Yes. 24 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu adzalanga dziko lapansi

1Zoona, Chauta adzaononga dziko

lapansi ndi kulisandutsa chipululu.

Adzalisakaza, nadzamwaza anthu ake onse.

2Aliyense adzaona zimodzimodzi:

ansembe ndi anthu,

akapolo aamuna ndi ambuyao aamuna,

adzakazi ndi ambuyao aakazi,

ogula ndi ogulitsa,

obwereka ndi oŵabwereka,

ndiponso okongola ndi okongoza.

3Dziko lapansi lidzaonongedwa kwathunthu,

lidzasakazikiratu,

pakuti Chauta wanena zimenezi.

4Dziko likulira ndipo likufota.

Dziko lonse lapansi likuvutika ndipo likuuma.

Mlengalenga ukuvutika pamodzi ndi dziko lapansi.

5Anthu aipitsa dziko lapansi

posatsata malamulo a Mulungu,

ponyoza mau ake,

ndipo pophwanya chipangano chamuyaya

chimene Iye adapangana nawo.

6Nchifukwa chake Mulungu watemberera

dziko lapansi, anthu am'dzikomo

akuzunzika chifukwa cha machimo ao.

Iwo amalizika,

ndipo atsala ndi oŵerengeka okha.

7Mphesa zikuuma,

ndipo vinyo akusoŵa.

Aliyense amene ankasangalala ali ndi chisoni.

8Kulira kokometsera kwa ting'oma tao kwatha,

phokoso la anthu osangalala latha,

zeze wosangalatsa uja wati zii.

9Anthu saimbanso pomwa vinyo,

akamamwa zaukali zimaŵaŵa m'kamwa mwao.

10Mu mzinda wachisokonezo uja zonse zaonongedwa,

nyumba iliyonse yatsekedwa,

kotero kuti palibe wotha kuloŵamo.

11Anthu akufuula m'miseu

chifukwa cha kusoŵa kwa vinyo.

Chimwemwe chonse chatheratu,

palibenso chisangalalo pa dziko lonse lapansi.

12Mzinda wasanduka bwinja,

zipata zake zagumuka.

13Zimenezi ndizo zimene zidzachitikire

mtundu uli wonse wa pa dziko lapansi.

Kudzakhala ngati khunkha la olivi

ndi khunkha la mphesa,

pamene kholola latha.

14Koma otsala aja adzafuula ndi kuimba mokondwa.

Akuzambwe adzatamanda ukulu wa Chauta.

15Nchifukwa chake inu akuvuma,

tamandani Chauta.

Anthu okhala m'mphepete mwa nyanja,

yamikani Ambuye, Mulungu wa Israele.

16Kuchokera ku maiko akutali

tilikumva nyimbo zotamanda,

zoyamika Wolungama uja.

Koma ine ndikuti:

Ndatheratu, ndatheratu!

Tsoka kwa ine!

Onyenga akupitirizabe

ndipo kunyenga kwao kukupitabe m'tsogolo.

17Inu anthu a dziko lapansi,

zoopsa, mbuna ndi misampha zikukudikirani.

18Aliyense wothaŵa phokoso la zoopsazo adzagwa m'mbuna,

ndipo wotuluka m'mbunamo adzakodwa mumsampha.

Kudzagwa mvula yachigumula

ndipo maziko onse a dziko adzagwedezeka.

19Dziko lapansi lidzathyokathyoka,

lidzang'ambika kwathunthu ndi kugwedezeka kwamphamvu.

20Dziko lapansi lidzadzandira ngati munthu woledzera,

lidzagwedezeka ngati chisimba nthaŵi ya mkuntho.

Dziko lapansi lalemedwa ndi zoipa zake,

lidzagwa ndipo silidzaukanso.

21Tsiku limenelo Chauta adzalanga

kumwamba zamphamvu zakumwamba,

ndipo pansi pano mafumu a pansi pano.

22Mulungu adzasonkhanitsa mafumu onse pamodzi,

ngati am'ndende amene ali m'dzenje.

Adzaŵatsekera m'ndende,

ndipo patapita nthaŵi yaitali, adzalangidwa.

23Mwezi udzanyala,

ndipo dzuŵa lidzachita manyazi,

pakuti Chauta Wamphamvuzonse adzakhala mfumu.

Adzalamulira pa phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu,

ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help