1Kunali nkhondo nthaŵi yaitali pakati pa anthu a Saulo ndi anthu a Davide. Davide mphamvu zake zinkakulirakulira pamene anthu a Saulo ankafookerafookera.
Ana a Davide obadwira ku Hebroni.2Davide adabereka ana aamuna ku Hebroni. Mwana wake woyamba anali Aminoni, wobadwa kwa Ahinowamu wa ku Yezireele.
3Wachiŵiri anali Kiliyabu, wobadwa kwa Abigaile, mkazi wamasiye wa Nabala, wa ku Karimele. Wachitatu anali Abisalomu, wobadwa kwa Maaka, mwana wa Talimai, mfumu ya ku Gesuri.
4Wachinai anali Adoniya, wobadwa kwa Hagiti. Wachisanu anali Sefatiya wobadwa kwa Abitala.
5Ndipo mwana wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, wobadwa kwa Egila. Ameneŵa ndiwo ana a Davide amene adabadwira ku Hebroni.
Abinere agwirizana ndi Davide.6Pamene kunali nkhondo pakati pa anthu a Saulo ndi anthu a Davide, Abinere adayamba kudzipatsa mphamvu pa anthu a Saulo.
7Saulo anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa, mwana wa Aya. Tsono Isiboseti adafunsa Abinere kuti, “Chifukwa chiyani wakaloŵa kwa mzikazi wa bambo wanga?”
8Abinere adapsa nawo mtima kwambiri mau a Isiboseti, ndipo adati, “Kodi ukundiyesa ine galu wa Ayuda, adani athu? Kuyambira poyamba pomwe ndakhala wokhulupirika kwa Saulo bambo wako, abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindidakupereke m'manja mwa Davide. Ndiye lero, iwe ukundiimba mlandu woti ndachimwa ndi mkazi!
91Sam. 15.28Nchifukwa chake Mulungu andilange, ngakhale kundipha kumene, ngati sindimchitira Davide zimene Chauta adamlonjeza.
10Ndidzachotsa ufumu pa banja la Saulo ndi kuupereka kwa Davide, kuti alamulire Israele ndi Yuda kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba.”
11Pamenepo Isiboseti adangoti kukamwa yasa, osatha kumuyankha Abinere mau ndi amodzi omwe, chifukwa ankamuwopa kwambiri.
12Tsono Abinere adatuma amithenga kwa Davide ku Hebroni kukamufunsa kuti, “Kodi dzikoli nlayani? Tipangane, ine ndidzakuthandizani kuti dziko la Israele likhale lanu.”
13Apo Davide adati, “Chabwino, tipangana. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: sudzandiwona ukapanda kubwera ndi Mikala, mwana wamkazi wa Saulo.”
141Sam. 18.27 Tsono Davide adatuma amithenga kwa Isiboseti, mwana wa Saulo, kukanena kuti, “Undipatse mkazi wanga, Mikala, amene ndidamukwatira polipira timakungu 100 ta nsonga za mavalo a Afilisti.”
15Pamenepo Isiboseti adatuma anthu kuti akamtenge Mikalayo kwa mwamuna wake Palatiele, mwana wa Laisi.
16Koma mwamuna wakeyo adamtsatira mkaziyo. Mwamunayo ankapita nalira njira yonse mpaka ku Bahurimu. Abinere adamuuza kuti, “Iwe, bwerera.” Iye uja nkubwereradi.
17Pambuyo pake Abinere pokambirana ndi atsogoleri a Aisraele, adaŵauza kuti, “Nthaŵi yapitayi mwakhala mukufuna Davide kuti akhale mfumu yanu yokulamulani.
18Ndiye zimenezi muchitedi. Paja Chauta adalonjeza Davide kuti, ‘Ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele kwa Afilisti kudzera mwa iwe mtumiki wanga, ndipo ndidzaŵapulumutsa kwa adani ao onse.’ ”
19Abinere adalankhulanso ndi anthu a fuko la Benjamini. Kenaka adakauzanso Davide ku Hebroni zonse zimene Abenjamini ndi Aisraele adavomerezana kuti achite.
20Pambuyo pake Abinere adabwera ndi anthu makumi aŵiri kwa Davide ku Hebroni. Davideyo adakonzera madyerero Abinere ndi anthu makumi aŵiri amene anali nawowo.
21Tsono Abinere adauza Davide kuti, “Loleni ndikasonkhanitse Aisraele onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuyanga mfumu, kuti adzachite nanu chipangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Choncho Davide adamlola Abinere kuti apite. Ndipo iye adapita mwamtendere.
Kuphedwa kwa Abinere.22Nthaŵi yomweyo ankhondo a Davide adafika ndi Yowabu kuchokera kumene adaakamenya nkhondo, atatenga zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ndi Davide ku Hebroni, popeza kuti anali atamlola kuti apite, ndipo iye anali atapitadi mwamtendere.
23Pamene Yowabu ndi ankhondo onse amene anali nawo adabwera, ena adauza Yowabuyo kuti, “Abinere mwana wa Nere adaabwera kwa amfumu, ndipo amfumuwo adamlola kuti apite, mwakuti wapitadi mwamtendere.”
24Atamva zimenezo Yowabu adapita kwa mfumu nakafunsa kuti, “Inu amfumu, kodi akuti mwachita zotani? Abinere wobwera bwinobwino kuno, nanga bwanjinso inu mwamlola kuti apite? Moti wapitadi?
25Inu amfumu, monga Abinere, mwana wa Nere, simumdziŵa? Amene ujatu adaabwera kudzangokumyatani m'maso. Adaafuna kudzangokutambwani, kuti adziŵe zonse zimene mukuchita.”
26Yowabu atachokako kwa Davide kuja, adatuma amithenga kuti amlondole Abinere. Iwowo adakampezadi ku chitsime cha Sira, nambweza, Davide osadziŵa kanthu.
27Pamene Abinere ankabwerera ku Hebroni, Yowabu adamtengera pambali, pafupi ndi chipata, nakhala ngati afuna kulankhula naye poduka mphepo. Pomwepo Yowabu adabaya Abinere m'mimba, nkuferatu. Yowabu adachita zimenezi chifukwa choti Abinere anali atamuphera mbale wake Asahele.
28Pambuyo pake Davide atamva, adati, “Ine pamodzi ndi anthu a mu ufumu wanga tilibe ndi mlandu womwe pamaso pa Chauta pa imfa ya Abinere, mwana wa Nere.
29Mlandu umenewu ugwere Yowabu ndi onse a pa banja la bambo wake. Ndipo Mulungu amlange Yowabuyu kuti pabanja pake pasadzakhale popanda munthu wa nthenda ya chidzonono, kapena wakhate, kapena wolumala, kapena wophedwa ku nkhondo kapenanso wosoŵa chakudya.”
30Choncho Yowabu ndi mbale wake Abisai adapha Abinere chifukwa choti Abinereyo anali ataŵaphera mbale wao Asahele pa nkhondo ya ku Gibiyoni.
31Tsono Davide adauza Yowabu ndi anthu onse amene anali naye kuti, “Ng'ambani zovala zanu, muvale ziguduli, kuti mulire maliro a Abinere.” Ndipo mfumu Davide mwiniwake ankatsatira onyamula mtembowo.
32Adakamuika Abinere ku Hebroni. Ndiye mfumu idalira mokweza mau ku manda a Abinere. Nawonso anthu onse adalira kwambiri.
33Polira maliro a Abinere mfumu Davide ankati,
“Abinere nkufa motere,
monga m'mene chimafera chitsiru?
34Manja ako anali osamanga,
mapazi ako anali osakulunga.
Komabe wafa monga m'mene amafera munthu
m'manja mwa anthu oipa mtima.”
Anthu onse adaliranso, kumlira Abinere.
35Kenaka anthuwo adadza kudzapempha mfumu kuti adye chakudya kudakali koyera. Koma Davide adalumbira kuti, “Mulungu andilange kwabasi, ngati ndidya chakudya kapena kanthu kena kalikonse dzuŵa lisanaloŵe.”
36Anthu onse adamvera zimenezo, ndipo zidaŵakomera. Zonse zimene ankachita mfumu zinkaŵakondwetsa anthu onse.
37Choncho onse amene ankakhala ndi mfumu pamodzi ndi Aisraele onse adamvetsa tsiku limenelo kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abinere mwana wa Nere aphedwe.
38Ndipo mfumu Davide adafunsa ankhondo ake kuti, “Kodi simukudziŵa kuti lero m'dziko la Israele mwagwa kalonga amene ali munthu wamkulu?
39Tsono ine lero ndafooka kwambiri, ngakhale kuti ndine mfumu yodzozedwa. Ndithu anthu ameneŵa, ana aamuna a Zeruya, akundivutitsa kwambiri. Chauta abwezere munthu wochita zoipa molingana ndi kuipa kwake.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.