1Ana a Isakara naŵa: Tola, Puwa, Yasubu, ndi Simironi, anai.
2Ana a Tola naŵa: Uzi, Refaya, Yeriyele, Yamai, Ibisamu, ndi Semuele, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ndiye kuti a banja la Tola. Onsewo anali ankhondo amphamvu pa mibadwo yao. Chiŵerengero chao pa nthaŵi ya Davide chinali 22,600.
3Mwana wa Uzi anali Iziraya. Ana a Iziraya naŵa: Mikaele, Obadiya, Yowele ndiponso Isiya. Asanu onsewo anali atsogoleri.
4Pamodzi ndi iwowo, malinga ndi mibadwo yao ndi mabanja a makolo ao, panali anthu ankhondo 36,000, pakuti anali ndi akazi ambiri ndiponso ana ambiri.
5Abale ao a mabanja onse a Isakara analipo onse pamodzi 87,000, ankhondo amphamvu, olembedwa potsata mibadwo yao.
Zidzukulu za Benjamini ndi za Dani6Ana a Benjamini naŵa: Bela, Bekere ndiponso Yediyaele, atatu pamodzi.
7Ana a Bela naŵa: Eziboni, Uzi, Uziyele, Yerimoti ndi Iri, asanu, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ankhondo amphamvu. Ndipo chiŵerengero chao potsata mibadwo yao chinali 22,034.
8Ana a Bekere naŵa: Zimira, Yowasi, Eliyezere, Eliyoenai, Omuri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onseŵa anali ana a Bekere.
9Ndipo kulembedwa kwao potsata kubadwa kwao ndiponso malinga ndi mibadwo yao, pokhala atsogoleri a mabanja a makolo ao, analipo 20,200, ankhondo amphamvu okhaokha.
10Mwana wa Yediyaele anali Bilihani. Ana a Bilihani naŵa: Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenana, Zetani, Tarisisi ndi Ahisahara.
11Onseŵa anali ana a Yediyaele, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ankhondo amphamvu 17,200, anthu okonzekera kumenya nkhondo.
12Supimu ndi Hupimu anali ana a Iri, ndipo analinso a fuko ili.
Husimu anali mwana wa Dan.
Zidzukulu za Nafutali13Ana a Nafutali naŵa: Yaziyele, Guni, Yezere ndi Salumu. Anali adzukulu a Biliha.
Zidzukulu za Manase14Ana a Manase naŵa: Asiriele amene adamuberekera mzikazi wake wa ku Aramu. Mkazi yemweyo adabalanso Makiri, bambo wake wa Giliyadi.
15Makiri adapezera Hupimu ndi Supimu akazi, wina wake wina wake. Mlongo wake anali Maaka. Dzina la wachiŵiriyo linali Zelofehadi. Ndipo Zelofehadiyo anali ndi ana aakazi okhaokha.
16Tsono Maaka, mkazi wa Makiri, adabala mwana wamwamuna, namutcha dzina loti Peresi. Mbale wake anali Seresi, ndipo ana ake aamuna anali Ulamu ndi Rakemu.
17Mwana wa Ulamu anali Bedani. Ameneŵa anali ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase.
18Mlongo wake Hamoleketi adabala Isihodi, Abiyezere ndi Mala.
19Ana a Semida naŵa: Ahiyani, Sekemu, Liki ndi Aniyamu.
Zidzukulu za Efuremu20Zidzukulu za Efuremu nazi: Sutela, Beredi, Tahati, Eleada, Tahati,
21Zabadi, Sutela. Efuremu anali nawonso ana aŵiri: Ezere ndi Eleadi amene adaphedwa ndi anthu a ku Gati eni ake a dzikolo, chifukwa chakuti adabwera kudzalanda ng'ombe zao.
22Ndiye Efuremu bambo wao adalira maliro masiku ambiri, choncho abale ake adadza kudzamtonthoza.
23Pambuyo pake Efuremu adakaloŵa kwa mkazi wake, ndipo mkaziyo adatenga pathupi nabala mwana. Mwanayo adamutcha dzina loti Beriya, chifukwa chakuti tsoka lidaagwera banja lake.
24Mwana wake wamkazi anali Seera, amene adamanga mzinda wa Betehoroni wakunsi ndi Betehoroni wakumtunda, kudzanso Uzeniseera.
25Mwana wina wa Efuremu anali Refa, amene zidzukulu zake zinali izi: Resefi, Tela, Tahani,
26Ladani, Amihudi, Elisama,
27Nuni ndi Yoswa.
28Maiko ao kumene ankakhala anali Betele pamodzi ndi midzi yake. Chakuvuma kunali Naarani, chakuzambwe kunali Gezere pamodzi ndi midzi yake, Sekemu pamodzi ndi midzi yake, ndiponso Aya pamodzi ndi midzi yake.
29Zidzukulu za Manase zinkalamulira mizinda iyi: Beteseani pamodzi ndi midzi yake, Tanaki pamodzi ndi midzi yake, Megido pamodzi ndi midzi yake, Dori pamodzi ndi midzi yake. Kumeneko ndiko kumene kunkakhala ana a Yosefe mwana wa Israele.
Zidzukulu za Asere30Ana a Asere naŵa: Imina, Isiva, Isivi, Beriya ndiponso mlongo wao Sera.
31Ana a Beriya naŵa: Hebere ndi Malakiyele, amene adamanga Birizaiti.
32Hebere adabereka Yafileti, Somere, Hotamu ndiponso mlongo wao Suwa.
33Ana a Yafileti naŵa: Pasaki, Bimala ndi Asivati. Ameneŵa ndiwo ana a Yafileti.
34Ana a Somere mbale wake naŵa: Roga, Yehuba ndiponso Aramu.
35Ana a Helemu mbale wake naŵa: Zofa, Imina, Selesi ndi Amala.
36Ana a Zofa naŵa: Suwa, Harenefere, Suwala, Beri, Imira,
37Bezere, Hodi, Sama, Silisa, Itirani ndi Beera.
38Ana a Yetere naŵa: Yefune, Pisipa ndi Ara.
39Ana a Ula naŵa: Ara, Haniyele ndi Riziya.
40Anthu onseŵa anali zidzukulu za Asere. Anali atsogoleri a mabanja a makolo ao, anthu omveka, ankhondo amphamvu, akuluakulu pakati pa akalonga. Chiŵerengero chao cholembedwa m'buku, potsata mibadwo yao yoyenera ntchito yankhondo, chinali 26,000.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.