1 Maf. 22 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ahabu achita chiwembu mzinda wa Ramoti-Giliyadi.(2 Mbi. 18.2-27)

1Padapita zaka zitatu popanda nkhondo pakati pa Siriya ndi Israele.

2Pa chaka chachitatu Yehosafati mfumu ya ku Yuda adakacheza kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele.

3Tsono Ahabu adafunsa aphungu ake kuti, “Ramoti-Giliyadi ndi mzinda wathu, nanga chifukwa chiyani ife tikukhala chete, osaulanda kwa mfumu ya ku Siriya?”

4Ndipo adafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane limodzi ku nkhondo ku Ramoti-Giliyadi?” Yehosafati adauza mfumu ya ku Israeleyo kuti, “Ine ndili nanu limodzi, anthu anga nganu, akavalo anga nganunso.”

5Yehosafati adauza Ahabu kuti, “Poyamba upemphe nzeru kwa Chauta.”

6Tsono Ahabu adasonkhanitsa aneneri ake okwanira ngati 400, ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi ndipite kukamenyana nkhondo ndi Ramoti-Giliyadi, kaya kapena ndileke?” Aneneriwo adamuuza kuti, “Pitani, pakuti Ambuye aupereka mzindawo kwa inu mfumu.”

7Koma Yehosafati adafunsa kuti, “Kodi pano palibe mneneri wina wa Chauta woti timpempheko nzeru?”

8Ahabu adauza Yehosafati kuti, “Alipo munthu wina amene angapemphe nzeru kwa Chauta, dzina lake ndi Mikaya, mwana wa Imila. Koma ine ndimadana naye ameneyo popeza kuti sandilosera zabwino koma zoipa.” Tsono Yehosafati adati, “Iyai mfumu, msatero.”

9Apo Ahabu adaitana imodzi mwa nduna zake nkuiwuza kuti, “Takaitanani Mikaya, mwana wa Imila, abwere kuno msanga.”

10Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adaakhala pa mipando yao yaufumu, atavala zovala zao zaufumu. Pamenepo panali pa bwalo lopererapo tirigu, pa khomo la pa chipata cha Samariya. Ndipo aneneri onse ankalosa pamaso pa mafumuwo.

11Wina mwa iwo, Zedeki, mwana wa Kenana adaadzisulira nyanga zachitsulo. Iyeyo adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndi nyangazi iwe udzagonjetsa Asiriya mpaka kuŵaonongeratu.’ ”

12Aneneri onsewo adalosa chimodzimodzi, adati, “Pitani ku Ramoti-Giliyadi, ndipo mukapambana. Chauta aupereka mzindawo kwa inu mfumu.”

Mneneri Mikaya alosa motsutsa Ahabu.

13Wamthenga uja amene adaapita kukaitana Mikaya namuuza kuti, “Onani, mau onse amene akunena aneneri, akulosera mfumu zabwino. Ndiye nanunso mau anu akhale ofanafana ndi mau aowo. Muzilosa zabwino.”

14Koma Mikaya adati, “Pali Chauta wamoyo, zimene Chautayo andiwuze, ndizo ndidzalankhule.”

15Tsono atafika kwa Ahabu, mfumuyo idamfunsa kuti, “Kodi Mikaya, ife tipite kukamenya nkhondo ku Ramoti-Giliyadi, kapena tileke?” Iye adayankha kuti, “Pitani, mukapambana. Chauta adzaupereka mzindawo kwa inu amfumu.”

16Koma mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi ndikulumbiritse kangati, kuti undiwuze zoona zokhazokha m'dzina la Chauta?”

17Num. 27.17; Mt. 9.36; Mk. 6.34 Mikaya adati, “Ndidaona Aisraele onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono Chauta adati, ‘Ameneŵa alibe mbuyawo. Aliyense apite kwao mwamtendere.’ ”

18Pamenepo mfumu ya ku Israele idafunsa Yehosafati kuti. “Suja ndidaakuuzani kuti ameneyu sadzandilosera zabwino, koma zoipa zokha?”

19Yob. 1.6; Yes. 6.1 Apo Mikaya adati, “Nchifukwa chake mverani mau a Chauta. Ine ndidapenya Chauta atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse lakumwamba litaima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere.

20Tsono Chauta adati, ‘Kodi ndani amene akanyengerere Ahabu kuti akafe ku Ramoti-Giliyadi?’ Wina ankanena zina, winanso nkumanena zina.

21Apo mzimu wina udadzaima pamaso pa Chauta nunena kuti, ‘Ndikamnyengerera ndine.’

22Tsono Chauta adaufunsa kuti, ‘Ukamnyengerera bwanji?’ Mzimuwo udati, ‘Ndidzapita nkumakanena zabodza kudzera mwa aneneri ake onse.’ Pamenepo Chauta adati, ‘Ukakatero, ukakhozadi. Pita ukamnyengerere.’

23Tsonotu Chauta waika bodza m'kamwa mwa aneneri anu onseŵa, ndiye kuti Iye yemwe waneneratu kuti mukaona tsoka.”

24Tsono Zedeki uja, mwana wa Kenana, adadza pafupi namenya Mikaya pa tsaya, namufunsa kuti, “Kodi mzimu wa Chauta udadzera njira iti kuti uchoke mwa ine, uzikalankhula ndi iwe?”

25Mikaya adayankha kuti, “Udzadziŵa pa tsiku limene uzikaloŵa m'chipinda china ndi china cham'kati kuti ukabisale.”

26Pamenepo Ahabu, mfumu ya ku Israele, adati, “Mgwireni Mikayayu, mupite naye kwa Amoni, mkulu wa mzinda, ndiponso kwa Yowasi, mwana wa mfumu.

27Mukaŵauze mau angaŵa akuti, ‘Munthu uyu muikeni m'ndende ndipo muzimpatsa chakudya pang'ono ndi madzi pang'ono mpaka nditabwerera mwamtendere.’ ”

28Mikaya adati, “Mukabwerera mwamtendere, ndiye kuti Chauta sadalankhule kudzera mwa ine.” Ndipo adaonjeza kuti, “Mumve anthu nonsenu zimene ndanenazi!”

Ahabu aphedwa ku Ramoti-Giliyadi.(2 Mbi. 18.28-34)

29Zitatero, Ahabu mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adapita ku Ramoti-Giliyadi.

30Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Ine ndidzizimbaitsa, ndipo ndipita kunkhondoko, koma iwe uvale malaya ako aufumu.” Choncho mfumu ya ku Israele idadzizimbayitsa onsewo nkupita ku nkhondo.

31Mfumu ya ku Siriya nkuti italamula akapitao a magaleta okwanira 32, kuti asamenye nkhondo ndi wina aliyense, wamng'ono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israele basi.

32Tsono pamene akapitao a magaletawo adaona Yehosafati, adati, “Ndithudi ameneyo ndiye mfumu ya ku Israele.” Choncho adabwerera kudzalimbana naye. Yehosafati adayamba kufuula.

33Apo akapitao a magaleta aja adaona kuti si mfumu ya ku Israele, ndipo adabwerera osamtsatanso.

34Koma Msiriya wina adakoka uta wake mwachiponyeponye, ndipo adalasa mfumu ya ku Israele pa maluma a malaya ake achitsulo. Pamenepo mfumuyo idauza munthu woyendetsa galeta lake kuti, “Tembenuka, ndipo undichotse pankhondo pano poti ndavulazidwa.”

35Nkhondo idakula kwambiri tsiku limenelo, mwakuti mfumu ija adangoisiya ili tsonga m'galeta lake atayang'anana ndi Asiriya, mpaka mfumuyo idafa madzulo. Monsemo nkuti magazi akutayikira pansi pa galetalo.

36Pamene dzuŵa linkaloŵa kudamveka mfuu wa ankhondo kuti, “Aliyense apite ku mzinda wakwao, aliyense apite ku dziko lakwao.”

37Motero mfumu ija idafa, ndipo anthu adapita nayo ku Samariya, nakaiika m'manda kumeneko.

38Anthu aja adatsuka galeta lija ku chidziŵe cha ku Samariya, kumene akazi adama ankasamba. Ndipo agalu adayamba kunyambita magazi a mfumuyo, potsata mau amene Chauta adaalankhula.

39Tsono ntchito zina za Ahabu ndi zonse zimene adazichita, kudzanso za nyumba ya minyanga ya njovu yomwe adaimanga, ndiponso za mizinda yonse imene adaimanga, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.

40Choncho Ahabu adamwalira, kulondola makolo ake naikidwa m'manda. Ahaziya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Yehosafati mfumu ya ku Yuda.(2 Mbi. 20.31—21.1)

41Yehosafati, mwana wa Asa, adayamba kulamulira ku Yuda pa chaka chachinai cha ufumu wa Ahabu, mfumu ya ku Israele.

42Yehosafatiyo anali wa zaka 35 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 25 ku Yerusalemu. Mai wake anali Azuba, mwana wa Sili.

43Yehosafati ankayenda motsata chitsanzo chabwino cha atate ake. Sadapatuke pa zimenezo. Ankachita zolungama pamaso pa Chauta. Komabe akachisi opembedzerako mafano sadaŵawononge, mwakuti anthu ankaperekabe nsembe ndipo ankafukizabe lubani pa malowo.

44Chinanso nchakuti Yehosafati adapangana za mtendere ndi mfumu ya ku Israele.

45Tsono ntchito zina zonse za Yehosafati, mphamvu zimene adaonetsa, ndiponso maponyedwe ake a nkhondo, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.

46Chinanso ndiye kuti Yehosafati adapirikitsa gulu lotsalira la anthu ochitana zadama ku malo achipembedzo, amene anali adakalipo pa nthaŵi ya Asa, bambo wake.

47Masiku amenewo ku Edomu kunalibe mfumu, koma kunali nduna yaikulu chabe yoikidwa ndi mfumu ya ku Yuda.

48Tsono Yehosafati adapanga zombo zazikulu zomapita ku Ofiri kukatenga golide. Koma zombozo sizidayende chifukwa zidaaonongeka ku Eziyoni-Gebere.

49Tsono Ahaziya mwana wa Ahabu, adauza Yehosafati kuti, “Amalinyero anga apite limodzi ndi amalinyero anu pa zombo.” Koma Yehosafati sadavomere zimenezi.

50Pambuyo pake Yehosafati adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Ndipo Yehoramu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Mfumu Ahaziya wa ku Israele.

51Tsono Ahaziya mwana wa Ahabu, adaloŵa ufumu wa Ku Israele ku Samariya pa chaka cha 17 cha ufumu wa Yehosafati, mfumu ya ku Yuda. Ndipo adalamulira anthu a ku Israele zaka ziŵiri.

52Iyeyo ankachita zoipa pamaso pa Chauta, ankatsata mayendedwe oipa a atate ake ndi amai ake. Ankatsatanso zoipa za Yerobowamu, mwana wa Nebati, amene ankachimwitsa kwambiri anthu a ku Israele.

53Ahaziyayo ankatumikira Baala ndi kumampembedza, ndipo potero adaputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, potsata zonse zimene atate ake ankachita.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help