1Atalandira mauwo mfumu Dariusi adapanga lamulo ndipo kafukufuku adachitikadi ku Babiloni m'nyumba mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri zakale.
2Tsono ku Ekibatana, likulu la dziko la Mediya, kudapezeka mpukutu m'mene mudaalembedwa kuti, “Chikumbutso.” Mau ake anali aŵa:
3“Pa chaka choyamba cha ufumu wake, mfumu Kirusi adapereka lamulo lalikulu lonena za Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Adalamula kuti Nyumbayo imangidwenso, ngati malo otsirirako nsembe. Maziko ake ayalidwe mwamphamvu pomwe paja pali maziko ake akale. Muutali mwake idzakhale mamita 27, muufupi mwake idzakhalenso mamita 27.
4Mudzamange mizere itatu ya miyala yaikulu ndi mzere umodzi wa matabwa. Ndalama zake zolipirira ntchitoyo zichokere m'thumba lachifumu.
5Tsono ziŵiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara adaazitulutsa ku Yerusalemu kunka nazo ku Babiloni, zonsezo zibwezedwe, zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake m'Nyumba ya Mulunguyo.”
Mfumu Dariusi alamula kuti ntchito ipitirire6Tsono mfumu Dariusi adayankha motere: “Inu Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai pamodzi ndi anzanu, muchokeko kumeneko.
7Ntchito iyi yomanga Nyumba ya Mulungu muileke. Mlekeni bwanamkubwa wa ku dera la Yuda ndiponso atsogoleri akumeneko kuti amangenso Nyumba ya Mulunguyo pamalo pake ndithu.
8Kuwonjezera pamenepo, ndikupanga lamulo lonena za m'mene mudzaŵachitire atsogoleri a Ayudawo zothandiza pomanganso Nyumbayo. Anthuwo muŵalipire msanga kuchokera m'thumba lachifumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate.
9Ndipo zonse zofunikira, monga anaang'ombe, nkhosa zamphongo kapena anaankhosa, zoperekera nsembe zopsereza kwa Mulungu Wakumwamba, kapena tirigu, mchere, vinyo ndi mafuta, monga m'mene ansembe a ku Yerusalemu angafunire, muziŵapatsa zimenezo tsiku ndi tsiku osalephera.
10Zimenezi zichitike kuti azipereka nsembe za fungo lokomera Mulungu Wakumwamba, ndi kuti anthuwo apempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake.
11Ndikupanganso lamulo lakuti ngati wina aliyense asintha zimene ndalamulazi, ndiye kuti adzasololako mtanda wa nyumba yake nadzamkhomera pamenepo, ndipo nyumba yakeyo adzaisandutsa dzala.
12Mulungu amene adasankhula Yerusalemu kuti akhale malo ompembedzerako, achotse mfumu iliyonse kapena anthu amene adzayerekeze kusintha zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu yakumeneko. Ine Dariusi ndikuika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri.”
Kumaliza Nyumba ya Mulungu13Tsono potsata mau amene mfumu Dariusi adaalamula, Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, Setari-Bozenai ndi anzao adachita mosamala kwambiri zimene mfumu Dariusi adaalamula.
14Hag. 1.1; Zek. 1.1 Ndipo akulu a Ayuda adapititsa m'tsogolo ntchito yomanga ija. Iwo ankalimbikitsidwa ndi aneneri aja Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Adamaliza ntchito yao yomanga Nyumba, monga momwe Mulungu wa Israele adaalamulira, ndiponso potsata lamulo la Kirusi, la Dariusi, ndi la Arita-kisereksesi, mafumu a ku Persiya.
15Nyumbayo adaimaliza kumanga pa tsiku lachitatu la mwezi wa Adara, chaka chachisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa mfumu Dariusi.
Kupereka Nyumba ya Mulungu16Tsono Aisraele, ndiye kuti ansembe, Alevi ndi anthu ena onse amene anali atabwerako ku ukapolo, adachita chikondwerero cha kupereka Nyumba ya Mulungu mwachimwemwe.
17Pochita mwambo umenewo, anthuwo adapereka nsembe za ng'ombe zamphongo 100, nkhosa zamphongo 200, anaankhosa 400. Adaperekanso atonde khumi ndi aŵiri ngati nsembe yopepesera uchimo wa anthu onse, potsata chiŵerengero cha mafuko a Aisraele.
18Choncho adaŵakhazika ansembe ndi Alevi pa ntchito zao zotumikira Mulungu ku Yerusalemu, monga momwe zidalembedwera m'buku la Mose.
Kusunga Paska19 Eks. 12.1-20 Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba, obwerako ku ukapolo aja adachita Paska.
20Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa, tsono onsewo anali oyeradi. Choncho adapha mwanawankhosa wa Paska, kuphera onse amene adatuluka ku ukapolo, ansembe anzao ndi eniakewo.
21Nkhosa ya Paskayo adaidya Aisraele onse amene adatuluka ku ukapolo. Adadyakonso wina aliyense amene adaphatikana nawo, atadziyeretsa ku zonyansa za mitundu ina ya anthu akunja am'dzikomo, kuti apembedze Chauta, Mulungu wa Israele.
22Motero pa masiku asanu ndi aŵiri adasangalala pa chikondwerero cha buledi wosatupitsa. Zidatero chifukwa Chauta adaŵakondweretsa, ndipo adaatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya, kotero kuti idaŵakomera mtima niŵathandiza pa ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wake wa Aisraele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.