Lev. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyama ndi mbalame zololedwa kuzidya(Deut. 14.3-21)

1Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,

2“Auzeni Aisraele kuti nyama zimene angathe kudya pakati pa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi izi:

3‘Nyama zonse zokhala ndi ziboda zogaŵikana, ndi zobzikula, angathe kudya zimenezo.

4Koma pakuti pa nyama zobzikula kapena za ziboda zogaŵikanazo, asadye izi: ngamira: imeneyi njonyansa kwa inu pa zachipembedzo, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana.

5Mbira: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana.

6Kalulu: ameneyu ndi wonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale amabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana.

7Nkhumba: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale ziboda zake nzogaŵikana ndipo mapazi ake ngogaŵikananso, koma siibzikula.

8Nyama ya zoŵeta zimenezo musamadye, ndipo zikafa musazikhudze. Zimenezi nzonyansa kwa inu.’

9“Zamoyo zam'madzi zimene mutha kudya ndi izi: zonse zam'madzi zimene zili ndi zilimba ndi mamba, mungathe kudya, ngakhale zikhale zam'nyanja kapena zam'mitsinje.

10Koma zamoyo zonse zam'nyanja kapena zam'mitsinje zopanda zilimba ndi mamba, tizilombo tonse tam'madzi ndi zamoyo zonse zopezeka m'menemo, nzonyansa kwa inu.

11Zimenezo zikhale zonyansa kwa inu, ndipo musadye. Zikafa zikhalebe zonyansa kwa inu.

12Zamoyo zonse zam'madzi zopanda zilimba ndi mamba, nzonyansa kwa inu.

13“Ndipo mbalame zimene muyenera kuziyesa zonyansa, zoti simuyenera kudya, popeza kuti nzonyansa kwa inu, ndi izi: mphungu, nkhwazi, ndi muimba,

14nankapakapa, akamtema a mitundu yonse,

15akhungubwi a mitundu yonse

16nthiŵatiŵa, chipudo, kakoŵa, akabaŵi a mitundu yonse,

17kadzidzi, chiswankhono ndi mantchichi,

18tsekwe, vuwo, dembo,

19indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.

20“Zonse za miyendo inai, zouluka, nzonyansa kwa inu.

21Komabe pakati pa zouluka zonse za miyendo inai, mungathe kudya zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira pa dothi.

22Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse.

23Koma zamapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inai nzonyansa kwa inu.

24“Tsono zimenezi mukazikhudza, zidzakuipitsani, ndipo aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.

25Aliyense akanyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo, achape zovala zake, komabe akhala woipitsidwa mpaka madzulo.

26Nyama iliyonse yokhala ndi ziboda zogaŵikana, koma mapazi ake osagaŵikana, kapenanso yosabzikula, njonyansa imeneyo kwa inu, ndipo aliyense woikhudza, adzakhala woipitsidwa.

27Pakati pa nyama zonse za miyendo inai, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo ku mapazi, nzonyansa kwa inu, ndipo aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.

28Ndipo munthu amene anyamula nyamazi zitafa, achape zovala zake, komabe akhala woipitsidwa mpaka madzulo. Zimenezi nzonyansa kwa inu.

29“Tsono zokwaŵa zonse zimene zili zonyansa kwa inu ndi izi: likongwe, mbeŵa, ng'azi za mitundu yonse,

30gondwa, mng'anzi, buluzi dududu ndi birimankhwe.

31Zimenezi nzonyansa kwa inu pakati pa zokwaŵa zonse. Munthu aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.

32Ndipo nyama zimenezi zikagwera pa chinthu chilichonse zitafa, chinthucho chidzakhala chonyansa, chingakhale chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa, kapena chiguduli, kapena chipangizo chilichonse chogwiritsa ntchito iliyonse. Chinthucho achiviike m'madzi, koma chidzakhalabe chonyansa mpaka madzulo. Pambuyo pake chidzakhala chabwino.

33Tsono china chilichonse mwa zimenezi chikagwera m'mbiya yadothi, zonse za m'menemozo zidzakhala zonyansa, ndipo mbiyayo muiphwanye.

34Madzi am'mbiyamo akathira pa chakudya chilichonse, chakudyacho chidzakhala chonyansa. Chakumwa chilichonse cha m'mbiya ya mtundu umenewo chidzakhala chonyansa.

35Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse, chinthucho chidzakhala chonyansa, kaya ndi uvuni kapena chitofu, zonsezo aziphwanye, poti nzonyansa zimenezo, ndipo zidzakhala zonyansa kwa inu.

36Koma kasupe kapena chitsime chamadzi zidzakhalabe zabwino, ngakhale kuti chilichonse chokhudza nyama chidzakhala chonyansa.

37Chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo chikagwera pa mbeu zimene anthu akuti abzale, mbeu zimenezo zikhalabe zabwino.

38Koma mbeuzo zikakhala zonyowa ndi madzi, ndipo chiwalo chilichonse cha nyama zakufa chigwera pa mbeuzo, zidzakhala zonyansa kwa inu.

39“Munthu akakhudza nyama yofa yokha imene anthu amadya, munthuyo adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.

40Ndipo munthu amene adyako nyamayo, achape zovala zake, komabe adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Nayenso amene anyamula nyama yakufayo, achape zovala zake, komabe adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.

41“Chinthu chilichonse chokwaŵa pansi nchonyansa, ndipo musadye.

42Chinthu chilichonse chokwaŵa ndi kumimba, ndiponso chilichonse cha miyendo inai kapena cha miyendo yambirimbiri, kungoti zonse zokwaŵa pansi, musadye poti nzonyansa kwa inu.

43Musadzisandutse oipitsidwa ndi chokwaŵa chilichonse, musadziipitse nazo, kuti mungasanduke oipitsidwa.

44Lev. 19.2; 1Pet. 1.16 Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Tsono mudziyeretse, ndipo mukhale oyera pakuti Ine ndine woyera. Musadziipitse ndi chinthu chokwaŵa pansi chilichonse.

45Pakuti Ine ndine Chauta, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale oyera, pakuti Ine ndine woyera.”

46Limeneli ndilo lamulo lonena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda m'madzi, ndi chinthu chilichonse chokwaŵa pansi,

47kuti muzisiyanitsa pakati pa zonyansa ndi zosanyansa, ndiponso pakati pa zamoyo zimene mungathe kudya ndi zimene simuyenera kudya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help