1Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi,
ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga.
2Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Mulungu,
Mulungu wamoyo.
Kodi ndidzafika liti pamaso pa Mulungu?
3Ntchito yanga ndi kulira usana ndi usiku,
osalaŵa chakudya chilichonse.
Ndipo anthu akhala akunena kuti,
“Mulungu wako ali kuti?”
4Mtima wanga umaŵawa ndikamakumbukira
m'mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu,
poŵatsogolera ku Nyumba ya Mulungu.
Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala,
akuimba nyimbo zothokoza
ndipo akuchita chikondwerero.
5Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga?
Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso,
Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
6Ndatayiratu mtima,
nchifukwa chake ndikukumbukira Inu Mulungu,
pamene ndili ku dziko la Yordani,
ku Heremoni ndi ku phiri la Mizara.
7Madzi akuya akuitanizana ndi madzi akuyanso,
mathithi anu akulindima kochititsa mantha.
Mafunde anu ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe andimiza.
8Komabe Chauta amaonetsa chikondi chake chosasinthika
tsiku ndi tsiku,
Nchifukwa chake nthaŵi zonse ndimamuimbira nyimbo,
ndi kumpemphera Mulungu wondipatsa moyo.
9Ndimafunsa Mulungu, thanthwe langa, kuti,
“Mwandiiŵaliranji?
Ndiziyenderanji ndilikulira
chifukwa chondipsinja mdani wanga?”
10Kunyoza kwa adani anga kumandipweteka
ngati bala lofa nalo la m'thupi mwanga,
akamandifunsa nthaŵi zonse kuti,
“Mulungu wako ali kuti?”
11Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga?
Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso,
Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.