Yob. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsono Yobe adayankha kuti,

2“Kodi mudzakhala mukundizunzabe mpaka liti?

Chifukwa chiyani mukundilasa ndi mau anu?

3Mwakhala mukundinyoza kambirimbiri,

Bwanji osachita manyazi kuti mukundisautsa?

4Ngakhale zitakhala zoona kuti ndachimwa,

kuchimwakotu nkwanga.

5Ndithudi, mukuganiza kuti mukundipambana.

Mukuti mavuto angaŵa akusonyeza kuchimwa kwanga.

6Koma tsono mudziwe kuti

Mulungu ndiye wandichita zimenezi,

ndiye amene wanditchera msampha umenewu.

7Ndithu, ndimafuula kuti, ‘Mayo, akundizunza ine!’

Koma palibe wondiyankha. Ndimapempha chithandizo,

koma palibe wondichitira zolungama.

8“Mulungu wanditsekera njira,

kotero kuti sindingathe kubzola.

Njira yangayo waiphimba ndi mdima.

9Iye wandilanda ulemerero wanga,

wandivula chisoti chaulemu.

10Wandiphwanyaphwanya mbali zonse, ndipo ndatheratu.

Wandilanda chikhulupiriro changa,

monga momwe amazulira mtengo.

11Mulungu wandikwiyira,

akundiyesa ngati mdani wake.

12Watumiza ankhondo ake ochuluka kuti adzalimbane nane.

Akonzekeratu zodzandithira nkhondo

pafupi ndi nyumba yanga.

13“Mulungu waumiriza abale anga kuti andikane.

Wasandutsa odziŵana nane kuti akhale achilendo kwa ine.

14Achibale anga andithaŵa.

Abwenzi anga anditaya.

15Anthu odzacheza kunyumba kwanga andiiŵala,

Antchito anga nawonso sakundilemekeza,

ndasanduka ngati wakudza m'maso mwao.

16Ndikaitana wantchito, sandiyankha,

ndimachita kupemba kuti andichitire kanthu.

17Ngakhale mkazi wanga yemwe amaipidwa nane.

Ndine chinthu chonyansa kwa abale anga a mimba imodzi.

18Ngakhale ana omwe amandinyoza,

ndikamayenda amandinyodola.

19 Mphu. 6.8 Abwenzi anga onse apamtima amanyansidwa nane,

amene ndinkaŵakonda kwambiri andiwukira.

20“Ndangoti gwa kuwonda,

moyo wanga wapulumukira pang'onong'ono.

21Mvereni chifundo, chonde mvereni chifundo,

inu abwenzi anganu, poti dzanja la Mulungu landikantha.

22Chifukwa chiyani mukundilondola ndinu ngati Mulungu?

Kodi simudandizunze kokwanira?

23“Ha, achikhala ena adaakumbukira mau anga!

Ha, achikhala mauwo adaalembedwa m'buku!

24Achikhala mauwo adaazokotedwa

pa thanthwe ndi chitsulo,

ndi kuthirapo mtovu kuti akhale mpaka muyaya!

25“Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo,

ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.

26Khungu langa litatha nkuwonongeka,

m'thupi langa lomweli ndidzamuwona Mulungu.

27Ine ndemwe ndidzamuwona, osati winanso ai.

Ndidzamuwona ndi maso angaŵa.

Mtima wanga ukulifunitsitsa tsikulo.

28Koma inu mukuti,

‘Ha, tingamzunze bwanji,

popeza kuti zovuta zonsezi zaoneka

chifukwa cha iye yemweyo?’

29Inu muwope chilango,

chifukwa ukali wa Mulungu umalangadi mosalephera.

Motero mudzadziŵa kuti chiweruzo chilipo ndithu.”

Zofari

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help