1Patapita nthaŵi pang'ono, Lisiyasi, nkhoswe ya mfumu ndiponso wachibale wake, amene anali nduna yaikulu ya boma, adavutika nazo zimene zidachitikazo.
2Adasonkhanitsa anthu 80,000 pamodzi ndi okwera pa akavalo ake onse, napita kukachita nkhondo ndi Ayuda. Ankaganiza zosandutsa mzinda wa Yerusalemu kuti ukhale mzinda Wachigriki.
3Ankati adzakhometse msonkho Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, monga m'mene ankachitira ndi malo achipembedzo a anthu akunja. Ankafunanso kuti chaka chilichonse azidzagulitsa ukulu wa mkulu wa ansembe.
4Sankalabadako za mphamvu za Mulungu, koma ankangonyadira zikwi ndi zikwi za ankhondo ake, ndipo zikwi za ankhondo ake okwera pa akavalo, ndi njovu zake makumi asanu ndi atatu.
5Tsono adaloŵa ku Yudeya, nakafika ku Betizure, mzinda wankhondo wotalikana ndi Yerusalemu ngati makilomita makumi atatu, nauzinga.
6Yudasi Makabeo ndi anthu ake atamva kuti Lisiyasi akuzinga mizinda yao yankhondo, adapemphera kwa Ambuye, akudandaula ndi kulira, kuti atume mngelo wabwino wodzapulumutsa Israele.
7Makabeo ndiye amene adayamba kutenga zida zake, nalangiza anzake kuti asaope ngakhale kutaya moyo wao pamodzi naye, kuti potero athandize abale ao. Pamenepo onse adathamangirako pamodzi.
8Asanapite kutali ndi Yerusalemu, wina wokwera pa kavalo adaŵaonekera atavala nsalu zoyera, akuŵatsogolera, zida zagolide zili m'manja.
9Tsono onsewo pamodzi adayamika Mulungu wachifundo; adalimba mtima, nakonzekera kumenya nkhondo, osati ndi anthu okha, koma ndi zilombo zaukali zomwe, ngakhalenso malinga achitsulo.
10Adasendera ali m'mizere yankhondo ali ndi woŵathandiza wakumwamba, chifukwa Ambuye adaaŵachitira chifundo.
11Adalumphira adani ao ngati mikango, napha anthu 11,000, okwera pa akavalo 1,600, ena onse nkuthaŵa,
12Ambiri mwa iwo adathaŵa ali olasidwa atataya zida zao. Lisiyasi nayenso adapulumutsa moyo wake pakuthaŵa monyozeka.
Lisiyasi apangana za mtendere ndi Ayuda13Koma poti Lisiyasiyo sanali wopusa, adayamba kulingalira za tsoka limene lidamgwera, nkumvetsa kuti Ayuda analidi anthu osagonjetseka, chifukwa Mulungu Wamphamvu ndiye ankaŵathandiza. Tsono adaŵatumira amithenga,
14kukaŵachonderera kuti avomerezane za kugwirizananso mwachilungamo. Ndipo adalonjeza kuti iye adzachonderera mfumu kuti ikhale bwenzi lao.
15Makabeo atalingalira za zimene zingaŵakhalire bwino anthu ake, adavomera mau onse a Lisiyasi. Nayonso mfumu idavomera zonse zimene Makabeo adalembera Lisiyasi.
Kalata ya Lisiyasi kwa Ayuda16Kalata imene Lisiyasi adalembera Ayuda inali yotere: “Lisiyasi akupereka moni kwa gulu lonse la Ayuda!
17Yohane ndi Abisalomu amene mudaŵatuma kuno adandipatsa kalata yanu, nandipempha kuti ndikuyankheni.
18Zonse zoyenera kudziŵitsa mfumu ndidaidziŵitsa, ndipo idavomera zonse zimene zingatheke.
19Mukalimbika kukhala okhulupirika ku boma, ineyo ndidzachita zotheka kukuthandizani kuti zanu zikuyendereni bwino.
20Tsono ndalamula amithenga anga ndi anu omwe kuti akambe nanu pa zonse zimene tagwirizana.
21Tsalani bwino. Chaka cha 148 tsiku la 24 la mwezi wa Dioskore.”
Kalata ya Mfumu Antioko kwa Lisiyasi22Kalata ya mfumu inali yotere: “Mfumu Antioko akupereka moni kwa mbale wake Lisiyasi!
23Popeza kuti tsopano atate athu adapita kwa milungu yao, ife timafuna kuti anthu a m'dziko mwathu azigwira ntchito zao mosavutika.
24Tidamva zoti Ayuda safuna kutsata Chigriki, monga m'mene atate athu ankafunira, koma akufunitsitsa kusunga miyambo yao ndi mazoloŵero ao.
25Ndiye popeza kuti inenso ndikufuna kuti fuko lao lisavutikenso, ndikulamula kuti uŵabwezere Nyumba yao ya Mulungu, ndipo kuti uŵalole kumatsata miyambo ya makolo ao.
26Nchifukwa chake ndi bwino kuti uŵadziŵitse zimenezi ndi kuŵatsimikizira zoti ndikuchita nawo ubwenzi, kuti choncho adziŵe zofuna zathu ndi kutikhulupirira, ndipo kuti azikhala akuyendetsa zinthu zao mokondwa.”
Kalata ya Mfumu Antioko kwa Ayuda27Kalata ya mfumu kwa Ayuda inali yotere: “Ine, Mfumu Antioko, ndikupereka moni kwa akulu a Ayuda ndi kwa Ayuda ena onse.
28Ngati muli bwino, ndimo m'mene tikufunira ife. Ifenso tili bwino.
29Menelasi adatidziŵitsa zakuti mukufuna kubwerera kwanu ndi kumakasamalanso ntchito zanu.
30Tsono onse amene akufuna kubwerera kwao lisanafike tsiku la 30 mwezi wa Ksantiko, atha kupita mwamtendere popanda chovuta.
31Tikuloladi kuti Ayudanu muzidya chakudya chanu, ndipo kuti muzitsata malamulo anu, monga momwe munkachitira kale. Sipadzakhalanso Myuda ndi mmodzi yemwe amene ena adzamvute chifukwa cha cholakwa chimene adachichita mosadziŵa.
32Ndikutuma Menelasi kuti adzakulimbitseni mtima.
33Tsalani bwino. Chaka cha 148, tsiku la 15 la mwezi wa Ksantiko.”
Kalata ya Aroma kwa Ayuda34Aromanso adalembera Ayuda kalata yotere: “Kwinto Memiusi ndi Tito Maniusi, akazembe a ku Roma, akupereka moni kwa Ayuda.
35Zimene Lisiyasi, mbale wa mfumu, adakuuzani, ifenso tazilola zimenezo.
36Koma zina zimene adaganiza kuti nzoyenera kuzifotokozera kwa mfumu, mutaziganizira bwino eniakenu, mutitumizire uthenga mwamsanga, kuti tithe kukunenerani kwa mfumu, poti tikupita ku Antiokeya.
37Tsono mufulumire, tumizani anthu msanga, tidziŵe zimene mukufuna.
38Tsalani bwino. Chaka cha 150, tsiku la 15 la mwezi wa Ksantiko.”
Ayuda a ku Yopa aphedwaWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.