1“Ine Nebukadinezara ndinkangodzikhalira mwamtendere m'nyumba mwanga, ndipo ndinali pabwino.
2Ndili m'tulo ndidalota maloto oopsa. Maganizo anga ndi zimene ndinkaona m'mutu mwangamu nditagona, zidandichititsa mantha kwambiri.
3Motero ndidalamula kuti anzeru onse a ku Babiloni abwere kwa ine kuti adzandiwuze kumasula kwake kwa malotowo.
4Tsono amatsenga, oombeza, alauli, ndi omasula maloto adabwera. Ndidaŵafotokozera maloto anga, koma sadathe kundimasulira.
5Potsiriza kudabwera Daniele, wotchedwa Belitesazara, potsata dzina la mulungu wanga, munthu wodzazidwa ndi nzeru za milungu yoyera. Iyeyo ndidamufotokozeranso malotowo.
6Ndidati, ‘Iwe Belitesazara, mkulu wa anthu amatsenga, ndimadziŵa kuti ndiwe wodzazidwa ndi nzeru za milungu yoyera, ndipo umadziŵa zinsinsi zonse, mvera zimene ndidaona m'maloto anga, ndipo undimasulire.
7Zimene ndidaona m'mutu mwanga ndili m'tulo ndi izi: Ndidaona mtengo wautali utaima pakati pa dziko lapansi.
8Mtengowo unkakulirakulira mwamphamvu. Nsonga yake idakafika mpaka ku mlengalenga, ndipo inkaonekera ku malire onse a dziko lapansi.
9Masamba ake anali okongola, zipatso zake zinali zochuluka, ndipo zinali zokwanira dziko lonse lapansi. Nyama zakuthengo zinkakhala mu mthunzi wake, mbalame zinkakhala m'nthambi zake, ndipo zolengedwa zonse zinkadya za mu mtengo umenewo.
10“ ‘Zina zimene ndidaziwona ndili m'tulo ndi izi: ndidaona wamthenga wina, woyera ndithu, akuchokera kumwamba.
11Adafuula, nati, “Ugwetseni mtengowo, ndipo musadze nthambi zake. Yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake. Nyama zakuthengo zithaŵe pamthunzi pake, ndipo mbalame zithaŵe pa nthambi zake.
12Koma musiye tsinde lake ndi mizu yake m'nthaka. Tsindelo mulimange ndi maunyolo achitsulo ndi amkuŵa, ndi kulisiya kuthengo pakati pa udzu. Anyowe ndi mame munthuyo, ndipo akhale pamodzi ndi nyama nkudya udzu wapanthaka.
13Asakhalenso ndi maganizo a munthu, koma apatsidwe nzeru za nyama zaka zisanu ndi ziŵiri.
14Amithenga oyera ndiwo akutsimikiza zimenezi. Tsono anthu onse adziŵe kuti Mulungu Wopambanazonse ali ndi mphamvu zolamulira maufumu a anthu. Angathe kusankha munthu wina aliyense monga afunira kuti akhale mfumu, ngakhale munthu wotsika kwambiri.”
15“ ‘Maloto amene ine mfumu Nebukadinezara ndidalota ndi ameneŵa. Tsono iwe Belitesazara undimasulire. Ngakhale kuti anthu anzeru onse a mu ufumu wanga alephere, iwe ungathe kundiwuza chifukwa uli ndi nzeru za milungu yoyera.’ ”
Daniele amasula maloto16Daniele amene ankatchedwanso Belitesazara adada nkhaŵa pa kanthaŵi, maganizo ake nkumamuvuta. Koma mfumu idati, “Belitesazara, malotoŵa ndi kumasulira kwake zisakuvute.” Belitesazara adayankha kuti, “Mbuyanga, bwenzi zili bwino, achikhala kuti malotowo akhalire adani anu ndipo kumasula kwake kugwere amene amakuzondani!
17Mudaona mtengo ukukulirakulira mwamphamvu. Nsonga yake idafika ku mlengalenga ndi kuwonekera ku malire onse a dziko lapansi.
18Masamba ake anali okongola, zipatso zake zinali zochuluka, zokwanira dziko lonse lapansi. Nyama zakuthengo zinkakhala mu mthunzi wake, ndipo mbalame zinkakhala m'nthambi zake.
19Inu amfumu, mtengo umenewo ndi inuyo. Mwasanduka wamkulu ndi wamphamvu. Ukulu wanu wachita ngati kufika ku mlengalenga, ufumu wanu wakafika mpaka ku malire onse a dziko lapansi.
20Komanso inu amfumu, mudaona wamthenga woyera akuchokera kumwamba, ndipo adati, ‘Gwetsani mtengowo, ndipo muuwononge. Koma musiye tsinde ndi mizu yake m'nthaka. Tsindelo mulimange ndi maunyolo a chitsulo ndi mkuŵa, ndipo mulisiye kuthengo pakati pa udzu. Anyowe ndi mame munthuyo, ndipo akhale pamodzi ndi nyama nkudya udzu wapanthaka zaka zisanu ndi ziŵiri.’
21“Inu amfumu, kumasula kwake ndi uku: Zimenezi ndizo zimene Mulungu Wopambanazonse watsimikiza kutitu zidzakugwereni.
22Mudzachotsedwa pakati pa anthu. Mudzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo. Muzidzadya udzu ngati ng'ombe, ndipo mudzanyowa ndi mame zaka zisanu ndi ziŵiri. Apo mudzavomereza kuti Mulungu Wopambanazonse amalamula maufumu onse a anthu, ndipo kuti angathe kulonga ufumu munthu aliyense monga afunira.
23Amithenga aja adalamula kuti asiye tsinde ndi mizu yake. Ndiye kuti mudzakhalanso mfumu, mukadzadziŵa kuti Mulungu ndiye amene amalamulira dziko lapansi.
24Nchifukwa chake inu amfumu, tsatani malangizo anga. Lekani machimo anu, muzichita zolungama. Muziŵachitira chifundo anthu osauka, kuti kapena nthaŵi ya mtendere wanu nkutalika.”
25Zonsezi zidachitikira mfumu Nebukadinezara.
26Pakutha pa miyezi khumi ndi iŵiri, iye ankayenda padenga pa nyumba yaufumu ku Babiloni.
27Ndipo adati, “Ati kukula ati mzinda wa Babiloniwu! Ndidaumanga kuti ukhale likulu langa loonetsa mphamvu zanga ndi ulemerero wa ufumu wanga.”
28Akulankhula choncho, adamva mau ochokera kumwamba akuti, “Iwe mfumu Nebukadinezara, imva zimene ndikunena. Ufumu wako wachotsedwa m'manja mwako.
29Adzakupirikitsa pakati pa anthu, udzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo. Udzadya udzu ngati ng'ombe pa zaka zisanu ndi ziŵiri, mpaka utadziŵa kuti Mulungu Wopambanazonse ndiye wolamulira ufumu wa anthu, ndipo amaupatsa aliyense monga momwe afunira.”
30Pa nthaŵi yomweyo zinthuzo zidachitikadi. Nebukadinezara adampirikitsira kutali ndi anthu, namakadya udzu ngati ng'ombe. Thupi lake lidanyowa ndi mame akumwamba, mpaka ndithu tsitsi lake kutalika ngati nthenga za chiwombankhanga, zikhadabo zake ngati za mbalame.
Nebukadinezara atamanda Mulungu31Mfumuyo idati, “Zitatha zaka zimenezo, ine Nebukadinezara ndidayang'ana kumwamba, ndipo nzeru zanga zidabwereramo. Apo ndidatamanda Mulungu Wopambanazonse, ndidayamika ndi kulemekeza Mulungu wamuyaya. Ndidati,
Adzalamula mpaka muyaya,
ufumu wake udzakhalapo pa mibadwo ndi mibadwo.
32Anthu onse a pansi pano sali kanthu pamaso pake.
Palibe ndi mmodzi yemwe woti angamuletse
kuchita zimene afuna,
kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchitanji?’
33“Tsono nzeru zanga zitabweramo, ndidalandiranso ufumu wanga wonse. Nduna zanga ndi akalonga anga adandilandira mokondwa. Adandikhazikitsanso mu ufumu wanga, ndipo mphamvu zanga zidaonjezeka kuposa kale.
34“Ndiye ine Nebukadinezara ndimatamanda, ndimachitira ulemu ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba. Zonse zimene imachita nzabwino, ndipo njira zake zonse nzolungama. Imachepetsa aliyense wodzikuza.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.