1 Yes. 15.1—16.14; 25.10-12; Yer. 48.1-47; Ezek. 25.8-11; Zef. 2.8-11 Zimene akunena Chauta ndi izi:
“Chifukwa Amowabu akunka nachimwirachimwira,
sindileka kuŵalanga.
Iwo adanyoza mafupa a mfumu ya ku Edomu
poŵatentha mpaka kuŵasandutsa phulusa.
2Nchifukwa chake Ineyo ndidzaponya moto ku Mowabu,
ndipo motowo udzapsereza malinga a ku Keriyoti.
Anthu a ku Mowabu adzafera pakati pa phokoso la nkhondo,
asilikali akufuula ndi kuliza malipenga.
3Ndidzaŵaphera wolamulira wao,
Ndidzaphanso nduna zake pamodzi naye.”
Akuterotu Chauta.
Chilango cha anthu a ku Yuda4Zimene akunena Chauta ndi izi:
“Chifukwa anthu a ku Yuda
akunka nachimwirachimwira,
sindileka kuŵalanga.
Iwo anyoza malamulo a Ine Chauta,
ndipo sadatsate malangizo anga.
Milungu yabodza imene makolo ao
ankaipembedza yaŵasokeretsa.
5Nchifukwa chake Ineyo ndidzaponya moto ku Yuda,
ndipo motowo udzapsereza malinga a Yerusalemu.”
Chilango cha anthu a ku Israele6Zimene akunena Chauta ndi izi:
“Chifukwa anthu a ku Israele
akunka nachimwirachimwira,
sindileka kuŵalanga.
Iwo amagulitsa anthu achilungamo ndi siliva,
amagulitsa anthu osauka ndi nsapato.
7Anthu osauka iwo amaŵadyera masuku pa mutu,
anthu ozunzika iwo safuna kuŵayang'ana.
Bambo ndi mwana amakagona ndi mdzakazi mmodzimmodzi,
mwakuti amanyoza dzina langa loyera.
8Anthuwo amagona pambali pa malo aliwonse opembedzerapo,
pa zovala zimene adalandira kwa osauka ngati chikole.
M'nyumba ya Mulungu amamweramo zakumwa
za anthu amene adaŵalipitsa pa mlandu.
9 Deut. 3.8-11 “Komabe ndine amene ndidaononga Aamori
pamene Aisraele ankafika,
ngakhale iwo aja anali ataliatali ngati mikungudza,
ngakhale anali amphamvu ngati mitengo ya thundu.
Ndidaŵaonongeratu zipatso zao m'mwamba
ndiponso mizu yao pansi.
10Inu Aisraele,
ndine ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito.
Ndine ndidakutsogolerani m'chipululu zaka makumi anai,
kuti mukalande dziko la Aamori lija.
11 Num. 6.1-8 Ndipo ndine ndidasankha ena mwa ana anu
kuti akhale aneneri,
nkusankha ena mwa anyamata anu
kuti akhale Anaziri.
Kodi si choncho, inu anthu a ku Israele?”
Akuterotu Chauta.
12“Koma Inu mudaŵamwetsa vinyo Anaziri aja,
ndipo mudaŵalamula aneneriwo kuti, ‘Musalose.’
13“Mverani, ndidzakukanikizani pansi kwanuko,
ndipo mudzalira ngati ngolo
yodzaza ndi katundu wopitirira muyeso.
14Waliŵiro sadzatha kuthaŵa,
wanyonga sadzakhalanso ndi mphamvu.
Wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.
15Munthu wamauta sadzalimbika.
Wothamanga sadzapulumuka,
ndipo wokwera pa kavalo sadzapulumutsa moyo wake.
16Pa tsiku limenelo ngakhale wolimba mtima
pakati pa anthu a mphamvu,
adzathaŵa ali maliseche.”
Akuterotu Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.