iyeyo adzautentha ndi moto.”

Chilango cha banja la mfumu

11“Tsono banja laufumu la ku Yuda uliwuze kuti, ‘Imvani mau a Chauta.

12Inu a m'banja la Davide, Chauta akunena kuti:

“ ‘Muziweruza motsata chilungamo m'maŵa mulimonse,

ndipo muzipulumutsa kwa anthu ozunza,

aliyense amene katundu wake wabedwa,

kuwopa kuti mkwiyo wanga ungayake nkukhala wosazimika,

chifukwa cha machimo anu.

13“ ‘Ndikukuimbani mlandu, inu anthu okhala m'chigwa

inu okhala ngati thanthwe lapachidikha,’ ”

akutero Chauta.

“Inu amene mumati, ‘Ndani angatithire nkhondo?

Ndani angathe kuloŵa m'malinga mwathu?’

14Ndidzakulangani potsata ntchito zanu.

Ndidzatentha nkhalango yanu,

moto udzapsereza zonse zimene zakuzungulirani,”

akuterotu Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help