1Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri,
kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.
2Wolemera ndi wosauka akulingana,
pakuti onsewo adaŵalenga ndi Chauta.
3Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,
koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
4Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Chauta,
ndi chuma, ulemu ndi moyo.
5M'njira ya munthu wosalungama muli minga ndi misampha,
koma wodzisamala bwino adzazilewa zonsezo.
6 Mphu. 6.18 Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo,
ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
7Wolemera amalamulira wosauka,
ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womkongozayo.
8Amene amabzala kusalungama adzakolola mavuto,
ndipo ndodo ya ukali wake idzathyoka.
9Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa,
poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.
10Mukampirikitsa wonyoza, kukangana kudzatha,
ndipo ndeu ndi zonyoza zidzalekeka.
11Amene amakonda kukhala woyera mtima
ndi kulankhula zabwino,
adzakhala bwenzi la mfumu.
12Chauta amayang'anira bwino anthu odziŵa zinthu,
koma mau a anthu osakhulupirika, Iye amaŵalepheretsa.
13Waulesi amati, “Pali mkango pabwalopo!
Ndikaphedwa m'miseu.”
14Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lakuya.
Amene Chauta amamkwiyira adzagwamo.
15Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana,
koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.
16Amene amapondereza osauka
kuti aonjezere pa chuma chake,
kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha,
adzasanduka wosauka.
Malangizo a anthu anzeru.17Utchere khutu lako, umve mau a anthu anzeru,
uike mtima wako pa zophunzitsa zanga, kuti uzidziŵe.
18Chidzakhala chokondwetsa ukazisunga,
ndi kukhala wokonzeka kumazilankhula pa nthaŵi yake.
19Ndakudziŵitsa zimenezi lero
kuti makamaka iweyo uzikhulupirira Chauta.
20Kodi suja ndidakulembera malangizo makumi atatu,
okuchenjeza ndi okupatsa nzeru,
21malangizo okudziŵitsa zolungama ndi zoona,
kuti ukaŵayankhe zoona amene adakutuma?
22Mmphaŵi usamubere, chifukwa choti iyeyo ndi wosauka.
Anthu ozunzika usaŵapondereze pa bwalo la milandu.
23Pakuti Chauta adzaŵateteza pa mlandu wao,
ndipo adzaŵalanda moyo amene amalanda zinthu zao.
24Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga,
ndipo usamayenda naye munthu waukali,
25kuwopa kuti ungadzaphunzireko mayendedwe ake,
ndi kukodwa mu msampha.
26Usakhale mmodzi mwa anthu opereka zikole,
amene amasanduka chigwiriro cha ngongole.
27Ngati ulephera kulipira,
adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.
28Usasendeze malire akalekale
amene makolo ako adaŵaika.
29Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso?
Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.