1 Maf. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nduna zazikulu za Solomoni

1Mfumu Solomoni ankalamulira dziko lonse la Israele,

2ndipo nduna zake zikuluzikulu zinali izi: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe.

3Elihorefe ndi Ahiya ana a Sisa, anali alembi. Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri.

4Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wankhondo. Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe.

5Azariya mwana wa Natani ankayang'anira nduna zam'zigawo. Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi mlangizi wapadera wa mfumu.

6Ahisara anali mkulu woyang'anira nyumba ya mfumu. Ndipo Adoniramu, mwana wa Abida, anali mkulu woyang'anira ntchito zathangata.

7Solomoni anali ndi nduna khumi ndi ziŵiri zimene adaziika m'zigawo zonse za dziko la Israele. Nduna zimenezi zinkapereka chakudya kwa mfumu ndi banja lake lonse. Nduna iliyonse inkapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka.

8Maina ndi aŵa: Benihuri, ku dziko lamapiri la Efuremu.

9Benedekere ku mizinda iyi: Makazi, Salabimu, Betesemesi, Etoni ndi Betehanani.

10Benihesedi ankayang'anira ku mzinda wa Aruboti. Ankayang'aniranso Soko ndi dziko lonse la Hefere.

11Benabidanabu ankayang'anira dziko lonse la mapiri la Dori. Iyeyo anali atakwatira Tafati mwana wa Solomoni.

12Baana mwana wa Ahiludi ankayang'anira ku Tanaki, Megido ndi ku Beteseani konse, pafupi ndi Zaretani kunsi kwake kwa Yezireele, ndiponso kuyambira ku Beteseani mpaka ku Abele-Mehola kukafika mpaka ku Yokomeamu.

13Benigebere ankayang'anira ku Ramoti-Giliyadi ndi midzi ya Yairo mwana wa Manase, imene ili ku Giliyadi. Analinso ndi chigawo cha Aigobu, chimene chili ku Basani, mizinda yaikulu 60 yokhala ndi malinga ndiponso zitseko zamkuŵa.

14Abinadabu mwana wa Ido ankayang'anira ku Mahanaimu.

15Ahimaazi ankayang'anira ku Nafutali. Iyeyu adaakwatira Basemati mwana wa Solomoni.

16Baana, mwana wa Husai ankayang'anira ku Asere ndi ku Bealoti.

17Yehosafati, mwana wa Paruwa, ankayang'anira ku Isakara.

18Simei mwana wa Ela ankayang'anira ku Benjamini.

19Gebere, mwana wa Uri, ankayang'anira ku dziko la Giliyadi kuphatikizapo dziko limene lidaali la Sihoni mfumu ya Aamori, ndiponso la Ogi mfumu ya ku Basani. Panalinso nduna yaikulu imodzi yoyang'anira dziko lonse la Yuda.

Ulamuliro wa Solomoni uyenda bwino

20Ayuda ndi Aisraele anali ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Anali okondwa chifukwa anali ndi zakudya ndi zakumwa zambiri.

21Gen. 15.18; 2Mbi. 9.26Solomoni ankalamulira maiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a Ejipito. Maikowo ankakhoma msonkho ndi kumatumikira Solomoni pa masiku onse a moyo wake.

22Chakudya chofunika ku nyumba ya mfumu pa tsiku limodzi chinkakwanira madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgaiwa,

23ng'ombe khumi zonenepa zodyetsera m'khola, ng'ombe zakubusa makumi aŵiri, nkhosa 100, osaŵerengera ngondo, nswala, mphoyo ndiponso mbalame zonona zoŵeta.

24Solomoni ankalamulira dziko lonse la kuzambwe kwa mtsinje wa Yufurate, kuyambira ku Tifisa mpaka ku Gaza. Mafumu onse akumeneko adamgonjera, choncho Solomoni anali pamtendere ndi maiko ozungulira.

25Choncho nthaŵi yonse Solomoni ali moyo anthu a ku Yuda ndi a ku Israele anali paufulu, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pamtendere, osasoŵa kanthu kalikonse.

261Maf. 10.26; 2Mbi. 1.14; 9.25 Ndipo Solomoni anali ndi zipinda 40,000 zosungiramo akavalo okoka magareta ake, analinso ndi anthu 12,000 okwera pa akavalo.

27Tsono nduna khumi ndi ziŵiri zija zinkapereka chakudya cha mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadzadya nao kunyumba kwa mfumu, nduna iliyonse mwezi wake. Ndunazo sizinkalola kuti kanthu kalikonse kasoŵe.

28Barele nayenso ndi udzu wodyetsa akavalo okoka magareta ndiponso akavalo enanso, zonsezo ankabwera nazo kumalo kumene zinkafunika, nduna iliyonse monga m'mene ankaiwuzira.

29Mulungu adapatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka, nzeru zake zinali zopanda malire.

30Motero nzeru za Solomoni zidapambaniratu nzeru za anthu onse akuvuma, ndiponso za anthu onse a ku Ejipito.

31Mas. 89Iyeyo anali wanzeru kuposa anthu ena onse, kuposa ngakhale Etani wa ku Ezara, kuposanso Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake idamveka kwa anthu a mitundu yonse yozungulira dziko lake.

32Miy. 1.1; 10.1; 25.1; Nyi. 1.1 Solomoniyo adapeka miyambi 3,000, ndiponso nyimbo zokwanira 1,005.

33Ankaphunzitsa za mitengo, kuyambira mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kachitsamba ka hisope komera pa khoma. Ankaphunzitsanso za nyama, mbalame, zinthu zokwawa pansi ndiponso za nsomba.

34Motero anthu ankabwera kwa Solomoni kuchokera ku maiko onse, kuti adzamve nzeru zake. Ankatumizidwa ndi mafumu onse a pa dziko lapansi amene anali atamva mbiri ya nzeru zake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help