1Zitapita zaka zambiri, pamene Arita-kisereksesi anali mfumu ya ku Persiya, panali wansembe wina dzina lake Ezara. Iyeyu anali mdzukulu wa Aaroni, mkulu wa ansembe woyamba wa Israele. Makolo ake anali aŵa: Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
2mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi,
3mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Meraiyoti,
4mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki,
5mwana wa Abisuwa, mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni mkulu wa ansembe uja.
6Ezarayu anali wophunzira kwambiri wa za Malamulo amene Chauta, Mulungu wa Israele, adaapereka kwa Mose. Popeza kuti Chauta, Mulungu wake, adaamdalitsa Ezarayo, mfumu Arita-kisereksesi ankamupatsa zonse zimene ankapempha.
7Tsono chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Arita-kisereksesi, Ezarayo adanyamuka kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Aisraele ena, ndiye kuti ansembe ndi Alevi, oimba nyimbo, alonda ndiponso anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu.
8Ezarayo adafika ku Yerusalemu pa mwezi wachisanu wa chaka chachisanu ndi chiŵiri cha mfumu.
9Adanyamuka ku Babiloni pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, nafika ku Yerusalemu ndi chithandizo cha Mulungu wake.
10Pakuti Ezara adaaika mtima wake pa kuphunzira Malamulo a Chauta ndi kuŵatsata. Ankafunitsitsanso kuphunzitsa Aisraele malamulo ndi malangizo a Chauta.
Kalata ya mfumu Arita-kisereksesi11Nayi kalata imene mfumu Arita-kisereksesi adapatsa wansembe Ezara, mlembi uja wophunzira kwambiri malamulo ndi malangizo amene Chauta adaapatsa Aisraele:
12“Ndine, Arita-kisereksesi, mfumu ya mafumu, ndikulembera iwe Ezara, wansembe ndi mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba.
13Tsopano ndikupanga lamulo lakuti Mwisraele aliyense kapena ansembe ao, kapena Alevi okhala m'dziko mwanga, amene afuna kuti apite ku Yerusalemu mwaufulu, apite nawe.
14Pakuti ine mfumu pamodzi ndi aphungu anga asanu ndi aŵiri tikukutuma kuti ukafunsitse za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu, kuti ukaone m'mene anthu akutsatira malamulo amene Mulungu wako adaŵapereka kwa iwe.
15Utenge siliva ndi golide zimene ine mfumu ndi aphungu anga tapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Aisraele, amene Nyumba yake ili ku Yerusalemu.
16Utengenso siliva ndi golide yense amene mumpeze m'dziko lonse la Babiloni, ndiponso zopereka zimene anthu ndi ansembe adzapereka mwaufulu, mosakakamiza, kuperekera Nyumba ya Mulungu wao ya ku Yerusalemu.
17Tsono ndi ndalama zimenezi, mudzagule mwachangu ng'ombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zake zaufa ndiponso nsembe zake zazakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa la ku Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu.
18Ndalama zotsala muzigwiritse ntchito monga momwe inuyo ndi abale anu mungafunire malinga nkufuna kwa Mulungu wanu.
19Ziŵiya zimene akupatsanizi kuti muzitumikira nazo m'Nyumba ya Mulungu wanu, mukazipereke kwa Mulungu ku Yerusalemu.
20Ndipo china chilichonse chimene chingafunikire m'Nyumba ya Mulungu wanu, chimene mudzapeze danga loperekera, ndalama zake zogulira zidzatuluke m'thumba la chuma cha mfumu.
21“Tsono ine, mfumu Arita-kisereksesi, ndikulamula onse osunga chuma m'dera la Patsidya pa Yufurate, kuti zonse zimene wansembe Ezara, wophunzira wa malamulo a Mulungu Wakumwamba, adzapemphe kwa inu, zichitike mwachangu.
22Ngakhale afunika makilogaramu 3,400 a siliva, makilogaramu 10,000 a tirigu, malitara 2,000 a vinyo, ndi malitara 2,000 a mafuta, ndiponso mchere wochuluka chotani, zonsezo muzipereke monga m'mene zingafunikire.
23Zonse zimene Mulungu Wakumwamba alamule, zichitike mwachangu ku Nyumba ya Mulungu Wakumwamba, kuwopa kuti mkwiyo wake ungayakire mfumu ndi dziko lake ndi ana ake.
24Tikukudziŵitsaninso kuti kudzakhala kosaloledwa kumkhometsa msonkho uliwonse wansembe aliyense, Mlevi aliyense, woimba aliyense, mlonda kapena wantchito aliyense wa ku Nyumba ya Mulungu.
25“Ndiye iwe Ezara, potsata nzeru zimene Mulungu wako adakupatsazi, usankhe oyendetsa zinthu ndi aweruzi oti azilamulira anthu onse okhala m'dera la Patsidya pa Yufurate, anthu ake otsata malamulo a Mulungu wako. Ndipo anthu osadziŵa malamulowo uzidzaŵaphunzitsa.
26Aliyense amene sadzamvera malamulo a Mulungu wako kapena malamulo a mfumu, alangidwe kolimba, kapena kuphedwa, kapena kuchotsedwa m'dzikolo, kapena kumlanda katundu wake, kapena kumponya m'ndende.”
Ezara atamanda Mulungu27Ezara adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa makolo athu, amene adaika nzeru zotere mu mtima wa mfumu, kuti apereke ulemu ku Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu.
28Ndiye amenenso adaonetsa chikondi chake chosasinthika pa ine kuti mfumu ndi aphungu ake ndi atsogoleri ake amphamvu andikomere mtima. Ndidalimba mtima popeza kuti Chauta Mulungu wanga anali nane, choncho ndidasonkhanitsa atsogoleri ambiri a Aisraele kuti apite nane pamodzi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.