1Tsono Chauta adalamula Mose kuti,
2“Uza Aisraele abwerere, amange zithando patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, moyang'anana ndi Baala-Zefoni. Mumange zithando pamenepo m'mbali mwa nyanja.
3Apo Farao adzaganiza kuti, ‘Aisraele asokonezeka, akungoyendayenda m'dzikomo, azingidwa ndi chipululu.’
4Ndidzamuumitsa mtima Farao, ndipo adzalondola Aisraelewo. Tsono ndikadzagonjetsa Farao pamodzi ndi gulu lonse lankhondo, ndidzalandira ulemu, ndipo Aejipito onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Choncho Aisraele adachita zonse monga momwe adaŵauzira.
5Atamva kuti anthu athaŵa, Farao, mfumu ya ku Ejipito, pamodzi ndi nduna zake zonse, adasintha maganizo pa za Aisraelewo. Adati, “Kodi ife tachitapo chiyani pamenepa? Talola Aisraele kuti athaŵe ndi kuleka kutitumikira.”
6Pamenepo Farao adakonzetsa galeta lake lankhondo, ndipo adauza asilikali ake kuti apite naye limodzi.
7Adatenga magaleta amphamvu 600 pamodzi ndi magaleta ena onse ndipo adaika atsogoleri pa magaleta onsewo.
8Chauta adaumitsa mtima Farao mfumu ya ku Ejipito, ndipo iye adalondola Aisraele, pamene Aisraele ankachoka monyada.
9Aejipitowo, ndiye kuti akavalo ndi magaleta a Farao, oyendetsa magaletawo, okwera pa akavalo ndi gulu lankhondo la Farao, adalondola Aisraele aja nakaŵapeza pamalo pomwe adaamanga zithando paja, pafupi ndi Pihahiroti, moyang'anana ndi Baala-Zefoni.
10Tsono Farao atayandikira, Aisraele aja adaona Aejipito akuŵalondola, ndipo adachita mantha kwambiri, nayamba kulira mofuula kwa Chauta.
11Adafunsa Mose kuti, “Kodi nchifukwa chakuti ku Ejipito kunalibe malo a manda, kuti inuyo mutifikitse kuchipululu kuno kuti tidzafe? Mwatichita chiyani potitulutsa ku Ejipito?
12Kodi ife tisanachoke ku Ejipito, sitidakuuzirenitu zimenezi? Ife tidaanena kuti, ‘Mutileke, tikhalebe akapolo a Aejipito.’ Zidakatikomera ife kukhalabe akapolo kupambana kuti tifere kuchipululu kuno.”
13Apo Mose adayankha anthuwo kuti, “Musaope! Limbikani, ndipo muzingopenya zimene Chauta achite lero lino pofuna kukupulumutsani. Aejipito amene mukuŵaona lerowo, simudzaŵaonanso.
14Chauta ndiye amene akumenyereni nkhondo. Inuyo simuchitapo kanthu konse.”
15Apo Chauta adafunsa Mose kuti, “Chifukwa chiyani ukulira kwa ine? Auze Aisraele kuti aziyenda.
16Tenga ndodo yakoyo, ndipo utambalitse dzanja pa nyanja, kuigaŵa nyanjayo kuti Aisraele aoloke pouma.
17Ndidzaŵaumitsa mtima Aejipitowo, kotero kuti adzalondola Aisraele ndithu. Ndipo kugonjetsa kumene ndidzagonjetsa Farao pamodzi ndi ankhondo ake, magaleta ake ndi oyendetsa ake omwe, ndidzapeza nako ulemerero.
18Aejipitowo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, akadzaona m'mene ndipambanire Farao ndi magaleta ake ndi oŵayendetsa ake.”
19Apo mngelo wa Mulungu, yemwe ankatsogolera Aisraele aja, adakakhala cha kumbuyo kwao. Mtambo womwe unkakhala patsogolo pao uja, udakakhalanso chakumbuyo kwao.
20Unali pakati pa gulu lankhondo la Aejipito ndi gulu lankhondo la Aisraele. Choncho panali mtambo ndi mdima, kotero kuti magulu ankhondo aŵiriwo sadayandikane usiku wonse.
21Tsono Mose adatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo pompo Chauta adaumitsa nyanja ija, pogwiritsa ntchito mphepo yamkuntho yakuvuma, imene idaomba usiku wonse ndi kuumitsa nyanjayo. Madziwo adagaŵikana,
221Ako. 10.1, 2; Ahe. 11.29 ndipo adakhala ngati chipupa pa mbali zonse ziŵiri, motero Aisraele adaoloka pouma.
23Aejipito aja adalondola Aisraelewo mpaka kukaloŵa nawo m'nyanja muja. Akavalo onse a Farao adaloŵa m'nyanja, pamodzi ndi magaleta ake ndi oŵayendetsa ake omwe.
24Tsono kusanache m'maŵa ndithu, Chauta, ali m'chipilala chamtambo ndi chamoto, adayang'ana ankhondo a Aejipito ndipo adaŵachititsa mantha.
25Adapinda mikombero ya magaleta ao, kotero kuti magaletawo ankayenda movutika. Pamenepo Aejipito aja adati, “Tiyeni tiŵathaŵe Aisraeleŵa, chifukwa Chauta akuŵamenyera nkhondo, kulimbana nafe.”
26Apo Chauta adauza Mose kuti, “Tambalitsa dzanja lako kunyanjako kuti madziwo abwerere, ndi kumiza Aejipitowo pamodzi ndi magaleta ao ndi oŵayendetsa ake omwe.”
27Motero Mose adatambalitsa dzanja lake ku nyanja, ndipo m'mene kunkacha, nkuti madziwo akubwerera m'malo mwake. Aejipitowo adayesa kuthaŵa, koma Chauta adaŵabweza momwe m'nyanjamo.
28Ndipo madziwo adabwerera, namiza magaleta aja ndi oŵayendetsawo, pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Farao lija linkaŵatsatali. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adapulumuka.
29Koma Aisraele onse aja adaoloka nyanjayo pansi pali pouma, madzi atangoima pa mbali zonse ziŵiri.
30Pa tsiku limenelo, Chauta adapulumutsa Aisraele kwa Aejipito. Aisraele adaona Aejipitowo ali ngundangunda m'mbali mwa nyanja.
31Choncho adaona mphamvu zazikulu zimene Chauta adaonetsa pogonjetsa Aejipito aja. Tsono adayamba kuwopa Chauta, ndipo ankakhulupirira Chautayo ndi Mose mtumiki wake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.