1Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona.
2Uuze amuna achikulire kuti azikhala osaledzera, ochita zachiukulu, a maganizo anzeru, olimba pa chikhulupiriro, pa chikondi ndi pa kusatepatepa.
3Chimodzimodzinso azimai achikulire, uŵauze kuti azikhala ndi makhalidwe oyenera azimai oyera mtima. Asakhale osinjirira anzao kapena akapolo a zoledzeretsa. Akhale alangizi abwino,
4kuti choncho athe kuphunzitsa azimai achitsikana kukonda amuna ao ndi ana ao.
5Aŵaphunzitse kukhala a maganizo anzeru, opanda dama, osamala bwino zapabanja, ndi omvera amuna ao. Pamenepo anthu sanganyoze mau a Mulungu.
6Momwemonso amuna achinyamata uŵauzitse kuti akhale odzigwira.
7Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu.
8Mau ako akhale oona, kuti anthu asadzathe kuŵatsutsa. Motero wotsutsana nawe adzachita manyazi, atasoŵa kalikonse koipa kuti atinenere.
9Antchito azimvera ambuye ao, aziŵakondweretsa pa zonse. Asamatsutsana nawo
10kapena kumaŵabera, koma makamaka adziwonetse kuti ngokhulupirika pa zonse zabwino. Motero pa zochita zao zonse adzaonetsa kukoma kwake kwa zophunzitsa zonena za Mulungu, Mpulumutsi wathu.
11Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse.
12Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.
13Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake.
14Mas. 130.8; Eks. 19.5; Deut. 4.20; 7.6; 14.2; 1Pet. 2.9Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.
15Zimenezi ndizo zimene uyenera kumaphunzitsa. Uziŵalimbikitsa anthu, ndi kuŵadzudzula komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ai.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.